Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Paulendo wobwereza mukapeza anthu achidwi, aikeni pa mndandanda wa anthu amene mumakawapatsa magazini. November: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati palibe mabuku ameneŵa, mungagaŵire mabuku aŵa, Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kapena Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. January: Buku lililonse la masamba 192 limene mpingo uli nalo, lofalitsidwa chaka cha 1987 chisanafike.
◼ “Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2002” ili mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno ndipo isungeni kuti mudzaigwiritse ntchito chaka chonse cha 2002.
◼ Mipingo iyambe kuitanitsa Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2002 pamodzi ndi oda yawo yamabuku ya October. Timabukuti tidzakhalako m’zinenero izi: Chicheŵa, Chifalansa ndi Chingelezi. Timabukuti tizidzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera katundu wa mipingo, kufikira tikabwera ndi kutumizidwa. Timabuku ta Kusanthula Malemba ndi zinthu za oda yapadera, kutanthauza kuti mpingo ndiwo woyenera kuitanitsa timabuku timeneti ngati pali anthu amene akutifuna; mtumiki wa mabuku asaodere mpingo mulu wa timabuku timeneti. Choncho afunika kusunga mosamala mayina a anthu onse omwe aitanitsa timabukuti.—Onani Malangizo a Watch Tower Ofunsira Mabuku, Gawo 3.
◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:
Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha—M’zilembo Zazikulu (kllp-E)—Chingelezi
◼ Makaseti Avidiyo Amene Alipo:
Faithful Under Trials—Jehovah’s Witnesses in the Soviet Union (vcut-E)—Chingelezi