Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/02 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 3/02 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo. April ndi May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ofalitsa aziuza eninyumba kuti apereke kangachepe kuthandizira ntchito ya padziko lonse ngati akufuna kuthandiza. Mukapeza achidwi, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Ngati eninyumba ali nazo kale zofalitsa tatchulazi, gaŵirani bulosha loyenerera limene mpingo uli nalo.

◼ Ofalitsa amene akufuna kuchita upainiya wothandiza mu April ayambe lero kukonzekera ndipo apereke mwamsanga mafomu awo ofunsirapo upainiya. Zimenezi zidzathandiza akulu kukonza dongosolo la utumiki wakumunda komanso kupeza magazini ndi mabuku ena okwanira. Lengezani kumpingo mwezi uliwonse mayina a anthu amene avomerezedwa kuchita upainiya wothandiza.

◼ Chikumbutso chidzachitika Lachinayi, pa March 28, 2002. Ngati mpingo wanu umachita misonkhano Lachinayi, dzapangeni misonkhanoyo tsiku lina mlungu womwewo ngati Nyumba ya Ufumu sidzakhala ikugwira ntchito tsiku limenelo. Ngati zimenezi n’zosatheka ndipo zikukhudza Msonkhano wa Utumiki, nkhani zake zomwe zili zofunika kwambiri pampingo wanu mungaziphatikize mu Msonkhano wa Utumiki wotsatira.

◼ Ofesi ya nthambi siilembera wofalitsa oda ya mabuku amene akuwafuna. Woyang’anira wotsogolera azilengeza mwezi uliwonse asanatumize ku nthambi oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo kuti onse amene akufuna mabuku auze mbale woyang’anira za mabuku. Chonde, kumbukirani zofalitsa zimene zili za oda yapadera.

◼ N’kofunika kuti pamene anthu 20 kapena kuposerapo akukonza zopita ku kukaona ofesi ya nthambi aziyamba alembera kalata ku Ofesi ya Beteli, Watch Tower Society, Box 30749, Lilongwe 3. Tumizani chiŵerengero cha anthu amene akufuna kubwera, tsiku komanso nthaŵi yokafikira kumeneko. Musanapite ku maloŵa, ŵerengani Bokosi la Mafunso lonena za kavalidwe ndi kapesedwe popita kukaona nyumba za Beteli, mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 1998.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena