Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira March 11
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Muphatikizeponso “Ndandanda ya Misonkhano Yachigawo ya 2002.”
Mph. 15: Kusaloŵerera m’Zandale Monga Akristu. Nkhani yokambidwa ndi mkulu waluso. Khalidwe lokonda dziko lako lafalikira kwambiri kusukulu, kuntchito ndiponso m’madera amene tikukhala. Ambiri amene akulimbikitsa zimenezi akutero pofuna kuthana ndi nkhaŵa ndi chisoni zimene masoka ochitika m’dziko lawo abweretsa. Ngakhale kuti tikumvanso chisoni ndi zimene zikuchitika m’dziko, timazindikira nkhani yaikulu yokhudza ulamuliro wa chilengedwe chonse ndipo uthenga wa Ufumu umatilimbitsa mtima. Pamene tikuuza ena chifukwa chimene sitiloŵera m’zochitika za dziko, tiziwauzanso uthenga wolimbikitsa ndi wopatsa chiyembekezo umene tapeza m’Mawu a Mulungu. Bulosha lakuti Mboni za Yehova ndi Maphunziro, patsamba 20-4, pa kamutu kakuti “Kuchitira Mbendera Suluti,” limafotokoza chifukwa chake sitichita nawo miyambo yokondwerera dziko lathu. Kambiranani mfundo zazikulu, ndipo limbikitsani makolo kuphunzira nkhani imeneyi mosamalitsa ndi ana awo. Simbani chokumana nacho cha patsamba 20 m’buloshali ndiponso mu Galamukani! yachingelezi ya January 8, 1996, patsamba 31. Nenani motsindika kufunika kolambira Yehova yekha basi, kwinaku tikulemekeza ulamuliro wa boma.
Mph. 20: “Khalani Ochuluka mu Ntchito Zabwino.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Limbikitsani anthu onse kuchita utumiki mokwanira pokonzekera Chikumbutso pa March 28. Fotokozani momwe tingagwiritsire ntchito mwanzeru timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso. Pemphani ofalitsa kunena zimene anachita kuti athe kubwera ndi achibale, anansi, ophunzira Baibulo, ndi anthu ena achidwi ku Chikumbutso chaka chatha ndiponso anene zosangalatsa zimene zinatsatirapo. Limbikitsani onse amene angathe kuchita upainiya mu April kuti atenge mafomu msonkhano uno ukatha.
Nyimbo Na. 82 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 18
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kambiranani “Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso.” Limbikitsani onse kutsatira ndandanda yoŵerenga Baibulo ya Chikumbutso kuyambira pa March 23 mpaka pa March 28, monga alembera m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2002.
Mph. 15: “Osangalala Pogwirizana ndi Yehova Komanso Mwana Wake.” Nkhani yolimbikitsa ya m’Malemba. Ikambidwe ndi mkulu. Limbikitsani onse kuti kuyambira lero mpaka pa March 28 ayesetse kuitanira anthu ambiri kudzachita nafe Chikumbutso.
Mph. 20: “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 45 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 25
Mph. 14: Zilengezo za pampingo. Fotokozani kuti nthaŵi ikalipo yakuti aliyense amene akufuna kuchita upainiya wothandiza mu April apereke fomu yofunsira upainiya. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo ziŵiri za ulaliki za mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya March 15 ndi Galamukani! ya April 8. M’zitsanzo zonsezi, sonyezani njira zosiyana za mmene tingachitire munthu akanena mawu otsekereza kukambirana monga akuti, “Sindikufuna.”—Onani buku la Kukambitsirana, patsamba 16.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 16: Gwiritsani Ntchito Buku la Kukambitsirana Polimbikitsa Ena. Kukambirana ndi omvetsera. Tonse nthaŵi zina timafuna kutilimbikitsa mwachikondi. Choncho, tonse tiziona kufunika ‘kolimbikitsa amantha mtima,’ ndiponso ovutika maganizo amene timakumana nawo mu utumiki. (1 Ates. 5:14) Mwa kugwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana, pemphani omvetsera kutchula Malemba olimbikitsa amene angauze munthu amene akuvutika ndi china mwa zimene atchula pa masamba 79-82. Nenani kuti onse azilimbikitsa ena pomwe akufunika chilimbikitso.—Agal. 6:10.
Nyimbo Na. 131 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 1
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a March. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zili patsamba 8, wachikulire asonyeze momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya April 1 ndipo wachinyamata asonyeze momwe tingagaŵire Galamukani! ya April 8. Pambuyo pa chitsanzo chilichonse nenani mbali zabwino za ulalikiwo
Mph. 15: “‘Mphatso mwa Amuna’ Zimaŵeta Gulu la Mulungu Mokondwa.” Ikambidwe ndi mkulu. Kambiranani malemba amene aperekedwawo. Tchulani zabwino zimene zimakhalapo ngati akulu achita ubusa kwa aja osagwira ntchito ndi kuthandiza okalamba. Abusa achikondi amayamikira zonse zimene gulu la nkhosa limachita kuti likhalebe la changu mu utumiki wa Yehova.
Mph. 20: “Onjezani Chimwemwe Chanu Polalikira.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 5, afunseni anene mfundo zimene zingatithandize kukhala ogwira mtima polalikira m’deralo. Sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri za momwe tingayambire kulankhula ndi munthu ndi cholinga chomulalikira mwachidule. Limbikitsani onse kuti mlungu uno apeze mpata wolalikira.
Nyimbo Na. 15 ndi pemphero lomaliza.