Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/01 tsamba 3-6
  • Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2002

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2002
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Timitu
  • Malangizo
  • NDANDANDA
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 10/01 tsamba 3-6

Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2002

Malangizo

Mu 2002, otsatiraŵa ndiwo adzakhale makonzedwe pochititsa Sukulu ya Utumiki Wateokalase.

MABUKU OPHUNZIRA: Nkhanizi zachokera mu Revised Nyanja (Union) Version [bi53], Nsanja ya Olonda [w-CN], Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako [gt-CN], ndi Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN].

Sukulu iyenera kuyamba PANTHAŴI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje achidule. Palibe chifukwa chofotokozera ndondomeko ya pulogalamu. Pamene woyang’anira sukulu aitana wokamba nkhani iliyonse, adzatchula mutu wa nkhani imene munthuyo adzakamba. Pulogalamuyi ichitike motere:

NKHANI NA. 1: Mphindi 15. Ayenera kukamba imeneyi ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira, ndipo izitengedwa mu Nsanja ya Olonda kapena mu buku la Munthu Wamkulu Woposa Wonse Amene Anakhalako. Ngati yatengedwa mu Nsanja ya Olonda, aikambe ngati nkhani yachilangizo ya mphindi 15 yopanda mafunso obwereramo; ngati yatengedwa mu buku la Munthu Wamkulu aikambe ngati nkhani yachilangizo ya mphindi 10 mpaka 12, kenako mphindi 3 mpaka 5 za mafunso obwereramo, kugwiritsa ntchito mafunso osindikizidwa m’bukulo. Cholinga chake sichiyenera kukhala kungokamba nkhaniyo koma kusonyeza phindu lake la mfundo zimene akufotokoza, ndipo atsindike mfundo zomwe zidzakhala zothandiza kwambiri mpingowo. Agwiritse ntchito mutu wosonyezedwa.

Abale opatsidwa nkhani imeneyi azionetsetsa kuti akusunga nthaŵi. Uphungu wamseri ungaperekedwe ngati ukufunika kapena ngati wokamba nkhaniyo wachita kupempha.

MFUNDO ZAZIKULU ZA KUŴERENGA BAIBULO: Mphindi 6. Ayenera kukamba imeneyi ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira amene adzagwiritsa ntchito mfundozo pa zofunika za pampingopo. Mutu wa nkhani sufunikira kwenikweni. Isakhale chidule chabe cha gawo loŵerenga mlunguwo. Choyamba tchulani mwachidule mfundo yaikulu imene ili m’chaputala chilichonse cha machaputala a mlunguwo pa masekondi 30 mpaka 60. Komabe, cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvera kuzindikira chifukwa chake komanso mmene mfundozo zilili zaphindu kwa ife. Ndiyeno woyang’anira sukulu apemphe ophunzirawo kupita ku makalasi awo osiyanasiyana.

NKHANI NA. 2: Mphindi 5. Iyi ndi nkhani ya mbale yoŵerenga Baibulo. Nkhaniyi ikambidwe m’sukulu yaikulu limodzinso ndi m’timagulu tinato. Kaŵirikaŵiri mbali zoŵerenga zimakhala zazifupi ndipo zimapatsa wophunzira mpata wokamba mawu oyamba ndi omaliza achidule kufotokoza mavesiwo. Angaphatikizepo mbiri yakale, tanthauzo la ulosi kapena la chiphunzitso, ndi mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zake zachikhalidwe. Mavesi onse ofunikirawo ayenera kuŵerengedwa mosalekeza. Komabe, pamene mavesiwo saali ondondozana, wophunzira angatchule vesi lopitirizira kuŵerengako.

NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhaniyi ipatsidwe kwa mlongo. Mutu wa nkhaniyi uzitengedwa m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba. Chochitikacho chingakhale umboni wamwamwayi, ulendo wobwereza, kapena phunziro la Baibulo la panyumba, ndipo otenga mbaliwo angakhale pansi kapena kuimirira. Woyang’anira sukulu adzafuna makamaka kuona mmene wophunzirayo adzafotokozera mutuwo ndi kuthandiza mwininyumba kusinkhasinkha malemba. Wophunzira wopatsidwa nkhani imeneyi ayenera kudziŵa kuŵerenga. Woyang’anira sukulu asankhe wothandiza mmodzi, koma n’zotheka kugwiritsa ntchito wothandiza winanso kuwonjezera pamenepo. Chofunika kuchionetsetsa makamaka si chochitikacho, koma luso logwiritsa ntchito Baibulo.

NKHANI NA. 4: Mphindi 5. Mutu wa nkhani imeneyi uzitengedwa m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba. Mbale kapena mlongo angapatsidwe Nkhani Na. 4. Akapatsidwa mbale, aziikamba ngati nkhani koma ngati ndi mlongo amene wapatsidwa, aziikamba mofanana ndi Nkhani Na. 3.

NDANDANDA YOŴERENGA BAIBULO: Tikulimbikitsa aliyense mumpingo kutsatira ndandanda yoŵerenga Baibulo mlungu ndi mlungu, imene imafuna kuŵerenga tsamba limodzi patsiku.

CHIDZIŴITSO: Za mfundo zina ndi malangizo onena za uphungu, kusunga nthaŵi, kubwereramo kolemba, ndi kukonzekera nkhani, onani patsamba 3 la Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 1996.

NDANDANDA

Jan. 7 Kuŵerenga Baibulo: Mlaliki 1-6

Nyimbo Na. 59

Na. 1: Kuphunzitsa Mkazi wa ku Samariya (gt-CN mutu 19 ndime 1-14)

Na. 2: Mlaliki 4:1-16

Na. 3: a Kodi Mumakhulupirira za Kuchiritsa?’ (rs-CN tsa. 170 ndime 3 ndi 4)

Na. 4: Kodi Tonse Tinayamba Takhala Kumalo a Mizimu Tisanabadwe Monga Anthu? (rs-CN tsa. 203 ndime 2–tsa. 204 ndime 2)

Jan. 14 Kuŵerenga Baibulo: Mlaliki 7-12

Nyimbo Na. 25

Na. 1: Chifukwa Chake Asamariya Ambiri Akukhulupirira (gt-CN mutu 19 ndime 15-21)

Na. 2: Mlaliki 8:1-17

Na. 3: Ngati Adamu Sakanachimwa, Kodi Potsiriza Pake Akanapita Kumwamba? (rs-CN tsa. 204 ndime 3-4)

Na. 4: Kodi Munthu Ayenera Kupita Kumwamba Kuti Akhaledi ndi Tsogolo Lachimwemwe? (rs-CN tsa. 204 ndime 5-tsa. 205 ndime 1)

Jan. 21 Kuŵerenga Baibulo: Nyimbo ya Solomo 1-8

Nyimbo Na. 11

Na. 1: Chozizwitsa Chachiŵiri Ali m’Kana (gt-CN mutu 20)

Na. 2: Nyimbo ya Solomo 5:1-16

Na. 3: Kodi 1 Petro 3:19, 20 Amatanthauzanji? (rs-CN tsa. 205 ndime 2)

Na. 4: Kodi 1 Petro 4:6 Amatanthauzanji? (rs-CN tsa. 205 ndime 3)

Jan. 28 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 1-6

Nyimbo Na. 204

Na. 1: Yesu Alalikira M’tauni ya Kwawo (gt-CN mutu 21)

Na. 2: Yesaya 2:1-17

Na. 3: Kodi Akristu Onse Amayembekeza Kukakhala ndi Moyo Kumwamba? (rs-CN tsa. 206 ndime 1-3)

Na. 4: Kodi “Chipangano Chatsopano” Chimati Chiyani za Moyo Wosatha pa Dziko Lapansi? (rs-CN tsa. 207 ndime 1–tsa. 208 ndime 1)

Feb. 4 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 7-11

Nyimbo Na. 89

Na. 1: Timafunikira Gulu Lolinganizidwa la Yehova (w00-CN 1/1 mas. 30-1)

Na. 2: Yesaya 8:1-22

Na. 3: Kodi Ndi Angati Amene Baibulo Limati Ali ndi Chiyembekezo cha Moyo wa Kumwamba? (rs-CN tsa. 208 ndime 2-3)

Na. 4: Kodi a 144, 000 Ndi Ayuda Akuthupi Okha? (rs-CN tsa. 208 ndime 4–tsa. 209 ndime 2)

Feb. 11 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 12-19

Nyimbo Na. 177

Na. 1: Kodi Mumadziona Motani? (w00-CN 1/15 mas. 20-2)

Na. 2: Yesaya 17:1-14

Na. 3: Kodi a “Khamu Lalikulu” Ali ndi Chiyembekezo Chotani cha m’Malemba? (rs-CN tsa. 209 ndime 3-5)

Na. 4: Kodi Amene Amapita Kumwamba Adzachitako Chiyani? (rs-CN tsa. 210 ndime 1-5)

Feb. 18 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 20-26

Nyimbo Na. 225

Na. 1: Pangani Ubwenzi Wathithithi ndi Yehova (w00-CN 1/15 mas. 23-6)

Na. 2: Yesaya 22:1-19

Na. 3: Kodi Baibulo Limanena Kuti Moyo Umapulumuka Imfa ya Thupi? (rs-CN tsa. 144 ndime 1–tsa. 145 ndime 1)

Na. 4: Kodi Ndi Anthu Otani Amene Amapita ku Helo Amene Baibulo Limanena? (rs-CN tsa. 145 ndime 2-4)

Feb. 25 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 27-31

Nyimbo Na. 192

Na. 1: Wozunza Aona Kuunika Kwakukulu (w00-CN 1/15 mas. 27-9)

Na. 2: Yesaya 29:1-14

Na. 3: Kodi Munthu Atha Kutulukamo m’Helo Amene Baibulo Limanena? (rs-CN tsa. 145 ndime 5–tsa. 146 ndime 2)

Na. 4: Kodi Oipa Amalangidwa Kwamuyaya? (rs-CN tsa. 146 ndime 3–tsa. 147 ndime 2)

Mar. 4 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 32-37

Nyimbo Na. 98

Na. 1: Chipambano Chifukwa cha Khama (w00-CN 2/1 mas. 4-6)

Na. 2: Yesaya 33:1-16

Na. 3: Kodi ‘Chizunzo Chamuyaya’ Chotchulidwa m’Chivumbulutso N’chiyani? (rs-CN tsa. 147 ndime 3-4)

Na. 4: Kodi ‘Gehena wa Moto’ Amene Yesu Ananena N’chiyani? (rs-CN tsa. 148 ndime 1–tsa. 149 ndime 1)

Mar. 11 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 38-42

Nyimbo Na. 132

Na. 1: Uphungu Wanzeru wa Mayi (w00-CN 2/1 mas. 30-1)

Na. 2: Yesaya 42:1-16

Na. 3: Kodi Chilango cha Uchimo N’chiyani? (rs-CN tsa. 149 ndime 2-5)

Na. 4: Kodi Yesu Anaphunzitsa Kuti Oipa Adzazunzika Akamwalira? (rs-CN tsa. 149 ndime 6)

Mar. 18 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 43-47

Nyimbo Na. 160

Na. 1: Chokani M’dera Langozi (w00-CN 2/15 mas. 4-7)

Na. 2: Yesaya 44:6-20

Na. 3: Kodi Fanizo la Munthu Wachuma ndi Lazaro Limatanthauzanji? (rs-CN tsa. 150 ndime 1–tsa. 151 ndime 1)

Na. 4: Kodi Khirisimasi Ndi Phwando Lozikidwa m’Baibulo? (rs-CN tsa. 239 ndime 2–tsa. 240 ndime 1)

Mar. 25 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 48-52

Nyimbo Na. 161

Na. 1: Mphamvu ya Pemphero (w00-CN 3/1 mas. 3-4)

Na. 2: Yesaya 49:1-13

Na. 3: Kodi Anzeru Akum’maŵa, Kapena Kuti Amagi, Amene Nyenyezi Inawatsogolera kwa Yesu Anali Ndani? (rs-CN tsa. 240 ndime 2-4)

Na. 4: Kodi Tiyenera Kuganizira Chiyani Tikamapenda Miyambo ya Khirisimasi? (rs-CN tsa. 241 ndime 1-3)

Apr. 1 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 53-59

Nyimbo Na. 210

Na. 1: Kufunafuna Yehova ndi Mtima Wokonzekera (w00-CN 3/1 mas. 29-31)

Na. 2: Yesaya 54:1-17

Na. 3: Kodi Ndi Mfundo Ziti Zimene Ziyenera Kutithandiza pa Nkhani ya Mapwando? (rs-CN tsa. 241 ndime 4–tsa. 242 ndime 3)

Na. 4: Kodi Tifunikira Kudziŵa Chiyani pa za Phwando la Isitala ndi la Chaka Chatsopano? (rs-CN tsa. 242 ndime 4–tsa. 243 ndime 4)

Apr. 8 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 60-66

Nyimbo Na. 111

Na. 1: Ophunzira Anayi Aitanidwa (gt-CN mutu 22)

Na. 2: Yesaya 61:1-11

Na. 3: Kodi Maholide Okumbukira “Mizimu ya Akufa” Anayamba Bwanji? (rs-CN tsa. 244 ndime 1–tsa. 245 ndime 1)

Na. 4: Kodi Tikudziŵapo Chiyani za Tsiku la Valentine, Tsiku la Amayi, ndi Miyambo Yokumbukira za Fuko? (rs-CN tsa. 245 ndime 3–tsa. 246 ndime 2)

Apr. 15 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 1-4

Nyimbo Na. 70

Na. 1: Zozizwitsa Zowonjezereka m’Kapernao (gt-CN mutu 23)

Na. 2: Yeremiya 2:4-19

Na. 3: Kodi Baibulo Limati Chiyani za Mafano ndi Zinthu Zina Zolambira? (rs-CN tsa. 434 ndime 3–tsa. 435 ndime 3)

Na. 4: Kodi Mafano Tingawagwiritse Ntchito Kungoti Atithandize Polambira Mulungu Woona? (rs-CN tsa. 435 ndime 4-8)

Apr. 22 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 5-8

Nyimbo Na. 205

Na. 1: Chifukwa Chimene Mtundu wa Anthu Ukufunira Nkhoswe (w00-CN 3/15 mas. 3-4)

Na. 2: Yeremiya 7:1-20

Na. 3: Kodi Tiyenera Kulemekeza “Oyera Mtima” Powayesa Ankhoswe Athu kwa Mulungu? (rs-CN tsa. 435 ndime 9–tsa. 436 ndime 5)

Na. 4: Kodi Mulungu Amawaona Motani Mafano Amene Anthu Amalambira? (rs-CN tsa. 437 ndime 1-4)

Apr. 29 Kubwereramo Kolemba. Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 9-13

Nyimbo Na. 46

May 6 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 14-18

Nyimbo Na. 224

Na. 1: Mmene Yesu Kristu Angatithandizire (w00-CN 3/15 mas. 5-9)

Na. 2: Yeremiya 17:1-18

Na. 3: Kodi Tiyenera Kuwaona Motani Mafano Alionse Amene Mwina Tinali Kuwalemekeza Kale? (rs-CN tsa. 437 ndime 5–tsa. 438 ndime 2)

Na. 4: Kodi Kugwiritsa Ntchito Mafano Polambira Kungakhudze Motani Tsogolo Lathu? (rs-CN tsa. 438 ndime 3-6)

May 13 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 19-23

Nyimbo Na. 73

Na. 1: Kudzichepetsa—Mkhalidwe Umene Umalimbikitsa Mtendere (w00-CN 3/15 mas. 21-4)

Na. 2: Yeremiya 19:1-15

Na. 3: Pamene Anthu Akankhira Pambali Miyezo ya Baibulo, Kodi Amapezadi Ufulu? (rs-CN tsa. 171 ndime 1-3)

Na. 4: Kodi Uphungu wa Baibulo Umati Chiyani za Kukonda Zinthu Zakuthupi ndi Kumwetsa Mowa? (rs-CN tsa. 171 ndime 4-5)

May 20 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 24-28

Nyimbo Na. 140

Na. 1: Mwamuna wa Chitsanzo Chabwino Amene Anavomera Kum’langiza (w00-CN 3/15 mas. 25-8)

Na. 2: Yeremiya 25:1-14

Na. 3: Yamikirani Ubwenzi Wanu ndi Yehova, Ndipo Pewani Mayanjano Oipa (rs-CN tsa. 172 ndime 2)

Na. 4: Kodi Anasonkhezera Anthu Kuswa Malamulo a Mulungu Ndani? (rs-CN tsa. 172 ndime 3–tsa. 173 ndime 1)

May 27 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 29-31

Nyimbo Na. 42

Na. 1: Kodi Mzimu wa Mulungu Umagwira Ntchito Motani Lerolino? (w00-CN 4/1 mas. 8-11)

Na. 2: Yeremiya 30:1-16

Na. 3: Kodi Tiyenera Kupeŵa Maganizo Otani? (rs-CN tsa. 173 ndime 2-8)

Na. 4: Kodi Kudziimira Kukam’limbikitsa Munthu Kutsanzira Dziko, Ndani Amayamba Kum’lamulira? (rs-CN tsa. 174 ndime 1-2)

June 3 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 32-35

Nyimbo Na. 85

Na. 1: Pezani Chitonthozo M’nyonga ya Yehova (w00-CN 4/15 mas. 4-7)

Na. 2: Yeremiya 34:1-16

Na. 3: Kodi Dzina la Mulungu Limapezeka Pati M’mabaibulo Amene Ambiri Akugwiritsa Ntchito Lerolino? (rs-CN mas. 415 ndime 8–tsa. 417 ndime 8)

Na. 4: Chifukwa Chiyani Mabaibulo Ambiri Sagwiritsa Ntchito Dzina Lenileni la Mulungu? (rs-CN tsa. 417 ndime 9–tsa. 418 ndime 4)

June 10 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 36-40

Nyimbo Na. 159

Na. 1: Kodi Anthu Achiwawa Mumawaona Monga Momwe Mulungu Amawaonera? (w00-CN 4/15 mas. 26-9)

Na. 2: Yeremiya 37:1-17

Na. 3: Kodi Ndi Dzina Liti la Mulungu Lomwe Lili Lolondola, Yehova Kapena Yahwe? (rs-CN tsa. 419 ndime 1–tsa. 421 ndime 7)

Na. 4: Kodi Yehova wa mu “Chipangano Chakale” Ndiye Yesu Kristu mu “Chipangano Chatsopano”? (rs-CN tsa. 421 ndime 8–tsa. 422 ndime 3)

June 17 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 41-45

Nyimbo Na. 26

Na. 1: “Tchinjiriza Mtima Wako” (w00-CN 5/15 mas. 20-4)

Na. 2: Yeremiya 41:1-15

Na. 3: Kodi Zitheka Bwanji Munthu Kukonda Yehova Kwinaku Kumuopa Iye? (rs-CN tsa. 422 ndime 4-5)

Na. 4: Kodi Ndi Zikhulupiriro Ziti Zimene Zimasiyanitsa Mboni za Yehova ndi Zipembedzo Zina? (rs-CN tsa. 270 ndime 3–tsa. 272 ndime 3)

June 24 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 46-49

Nyimbo Na. 15

Na. 1: Moyo Wangwiro Si Loto Chabe! (w00-CN 6/15 mas. 5-7)

Na. 2: Yeremiya 49:1-13

Na. 3: Kodi Mboni za Yehova Ndi Chipembedzo cha ku America? (rs-CN tsa. 272 ndime 4–tsa. 273 ndime 3)

Na. 4: Kodi Mboni za Yehova Ndi Kagulu Kampatuko? (rs-CN tsa. 273 ndime 4–tsa. 274 ndime 4)

July 1 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 50-52

Nyimbo Na. 100

Na. 1: Chifukwa Chake Yesu Anadza Kudziko Lapansi (gt-CN mutu 24)

Na. 2: Yeremiya 50:1-16

Na. 3: Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Kuti Chipembedzo Chawo Ndi Chokhacho Cholondola? (rs-CN tsa. 275 ndime 1-2)

Na. 4: Chipembedzo Choona Chimatsata Baibulo (rs-CN tsa. 275 ndime 3)

July 8 Kuŵerenga Baibulo: Maliro 1-2

Nyimbo Na. 8

Na.1: Kuchitira Chifundo Wakhate (gt-CN mutu 25)

Na. 2: Maliro 1:1-14

Na. 3: Kodi Mboni za Yehova Zimafika Bwanji Polongosola Baibulo Mmene Zimalongosoleramu? (rs-CN tsa. 276 ndime 1-4)

Na. 4: Chifukwa Chiyani Ziphunzitso za Mboni za Yehova Zasintha? (rs-CN tsa. 277 ndime 1)

July 15 Kuŵerenga Baibulo: Maliro 3-5

Nyimbo Na. 145

Na. 1: Abwerera Kwawo ku Kapernao (gt-CN mutu 26)

Na. 2: Maliro 3:1-30

Na. 3: Chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Zimalalikira Kunyumba ndi Nyumba? (rs-CN tsa. 277 ndime 2-5)

Na. 4: Chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Amazizunza? (rs-CN tsa. 278 ndime 2-3)

July 22 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 1-6

Nyimbo Na. 94

Na. 1: Akuitana Mateyu Ndiponso Akuchita Phwando (gt-CN mutu 27)

Na. 2: Ezekieli 4:1-17

Na. 3: b ‘Chifukwa Chiyani Simuthandiza Nawo Kusintha Dzikoli Kuti Likhale Malo Abwino Kukhala?’ (rs-CN tsa. 278 ndime 4–tsa. 279 ndime 3)

Na. 4: c ‘Akristu Ayenera Kukhala Mboni za Yesu, Osati za Yehova’ (rs-CN tsa. 280 ndime 1)

July 29 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 7-12

Nyimbo Na. 221

Na. 1: Pindulani ndi Zitsanzo Zabwino (w00-CN 7/1 mas. 19-21)

Na. 2: Ezekieli 10:1-19

Na. 3: Kodi Yesu Kristu Anali Munthu Weniweni? (rs-CN tsa. 423 ndime 1–tsa. 424 ndime 1)

Na. 4: Kodi Yesu Kristu Anangokhala Munthu Wabwino Chabe? (rs-CN tsa. 424 ndime 2)

Aug. 5 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 13-16

Nyimbo Na. 106

Na. 1: Mukhoza Kudzisunga M’dziko Lachiwerewereli (w00-CN 7/15 mas. 28-31)

Na. 2: Ezekieli 13:1-16

Na. 3: Kodi Yesu Anali Mtsogoleri Chabe Ngati Mmene Analili Atsogoleri Ena Onse a Zipembedzo? (rs-CN tsa. 424 ndime 3)

Na. 4: Chifukwa Chiyani Ayuda Ambiri Sanam’landire Yesu? (rs-CN tsa. 425 ndime 1-2)

Aug. 12 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 17-20

Nyimbo Na. 214

Na. 1: Chifukwa Chiyani Tifunikira Kulemekeza Ulamuliro? (w00-CN 8/1 mas. 4-7)

Na. 2: Ezekieli 17:1-18

Na. 3: Kodi Yesu Kristu Kwenikweni Ali Mulungu? (rs-CN tsa. 426 ndime 1-2)

Na. 4: Kodi Yohane 1:1 Amatsimikiza Kuti Yesu Ndi Mulungu? (rs-CN tsa. 426 ndime 4–tsa. 427 ndime 1)

Aug. 19 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 21-23

Nyimbo Na. 86

Na. 1: Kodi Mumatani Pakakhala Kusamvana? (w00-CN 8/15 mas. 23-5)

Na. 2: Ezekieli 22:1-16

Na. 3: Kodi Kudabwa kwa Tomasi pa Yohane 20:28 Kumatsimikiza Kuti Yesu Ndi Mulungudi? (rs-CN tsa. 427 ndime 2-4)

Na. 4: Kodi Mateyu 1:23 Amasonyeza Kuti Pamene Yesu Anali pa Dziko Lapansi Anali Mulungu? (rs-CN tsa. 428 ndime 1-3)

Aug. 26 Kubwereramo Kolemba. Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 24-28

Nyimbo Na. 18

Sept. 2 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 29-32

Nyimbo Na. 40

Na. 1: N’kukhaliranji Wodzimana? (w00-CN 9/15 mas. 21-4)

Na. 2: Ezekieli 30:1-19

Na. 3: Kodi Yohane 5:18 Amatanthauzanji? (rs-CN tsa. 428 ndime 4-5)

Na. 4: Kodi Kungoti Yesu Akum’lambira Ndiye Kuti Basi Umenewo Ndi Umboni Wakuti ndi Mulungu? (rs-CN mas. 429 ndime 1-3)

Sept. 9 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 33-36

Nyimbo Na. 49

Na. 1: Mmene Mungayandikirire kwa Mulungu (w00-CN 10/15 mas. 4-7)

Na. 2: Ezekieli 33:1-16

Na. 3: Kodi Zozizwitsa Zimene Yesu Anachita Zimatsimikiza Kuti Iye Ndi Mulungu? (rs-CN tsa. 429 ndime 4–tsa. 430 ndime 2)

Na. 4: Kodi Munthu Angofunikira Kukhulupirira Yesu Kristu Basi Kuti Akapulumuke? (rs-CN tsa. 430 ndime 4)

Sept. 16 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 37-40

Nyimbo Na. 34

Na. 1: Kodi Kupambana Mumati N’kutani? (w00-CN 11/1 mas. 18-21)

Na. 2: Ezekieli 39:1-16

Na. 3: Kodi Yesu Anali ndi Moyo Kumwamba Asanakhale Munthu? (rs-CN tsa. 431 ndime 1-2)

Na. 4: Kodi Yesu Ali ndi Thupi Lake Lanyama Kumwamba? (rs-CN tsa. 431 ndime 3-6)

Sept. 23 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 41-45

Nyimbo Na. 50

Na. 1: Tumikirani Mulungu ndi Mzimu Wofunitsitsa (w00-CN 11/15 mas. 21-3)

Na. 2: Ezekieli 42:1-20

Na. 3: Kodi Yesu Kristu Ndiyenso Mikaeli Mngelo Wamkulu? (rs-CN tsa. 432 ndime 1-3)

Na. 4: d ‘Simukhulupirira Yesu’ (rs-CN tsa. 433 ndime 1-3)

Sept. 30 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 46-48

Nyimbo Na. 112

Na. 1: Afunsidwa za Kusala Chakudya (gt-CN mutu 28)

