Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati palibe mabuku ameneŵa, mungagaŵire mabuku aŵa, Achichepere Akufunsa—Mafunso amene Amathandiza, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. January: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. February: Buku lililonse lakale la masamba 192 limene mpingo uli nalo. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
◼ Mipingo iyambe kufunsira mabaundi voliyumu a Watchtower ndi Awake! a 2001 pofunsira mabuku awo a December. Mabaundi voliyumuwa adzakhalapo m’Chingelezi ndi Chifalansa. Adzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera katundu wa mipingo kufikira pamene mabaundi voliyumu adzakhalapo ndi kutumizidwa. Mabaundi voliyumu ndi zinthu za oda yapadera.
◼ Mapepala a mpingo uliwonse oitanira anthu ku Chikumbutso cha 2002 adzabwera pamodzi ndi mabuku ndi magazini mu February 2002.
◼ Dziŵani kuti Chikumbutso cha 2003 chidzachitika Lachitatu, pa April 16, dzuŵa litaloŵa. Taneneratu zimenezi kuti abale apangiretu makonzedwe ofunikira opeza maholo ena ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndipo ikufunikadi kupeza malo ena. Akulu ayenera kugwirizana ndi eni malowo n’kutsimikizira kuti mwambowu usadzadodometsedwe ndi zochitika zina pamalowo kuti Chikumbutsocho chidzachitike mwamtendere ndi mwadongosolo. Popeza mwambowu ndi wapadera, posankha wokamba nkhani ya Chikumbutso, bungwe la akulu liyenera kusankha mkulu yemwe alidi woyenerera, osati kumangosinthana mwachisawawa kapena kuti chaka chilichonse azingokamba mbale mmodzimodzi yemweyo. Ngati pali wodzozedwa amene ndi mkulu komanso angathe kukamba nkhaniyo musankheni ameneyo.
◼ Pamsonkhano Wachigawo wa mutu wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu” tinasangalala kumva kuti posachedwapa tilandira buku latsopano la Sukulu ya Utumiki Wateokalase lamutu wakuti Benefit From Theocratic Ministry School Education. M’malo ena a msonkhanowu analengeza kuti bukuli lidzayamba kugwira ntchito mu Sukulu ya Utumiki Wateokalase mu July 2002. Ngakhale kuti bukuli lidzakhala litatuluka nthaŵi imeneyi, lidzayamba kugwira ntchito m’sukulu kuyambira January 2003.
◼ Pa mafomu a S-18 taona kuti mipingo yambiri imasunga mulu wa mabuku ena ake. Ngati mabuku ameneŵa sagwiritsidwa ntchito, ndiye kuti ndalama zambiri zimangowonongeka. Chonde aperekeni kwa ofalitsa mu mpingo wanu ndipo alimbikitseni kuti awagwiritse ntchito mu utumiki kapena agwiritse ntchito iwowo. Ngati mabuku otereŵa muli nawo ambiri, chonde perekani ku mipingo imene mwayandikana nayo. Mukatha kugaŵira mabuku ndi magazini otsalawa mu mpingo wanu ndi m’mipingo yapafupi, ndipo mwatsala ndi ena abwinobwino, chonde m’patseni woyendetsa galimoto ya Sosaite yonyamula mabuku. Ndiyeno muzitumiza oda yanu ya mabuku ku ofesi ya nthambi mwezi uliwonse, koma muziitanitsa okhawo amene mudzagwiritsa ntchito mwezi umenewo. Zinthu za oda yapadera monga ma Baibulo ndi ma Yearbook, muziitanitsa kokha pakakhala wofalitsa amene waitanitsa mwapadera. Musamasunge mabuku ameneŵa. Ngati mukufuna kuchepetsa oda yanu ya mwezi ndi mwezi ya magazini, chonde lembani pa fomu ya M-202 ndikuitumiza ku ofesi ya nthambi.