Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/01 tsamba 3
  • Kuchitira Ana Zabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchitira Ana Zabwino
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 12/01 tsamba 3

Kuchitira Ana Zabwino

1 Yehova nthaŵi zonse amadera nkhaŵa anthu ovutika. (Sal. 146:7-9) M’nthaŵi zakale anakonza dongosolo lapadera kuti azionetsetsa kuti ngakhale ana ovutika anali kusamalidwa. Chilamulo chake kwa Israyeli chimatchula mwachindunji “mwana wamasiye.” (Eks. 22:22-24) Ngakhale kuti masiku ano sitikuyendera chilamulo chakale, kodi ife monga Akristu, mfundo ya lamulo limenelo sikutikhudza?

2 M’mipingo ina ya Mboni za Yehova, muli ana amene tingati ndi ‘amasiye.’ Zingakhale choncho chifukwa chakuti makolo awo ndi osakhulupirira. Makolo a achinyamata ena ndi okhulupirira amene amafuna kuti athandizidwe kuphunzitsa ana awo mwauzimu. Makolo amadziŵa kuti ndi ntchito yawo kuphunzitsa ana awo choonadi cha Mawu a Mulungu ndipo izi n’zimene makolo ambiri akuchita. (Deut. 6:6, 7) Komabe, ana onse amasangalala kuwayamikira ndi kuwalimbikitsa, ndipo mosakayikira alipo makolo ena amene akufuna kuthandizidwa kuphunzitsa ana awo utumiki wakumunda.

3 Kodi Mungachite Chiyani?: Funso limene anthu onse a mu mpingo ayenera kulingalira mozama n’lakuti: “Kodi ndi motani mmene ndingathandizire ana ndi kuwalimbikitsa?” Anthu amene amakhala ndi nkhani yoti akambe pa misonkhano, nthaŵi zina angaikeponso ana. Kodi ana osiyanasiyana achitsanzo chabwino mu mpingo angagwiritsidwe ntchito m’mbali zina pamsonkhano? (Mac. 16:1, 2) Ngakhale kuti ena salankhula mwaluso, kuwapatsako mwayi nthaŵi zina kumawalimbikitsa komanso kumalimbikitsa mpingo. Ana ena amachedwa kuphunzira, koma kuwaphunzitsa zinthu zosiyanasiyana, ndi kuwasamalira nthaŵi zonse kudzabweretsa phindu lalikulu pamene ana athu amene akutsatira mosamala zimene tawaphunzitsazo akukula m’choonadi.

4 Mulungu wapatsa makolo udindo wothandiza ana awo. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti ena sangawathandize? Ayi, si choncho. Kodi nthaŵi zina popita mu utumiki, mungayendeko ndi mwana mmodzi wa makolo amene ali ndi ana ambiri ofunika kuwaphunzitsa utumiki wakumunda? Bwanji osaitana banja lina kudzakhala nanu pamene banja lanu likukonzekera Nsanja ya Olonda ya pamsonkhano wa mpingo wa mlungu umenewo? Kodi mawu a mtumwi Paulo akuti “futukukani” sakugwira ntchito pankhani imeneyi?—2 Akor. 6:11-13, NW.

5 Mungalankhulane ndi ana misonkhano isanayambe ndiponso itatha. Osati ungokhala “Moni” ndi “Uli bwanji?” basi. Mkulu wina anapatsa moni mwana wina, koma mwanayo asanayankhe, mkulu uja anayamba kulankhulana ndi mbale wachikulire amene ankafuna kuti aonane naye. Ndiyeno mwana uja anapita kwa mkulu uja ndi kum’funsa kuti: “Kodi mumafunadi kudziŵa kuti ndili bwanji?” Mkulu uja anati anatengapo phunziro.

6 Ana amasangalala kuwadziŵa mayina awo. Inde, iwonso ndi mbali ya mpingo ndipo anthu achikulire ayenera kukhala nawo paunansi wabwino. Kodi si zoona kuti ana akamakuonani monga “mnzawo” savuta kumvera uphungu ndi malangizo?

7 Zimatsala M’maganizo: Ndithudi ambirife tikaganizira za m’mbuyo timakumbukira bwinobwino zinthu zina zabwino zimene ankatipatsa tili ana. Ankatilimbikitsa ndipo tinkayamikira chidwi chimene anali kutisonyeza, kodi sichoncho? Kodi chinakusangalatsani n’chiyani? Kodi ndi mbali yochepa imene munachita m’chitsanzo? Kapena ndi mawu abwino okulangizani kapena okuyamikirani amene munthu wachikulire ananena? Kapena mwina ndi zimene zinakuchitikirani mu utumiki wakumunda mukuyenda ndi mbale kapena mlongo wachikulire? Mwa kuona onse mumpingo monga mbali ya “banja” lalikulu la mpingo, ana ndi achikulire omwe adzapindula kwambiri. Pamene tikuyesetsa kutsanzira chitsanzo cha Yehova chosamalira ndi kukonda anthu onse, tipitirize kuchitira ana athu zabwino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena