Kulalikira Uthenga Wabwino—Monga Banja
1 Banja lodzipatulira limene limachita mokwanira ndiponso ndi mtima wonse utumiki wopatulika kwa Mulungu kuyambira bambo, mayi, ndi ana, limatamanda dzina lalikulu la Yehova. Tikusangalala kuti padziko lonse, m’mipingo ya anthu a Yehova tili ndi mabanja ambiri otero. Yesu anati: “Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Mawu ameneŵa amapatsa Mkristu aliyense wachikumbumtima chabwino ntchito yolalikira, kuuza ena uthenga wabwino wa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu. Popeza ana amatsanzira kwambiri chitsanzo cha makolo oopa Mulungu, anawo angalimbikitsidwe kuika zinthu za Ufumu patsogolo ngati makolo awo amalimbikira mu utumiki wakumunda ndiponso ngati amayesetsa kuchita zomwe angathe mu ntchito yolalikira.
2 Makolo azipita mu utumiki wakumunda ndi ana awo kuyambira pomwe anawo akadali aang’onoang’ono. Uwu ndi udindo wina wa makolo. Ngati zingatheke, bambo kapena mayi, kapena onse aŵiri, nthaŵi zonse aziphunzitsa ana awo utumiki wakumunda. Komabe nthaŵi zina zimenezi zimavuta. Koma tonse tingavomereze kuti kuchitira pamodzi zimenezi monga banja n’kolimbikitsa ndi kosangalatsa ndiponso kungabale zipatso zambiri. Nthaŵi zina anthu amamvetsera kwambiri ulaliki wosavuta koma wogwira mtima wa mwana. Ndiyeno Mayi kapena Bambo ake amam’thandiza mwanayo ngati pangafunike kutero.
3 Kodi mungachite chiyani kuti muthandize ana anu kudziŵa ndi kuchita utumiki wakumunda? Konzekerani pamodzi utumiki wakumunda monga banja. Nthaŵi zambiri, ngakhale ana aang’ono angathe kupereka kapepala koitanira anthu kapena thirakiti kwa mwininyumba. Angalalikire nawo mwa kuitanira anthu ku Nyumba ya Ufumu, ndi kuwauza kuti ndi aufulu kudzafika. Akafika panyumba ya munthu, makolo angatchule zoti mwana wawoyo akuphunzira utumiki ndipo akusangalala kuyenda naye. Mwanayo akamachita bwino mu utumiki, makolo anganene kaye mawu oyamba akafika pa nyumba ya munthu ndiyeno m’kumuuza mwanayo kuŵerenga lemba kapena kungosonyeza magazini. Ana ambiri amasangalala ndi ulaliki wa magazini. Ulaliki wa magazini wachidule suvuta kuphunzira. Musanyozere zimene ana angachite mu utumiki! Kaŵirikaŵiri eninyumba amachita chidwi ndi ana amene amalankhula bwino pa nyumba zawo.—Mat. 21:16.
4 Mayi a mtsikana wina wa zaka zinayi anathandiza mtsikana wawoyu kuloŵeza Yohane 17:3. Mwanayu ankakonda kunena pamtima lembali pakhomo la munthu atatsegula Baibulo lake. Amayi ake akuti “Mlungu uno mwamuna wina anakana kuti ndiŵerenge naye lemba la m’Baibulo, ndipo akutseka chitseko, mwana wangayu anati: ‘Kodi ndingaŵerenge nanu lemba?’ Nthaŵi yomweyo mwamuna uja anayankha kuti inde ndipo anatsegulanso chitseko chija.” Lalikirani limodzi ndi ana anu. Yambani akadali ang’onoang’ono. Athandizeni malinga ndi luso lawo. Yamikirani ntchito yawo ndi kupita kwawo patsogolo.—Onani Olinganizidwa, masamba 99-100.
5 Bambo ena ponena za mwana wawo wamwamuna anati: “Luso lake logwira malemba limam’thandiza kuchita bwino kwambiri mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba chifukwa eninyumba ambiri amadabwa ndipo sakana magazini ophunzirira Baibulo amene iye amawagaŵira. Wakhala akuchita utumiki wachikristu umenewu kuyambira ali ndi zaka zitatu, ndipo pano [ali ndi zaka zisanu ndi chimodzi] amagaŵira mabuku a nkhani za m’Baibulo ambiri kuposa ine ndi mkazi wanga.”
6 N’zoonekeratu kuti akulu ndi makolo angathandize kwambiri mwa kulimbikitsa ndi kuthandiza ana amene akupita patsogolo kuti akhale otamanda Yehova. (Miy. 3:27) Pulogalamu yophunzitsa mwana pang’onopang’ono imeneyi, pamodzi ndi chitsanzo chanu monga makolo, zidzathandiza mwana wanuyo kuyamba moyo umene udzam’chititsa kukuyamikirani kosatha. (Miy. 22:15; 23:13, 14) Pangitsani ulaliki kukhala wokondweretsa kwambiri mwa kukonzekeretsa mwana wanu kuchita nawo ntchitoyi mokwanira.