Na. 2: Ezekieli 46:1-15

Na. 3: e ‘Kodi Mumavomereza Yesu Kukhala Mpulumutsi Wanu?’ (rs-CN tsa. 433 ndime 4–tsa. 434 ndime 1)

Na. 4: f ‘Ndinavomereza Yesu Kukhala Mpulumutsi Wanga’ (rs-CN tsa. 434 ndime 2)

Oct. 7 Kuŵerenga Baibulo: Danieli 1-4

Nyimbo Na. 10

Na. 1: Kuchita Ntchito Zabwino pa Sabata (gt-CN mutu 29)

Na. 2: Danieli 1:1-17

Na. 3: Kodi Ayuda Achibadwidwe Lerolino Ndi Anthu Osankhika a Mulungu? (rs-CN tsa. 42 ndime 2–tsa. 43 ndime 4)

Na. 4: Kodi Ayuda Onse Adzatembenuka ndi Kukhulupirira Kristu? (rs-CN tsa. 44 ndime 1-2)

Oct. 14 Kuŵerenga Baibulo: Danieli 5-8

Nyimbo Na. 191

Na. 1: Kodi Muyenera Kukhulupirira Zimene “Anzeru” Anena? (w00-CN 12/1 mas. 29-31)

Na. 2: Danieli 5:1-16

Na. 3: Kodi Ayuda Afunikira Kukhulupirira Yesu Kuti Akapulumuke? (rs-CN tsa. 44 ndime 3-4)

Na. 4: Kodi Zimene Zikuchitika ku Israyeli Lerolino Zikukwaniritsa Ulosi wa Baibulo? (rs-CN tsa. 45 ndime 1–tsa. 46 ndime 2)

Oct. 21 Kuŵerenga Baibulo: Danieli 9-12

Nyimbo Na. 108

Na. 1: Yesu Akuwayankha Anthu Amene Akumuimba Mlandu (gt-CN mutu 30)

Na. 2: Danieli 10:1-21

Na. 3: Kodi Maulosi Onena za Kubwezeretsedwa kwa Israyeli Akukwaniritsidwa Lero? (rs-CN tsa. 46 ndime 3–tsa. 47 ndime 2)

Na. 4: Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Boma Lenileni? (rs-CN tsa. 375 ndime 1-2)

Oct. 28 Kuŵerenga Baibulo: Hoseya 1-14

Nyimbo Na. 23

Na. 1: Kodi N’kololeka Kubudula Ngala pa Sabata? (gt-CN mutu 31)

Na. 2: Hoseya 4:1-19

Na. 3: Kodi Olamulira Ndani mu Ufumuwo? (rs-CN tsa. 375 ndime 3-5)

Na. 4: Kodi Ufumu wa Mulungu Udzawakhudza Motani Maboma a Anthu? (rs-CN tsa. 376 ndime 1-2)

Nov. 4 Kuŵerenga Baibulo: Yoweli 1-3

Nyimbo Na. 166

Na. 1: Kodi Chololeka N’chiyani pa Sabata? (gt-CN mutu 32)

Na. 2: Yoweli 1:1-20

Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzayeretsa Dzina la Yehova (rs-CN tsa. 376 ndime 3-5)

Na. 4: Ufumu wa Mulungu Udzagwirizanitsa Zolengedwa Zonse pa Kulambira Koyera (rs-CN tsa. 377 ndime 1-2)

Nov. 11 Kuŵerenga Baibulo: Amosi 1-9

Nyimbo Na. 80

Na. 1: Kukwaniritsa Ulosi wa Yesaya (gt-CN mutu 33)

Na. 2: Amosi 1:1-15

Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzathetsa Nkhondo ndi Kuipa (rs-CN tsa. 377 ndime 3–tsa. 378 ndime 1-2)

Na. 4: Ufumu wa Mulungu Udzapereka Chakudya kwa Anthu Onse ndi Kuthetsa Matenda (rs-CN tsa. 378 ndime 3-5)

Nov. 18 Kuŵerenga Baibulo: Obadiya 1–Yona 4

Nyimbo Na. 96

Na. 1: Kusankha Atumwi Ake (gt-CN mutu 34)

Na. 2: Obadiya 1:1-16

Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzapereka Nyumba, Ntchito ndi Chitetezo (rs-CN tsa. 378 ndime 6–tsa. 379 ndime 2)

Na. 4: Ufumu wa Mulungu Udzachititsa Chilungamo Kufala (rs-CN tsa. 379 ndime 3-5)

Nov. 25 Kuŵerenga Baibulo: Mika 1-7

Nyimbo Na. 138

Na. 1: Ulaliki Wotchuka Woposa Wonse Umene Unaperekedwa (gt-CN mutu 35 ndime 1-6)

Na. 2: Mika 1:1-16

Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzaukitsa Akufa (rs-CN tsa. 379 ndime 6–tsa. 380 ndime 2)

Na. 4: Ufumu wa Mulungu Udzadzetsa Dziko la Chikondi ndi Mgwirizano (rs-CN tsa. 380 ndime 3-5)

Dec. 2 Kuŵerenga Baibulo: Nahumu 1–Habakuku 3

Nyimbo Na. 137

Na. 1: Kodi Ndani Amene Alidi Odala? (gt-CN mutu 35 ndime 7-17)

Na. 2: Nahumu 3:1-19

Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzasandutsa Dziko Lapansi Paradaiso (rs-CN tsa. 380 ndime 6–tsa. 381 ndime 1)

Na. 4: Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Kulamulira Zaka za Zana Loyamba? (rs-CN tsa. 381 ndime 2-4)

Dec. 9 Kuŵerenga Baibulo: Zefaniya 1–Hagai 2

Nyimbo Na. 146

Na. 1: Muyezo Wapamwamba wa Otsatira Ake (gt-CN mutu 35 ndime 18-27)

Na. 2: Zefaniya 2:1-15

Na. 3: Kodi Dziko Lonse Lifunika Liyambe Latembenuka Mtima Kuti Ufumu wa Mulungu Udze? (rs-CN tsa. 381 ndime 5–tsa. 382 ndime 1)

Na. 4: g ‘Ufumu wa Mulungu Subwera Ine Ndili Moyo’ (rs-CN tsa. 382 ndime 3-4)

Dec. 16 Kuŵerenga Baibulo: Zekariya 1-8

Nyimbo Na. 1

Na. 1: Pemphero ndi Chidaliro mwa Mulungu (gt-CN mutu 35 ndime 28-37)

Na. 2: Zekariya 6:1-15

Na. 3: N’chiyani Chikusonyeza Kuti Tili M’masiku Otsiriza? (rs-CN tsa. 261 ndime 2)

Na. 4: Kodi Ndi Motani Mmene Nkhondo ndi Njala Zakhalira “Chizindikiro”? (rs-CN tsa. 262 ndime 1–tsa. 263 ndime 1)

Dec. 23 Kuŵerenga Baibulo: Zekariya 9-14

Nyimbo Na. 176

Na. 1: Njira ya Kumoyo (gt-CN mutu 35 ndime 38-49)

Na. 2: Zekariya 9:1-17

Na. 3: Kodi Luka 21:11 Wakhala Akukwaniritsidwa Motani Chiyambireni 1914? (rs-CN tsa. 263 ndime 2–tsa. 264 ndime 1)

Na. 4: Kodi Kuwonjezeka kwa Kusaweruzika Kukusonyeza Chiyani? (rs-CN tsa. 264 ndime 2-3)

Dec. 30 Kubwereramo Kolemba. Kuŵerenga Baibulo: Malaki 1-4

Nyimbo Na. 118

[Mawu a M’munsi]

a Ngati nthaŵi ilola, wophunzira ayankhe zimene mwiniyumba akunena, kutsutsa, ndi zina zotero, kuti akwanitse zosoŵa za m’gawolo.

b Ngati nthaŵi ilola, wophunzira ayankhe zimene mwiniyumba akunena, kutsutsa, ndi zina zotero, kuti akwanitse zosoŵa za m’gawolo.

c Ngati nthaŵi ilola, wophunzira ayankhe zimene mwiniyumba akunena, kutsutsa, ndi zina zotero, kuti akwanitse zosoŵa za m’gawolo.

d Ngati nthaŵi ilola, wophunzira ayankhe zimene mwiniyumba akunena, kutsutsa, ndi zina zotero, kuti akwanitse zosoŵa za m’gawolo.

e Ngati nthaŵi ilola, wophunzira ayankhe zimene mwiniyumba akunena, kutsutsa, ndi zina zotero, kuti akwanitse zosoŵa za m’gawolo.

f Ngati nthaŵi ilola, wophunzira ayankhe zimene mwiniyumba akunena, kutsutsa, ndi zina zotero, kuti akwanitse zosoŵa za m’gawolo.

g Ngati nthaŵi ilola, wophunzira ayankhe zimene mwiniyumba akunena, kutsutsa, ndi zina zotero, kuti akwanitse zosoŵa za m’gawolo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena