Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira December 10
Mph. 3: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina muzisankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 10: “Kukondwera ndi Madalitso a Yehova!” Nkhani yolimbikitsa ndi kukambirana ndi omvetsera.
Mph. 12: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: “Madalitso Amene Amabwera Chifukwa Choyamikira Chikondi cha Yehova—Gawo 2.” Kambani mawu oyamba kwa nthaŵi yosakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 2 mpaka 6, pemphani anthu pampingopo kusimba zinthu zimene zinawachitikira polimbikitsa ovutika maganizo kapena odandaula chifukwa cha masoka amene achitika posachedwapa ndi zotsatirapo zake. Konzeranitu kuti munthu m’modzi kapena aŵiri adzachite chitsanzo cha zomwe zinachitikazo.
Nyimbo Na. 222 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 17
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Malipoti a maakaunti. Lengezani pulogalamu yopita mu utumiki wakumunda pa December 25 ndi January 1.
Mph. 22: “Lunjikani Nawo Bwino Mawu a Mulungu.” Kambani mawu oyamba kwa nthaŵi yosakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo chitsanzo cha zimene mungachitedi pa ulaliki wa m’ndime 4. Komanso, chitani chitsanzo cha ulaliki wabwino umene anthu akhala akuugwiritsa ntchito m’gawolo polimbikitsa kapena kusangalatsa anthu amene akuvutika maganizo chifukwa cha zinthu zimene zikuchitika m’dziko. Angasimbe mwachidule zimene zawachitikira. Ndiyeno, pemphani omvetsera kufotokoza chifukwa chake akuona kuti kugwiritsa ntchito Baibulo kungachititse zimene akulalikira kukhala zogwira mtima kwambiri.
Mph. 13: ‘Kulalikira Uthenga Wabwino—Monga Banja.’ Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime zonse.
Nyimbo Na. 225 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 24
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Fotokozani mabuku odzagaŵira mu January ndi mabuku amene mpingo uli nawo.
Mph. 10: “Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2002.” Woyang’anira sukulu akambe nkhaniyi. Limbikitsani onse kuchita khama kuti azikwaniritsa mbali zawo.
Mph. 25: Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho nkhani yakuti “Kuchitira Ana Zabwino.” Funsani makolo amene alera ana m’choonadi kapena amene akupereka chitsanzo chabwino pothandiza ana awo mwauzimu. Afunseni momwe amagaŵira nthaŵi ya phunziro, utumiki, kucheza ndi kusangalala; ndi zinthu zimene aona kuti zimagwira ntchito pothandiza ana awo kukhala ndi malingaliro abwino pa za sukulu zakudziko, phunziro la Baibulo laumwini, utumiki wakumunda, kugwira ntchito za panyumba, ndi zina zotero.
Nyimbo Na. 24 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 31
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Mogwiritsa ntchito malingaliro a patsamba 8, sonyezani zitsanzo za ulaliki wothandiza mmene tingagaŵire (1) Nsanja ya Olonda ya December 15 ndiponso (2) mmene tingagaŵire Galamukani! ya December 8. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a December. Ngati mpingo wanu udzasintha nthaŵi ya misonkhano chaka chikubwerachi, limbikitsani onse mokoma mtima kuti azidzapezeka kumisonkhano mokhazikika pa nthaŵi zatsopanozi. Tsimikizirani kuti anthu achidwi onse ndi aliyense amene anazilala adziŵe za kusinthaku.
Mph. 15: Apatseni Akulu Ulemu Wowayenera. Atumiki otumikira aŵiri kapena atatu akambirane Nsanja ya Olonda ya June 1, 1999, patsamba 18 mpaka 19. Atchulepo ntchito zambiri zimene akulu amagwira, kuphatikizapo ntchito yolembedwa, udindo wabanja, ndi ntchito zaumulungu. Pendani njira zina zomwe aliyense angalimbikitsire akulu, kuwachepetsera ntchito yawo, ndi kutsatira malangizo awo. Atumiki otumikirawo avomereze kuti akulu akuchita utumiki wofunika kwambiri ndipo ndi ofunika “ulemu woposatu.”—1 Ates. 5:12, 13.
Mph. 15: Bokosi la Mafunso. Nkhaniyi ikambidwe ndi woyang’anira wotsogolera.
Nyimbo Na. 219 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 7
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Sonyezani zitsanzo ziŵiri zachidule za mmene mungachitire ulaliki wa magazini pogwiritsa ntchito malingaliro a patsamba 8. M’chitsanzo chimodzi gwiritsani ntchito Nsanja ya Olonda ya January 1, ndipo pa chitsanzo chinacho gwiritsani ntchito Galamukani! ya December 8. Chitsanzo chimodzi achite wachinyamata.
Mph. 20: Khalani ndi Moyo Wopindulitsa. Banja likambirane Nsanja ya Olonda ya August 15, 1998, masamba 8-9. Bambo akufuna kuti banjalo lichite zinthu zimene zingawapatse chimwemwe osati nkhaŵa. Aone malangizo a m’Malemba omwe ali mu nkhaniyi amene akusonyeza momwe angapezere chimwemwe, kuona kufunika kochita zinthu mozindikira, kuchita kaye zinthu zofunika, ndi kudalira Yehova. Anene malingaliro othandiza a mmene banjalo lingasinthire zimene limachita.
Mph. 15: Kusamalira Nyumba Yathu ya Ufumu. Mkulu akambe nkhaniyi. Onani momwe Nyumba ya Ufumuyo ikuonekera. Kodi pakonzedwa zotani zodzakonza m’holomo Chikumbutso chisanachitike? Ndi zinthu zotani m’holoyo zofunika kukonzeratu? Fotokozani momwe mpingo ungathandizire pa ntchitoyo. Gogomezerani kuti m’pofunika kuonetsetsa kuti malo athu olambirira ndi okongola ndiponso opereka ulemu monga nyumba ya Yehova.—Sal. 84:1.
Nyimbo Na. 126 ndi pemphero lomaliza.