Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/01 tsamba 5-6
  • Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 12/01 tsamba 5-6

Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase

Kubwereramo kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa September 3 kufikira December 24, 2001. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.

[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso n’ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]

Yankhani kuti Zoona kapena Zonama m’ndemanga zotsatirazi:

1. Popeza chikhulupiriro ndi chipatso cha mzimu wa Mulungu, anthu amene alibe chikhulupiriro sakufunafuna mzimuwo, kapena akuufunafuna ndi cholinga cholakwika kapena akukana kuti ugwire ntchito pamoyo wawo. (Luka 11:13; Agal. 5:22) [rs-CN tsa. 67 ndime 1]

2. Masalmo 58:4 amasonyeza molondola kuti mphiri ili ndi ‘makutu’ amene sagwira ntchito chifukwa iyo ndi yogontha mwachibadwa. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani Rbi8 tsa. 1583.]

3. “Khamu lalikulu” la akazi limene alitchula pa Salmo 68:11 anali adzakazi achilendo amene amuna achiisrayeli anawamasula muukapolo pamene ankagonjetsa mitundu imene anali kudana nayo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 10/15 tsa. 31 ndime 6.]

4. Ngati nthaŵi ya kumwalira kwa munthu ndiponso mmene adzamwalirire zinakonzedweratu ndi Mulungu munthuyo asanabadwe kapena pamene ankabadwa, sipakanafunikanso kupeŵa zinthu zoopsa kapena kusamalira thanzi lathu, ndipo njira zodzitetezera sizikanasintha chiŵerengero cha anthu amene akumwalira. [rs-CN tsa. 114 ndime 4]

5. Mawu a Paulo akuti “munthu asapeputse ubwana wako” akusonyeza kuti Timoteo anali asanakwanitse zaka 20 kapena anali atangopitirira kumene zaka zimenezo. (1 Tim. 4:12) [w99-CN 9/15 tsa. 29 ndime 1-3; tsa. 31 ndime 2]

6. “Ambuye wanga” wotchulidwa pa Salmo 110:1, ndi Yesu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 6/1 tsa. 28 ndime 5.]

7. Salmo 139:13-16 limasonyeza kuti dongosolo la majini linali kudziŵika zaka pafupifupi 3,000 a sayansi asanatulukire zimenezi. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 5/15 tsa. 4.]

8. Ngakhale kuti Malemba amanena kuti Yesu ndi “mulungu” kapenanso kuti “Mulungu wamphamvu” palibe pamene amanena kuti iye ndi wamphamvuyonse. (Yoh. 1:1; Yes. 9:6; Gen. 17:1) [rs-CN tsa. 311 ndime 4]

9. Miyambo 8:22-31 ikungofotokoza nzeru basi. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 5/15 tsa. 28.]

10. Langizo la Baibulo, limene lili pa Miyambo 21:17, lakuti tipeŵe ‘kukonda zoseketsa’ limasonyeza kuti kusangalala n’kolakwika chifukwa choti kumadya nthaŵi yomwe ikanagwiritsidwa ntchito pa zinthu zofunika kwambiri. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w97-CN 10/1 tsa. 27 ndime 7.]

Yankhani mafunso otsatiraŵa:

11. Kodi chidzudzulo chofeŵa cha Yesu kwa Marita chinaphunzitsa chiyani? (Luka 10:40, 41) [w99-CN 9/1 tsa. 30 ndime 7]

12. Kodi Yehova anamulandira wamasalmo “m’ulemerero” wotani? (Sal. 73:24) [4 Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 12/15 tsa. 29 ndime 3.]

13. Malinga ndi Salmo 84:1-3, kodi wamasalmo akusonyeza kuti ankauona motani mwayi wautumiki? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w97-CN 3/15 tsa. 8 ndime 5-7.]

14. Kodi malemba a Chivumbulutso 22:17 ndi Aroma 2:4, 5 amasonyeza motani kuti Yehova sadziŵiratu kapena kukonzeratu chilichonse chimene anthu amachita? [rs-CN tsa. 117 ndime 2-3]

15. Popeza Akristu oyambirira ankakhulupirira kuti kudzakhala Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Yesu monga mmene buku la Chivumbulutso limanenera, kodi n’chiyani chinachititsa Akristu ampatuko kukana chiphunzitso cha Mulungu chimenechi m’kupita kwa nthaŵi? [w99-CN 12/1 tsa. 6 ndime 3–​tsa. 7 ndime 5]

16. Kodi Akristu ayenera kukhala ndi malire otani pa ‘kupenyerera’ za anthu ena? (Afil. 2:4) [w99-CN 12/1 tsa. 29 ndime 1]

17. Kodi mawu a pa Salmo 128:3 onena za ana, “onga timitengo ta azitona” pa gome la munthu amatanthauza chiyani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w00-CN 8/15 tsa. 30 ndime 4.]

18. Ngati timaona kuti ntchito za Mulungu n’zoopsa, kodi zidzatikhudza motani? (Sal. 139:14) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 10/1 tsa. 15 ndime 18.]

19. Kodi n’chifukwa chiyani Miyambo 5:3, 4 imanena kuti chimaliziro cha chiwerewere “n’choŵaŵa ngati chivumulo” ndi “chakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse”? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w00-CN 7/15 tsa. 29 ndime 2.]

20. Mogwirizana ndi Miyambo 14:29, kodi kuzindikira kungatithandize motani kupeŵa zotsatirapo za kusaleza mtima ndi kukwiya kosalamulirika? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w97-CN 3/15 tsa. 13 ndime 7-8.]

Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:

21. Aneneri oona ankalankhula ․․․․․․․ ndipo ankadziŵikitsa ․․․․․․․ . (Deut. 18:18-20; 1 Yoh. 4:1-3) [rs-CN tsa. 32 ndime 1, 3]

22. Cholinga cha Miyambo chili ndi mbali ziŵiri—kuzindikiritsa ․․․․․․․ ndi kupereka ․․․․․․․ (Miy. 1:1-4) [w99-CN 9/15 tsa. 13 ndime 1]

23. ‘Ngaka ya Wam’mwambamwamba’ ndiwo malo a ․․․․․․․ kwa anthu amene ali kumbali ya Mulungu pankhani ya ․․․․․․․ ameneŵa ndi malo obisika, kapena osadziŵika, kwa anthu amene ․․․․․․․ . (Sal. 91:1) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 12/15 tsa. 30 ndime 6.]

24. ‘Kusaiŵala zokoma zonse za Yehova’ mwachionekere kumachitika mwa ․․․․․․․ pa “zokoma zake,” zochita zake za kukoma mtima kwachikondi monga momwe Salmo 103 amafotokozera. (Sal. 103:2) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w99-CN 5/15 tsa. 21 ndime 5-6.]

25. ․․․․․․․ ndiko kutha kuona tanthauzo la nkhani ndi kuzindikira nkhani yonseyo mwa kumvetsa kugwirizana kwa mbali zake zonse ndi mutu wa nkhaniyo, potero mukumamvetsa tanthauzo lake. (Miy. 4:1) [w99-CN 9/15, tsa. 13]

Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:

26. Ngakhale kuti anali ndi zifukwa zokwanira zokwiyira malinga ndi zimene Sauli anam’chitira, Davide anadziletsa chifukwa chakuti (ankadziŵa kuti Sauli anali wopanda ungwiro ndi kuti atumiki a Mulungu ayenera kukhala okhululuka; ankaganizira za unansi wake ndi Yehova; ankadziŵa kuti kuweruza ena n’kulakwa). (1 Sam 24:6, 15) [w99-CN 8/15 tsa. 8 ndime 7]

27. Kumvetsa, chidziŵitso, kuchenjera, ndiponso luso la kulingalira ndi zina mwa zinthu zambiri zomwe zimapanga ( nzeru; mwambo; chilungamo); (ubwino; kumvetsa; kuganiza bwino) ndiko kutha kuona tanthauzo la nkhani ndi kuzindikira nkhani yonseyo mwa kumvetsa kugwirizana kwa mbali zake zonse ndi mutu wa nkhaniyo, potero mukumamvetsa tanthauzo lake. (Miy. 1:1-4) [w99-CN 9/15 tsa. 13 ndime 2]

28. Yosefe anatha kukana kunyengerera kwa mkazi wa Potifara kuti agone naye chifukwa (ankadziŵa Chilamulo cha Mose chimene chinaletsa kuchita chigololo; ankafuna kulemekeza udindo waukulu umene Potifara anali nawo; ankaona ubwenzi wake ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali). (Gen. 39:7-9) [w99-CN 10/1 tsa. 29 ndime 3]

29. Amene analemba Salmo 119 mwachionekere ankayamikira kwambiri ( mawu kapena chilamulo cha Mulungu; mphatso ya moyo; chiyembekezo cha kupulumuka), zimene akutchula pafupifupi m’vesi iliyonse ya salmo limeneli. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w99-CN 11/1 tsa. 9 ndime 5; w87-CN 3/15 tsa. 28 ndime 2.]

30. Mwachidziwikire, “milungu” imene akuitchula pa Salmo 82 ndiyo (Satana ndi ziwanda; milungu yachikunja ya mitundu ya anthu; amuna amene anali oweruza a Israyeli). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 12/15 tsa. 29.]

Gwirizanitsani malemba otsatiraŵa ndi ndemanga zomwe zili m’munsizi:

Miy. 2:19; 14:15; 3:27, 28; Aroma 10:17; Aheb. 13:18

31. Kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro, afunika choyamba adziŵe zimene Baibulo limanena ndi kulipenda mosamalitsa. [rs-CN tsa. 68 ndime 3]

32. Akristu sangatengere zochita zina za malonda zimene zili zachinyengo ndiponso zimene zimanyalanyaza zofuna zoyenerera za anthu ena. [w99-CN 9/15 tsa. 10 ndime 2]

33. Anthu amene amachita chisembwere angafike poti sangachitire mwina koma kufa, asanafike poti angathe kuchira. [w99-CN 11/15 tsa. 27 ndime 4-5]

34. Munthu wanzeru ndi wozindikira amapenda zotsatirapo za zimene angachite ndipo satsatira zinthu zatsopano mwachimbulimbuli chabe chifukwa chakuti n’zofala. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani g94-CN 12/8 tsa. 18 ndime 1.]

35. Tikapeza mpata wochitira ena zabwino, kaya mwauzimu kapena mwakuthupi, tiyenera kuugwiritsa ntchito mpatawo ndi kuthandiza anzathu, makamaka abale athu auzimu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu: onani w93-CN 12/15 tsa. 20.]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena