Kukondwera ndi Madalitso a Yehova!
N’zosangalatsa kuona kuti m’chaka chautumiki cha 2001, Yehova anadalitsa kwambiri ntchito yathu m’Malaŵi muno. Mwezi ulionse tinganene kuti pankapezeka ofalitsa 47,591 amene anali kuchita nawo utumiki wa Yehova, kusonyeza kuti panawonjezeka anthu 8 pa anthu 100 alionse. Tinali ndi chiŵerengero choposa ziŵerengero zonse za m’mbuyomo cha ofalitsa 49,196. Ndipo mu April tinali ndi chiŵerengero chachikulu choposa n’kale lonse cha anthu 6,845 amene anali kuchita utumiki waupainiya wothandiza ndi wokhazikika!
Pamapeto a chaka chautumiki, panali mipingo 781, ndipo tikayerekeza ndi mipingo imene inalipo chaka chatha yaposa ndi mipingo 92. Tinali ndi chiŵerengero chachikulu cha magazini, mabuku ndi mabulosha amene tinagaŵira. Tinaposa chiŵerengero cha magazini amene tinagaŵira chaka chautumiki cha 2000 ndi magazini oposa miliyoni imodzi! Tinathera maola ambiri mu utumiki wakumunda, tinapanga maulendo obwereza ambiri ndiponso tinachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba ochuluka. Anthu 4,728 anabatizidwa. Anthu amene anabatizidwawa anaposa chiŵerengero cha amene anabatizidwa chaka chatha ndi 2,196.
N’zosangalatsa kwambiri kukuuzaninso kuti mapeto a August panali Nyumba za Ufumu 251 zimene anamaliza kuzimanga. Pakalipano, palinso Nyumba zambiri zimene amaliza kumanga, popeza abale athu akumamaliza Nyumba za Ufumu 20 kapena 30 pamwezi! M’mipingo ina, chiŵerengero cha opezeka pamisonkhano tsopano chaŵirikiza kaŵiri, ngakhalenso katatu.
Tikukhaladi m’nthaŵi yosangalatsa m’munda wa Malaŵi. Kodi pali mbali ina ya utumiki yofunika kugwirirapo ntchito? Inde, ilipo. Ngakhale kuti mwezi uliwonse tingati tinkachititsa maphunziro a Baibulo oposa 5,000 kuposa amene tinkachititsa chaka cha 2000, pali ntchito yochuluka yophunzitsa ena yomwe tifunika kuchita malinga ndi mmene anthu m’munda akusonyezera chidwi. (Mat. 28:19, 20) Ngati ndinu mutu wa banja, kodi mukuchititsa phunziro la Baibulo m’banja lanu mokhazikika, mlungu uliwonse? Tifunika kupitirizabe ‘kuwoka’ ndi ‘kuthirira,’ ngakhalenso m’mabanja mwathu momwe.
Chifukwa cha dalitso la Yehova takhala ndi zotsatira zabwino kwambiri! Ndipo tili nanu limodzi kutamanda Yehova, amene amachulukitsa.—1 Akor. 3:6, 7.