Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/02 tsamba 6
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 3/02 tsamba 6

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Pamene tili m’zaka zoyambirira za m’ma 2000, ndife osangalala kulemba kalata yokuthokozani inu, “gulu lonse la abale” padziko lonse lapansi, chifukwa chogwira ntchito molimbika. (1 Pet. 2:17, NW) Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Yesu anafunsa kuti: “Mwana wa munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?” (Luka 18:8) Kugwira kwanu ntchito molimbika m’chaka chautumiki chathachi, kwayankha funso la Yesu ndi mawu amphamvu akuti inde, adzapeza chikhulupiriro. Enanu mwachitidwa chipongwe ndi kunyozedwa chifukwa cha chikhulupiriro chanu. Mukupirira ngakhale kuti m’mayiko ambiri mukuchitika nkhondo, masoka, matenda, kapena njala. (Luka 21:10, 11) Chifukwa cha changu chanu pantchito zabwino, Yesu atha ‘kudzapeza chikhulupiriro padziko lapansi.’ Ndithudi kumwamba akusangalala ndi zimenezi.

Timadziŵa kuti kupirira n’kovuta. Talingalirani ziyeso za abale athu m’dziko lina la kumadzulo kwa Asia. M’dzikolo, n’kofala kwambiri kuchitira Mboni za Yehova chiwawa. Posachedwapa, apolisi anasokoneza msonkhano wabata wa anthu pafupifupi 700. Chifukwa cha malo a chipikisheni m’misewu, abale okwana 1,300 analephera kupezeka pamsonkhanowo. Gulu la anthu ovala zobisa nkhope, omwe ena mwa iwo anali apolisi, anafika pamalo amsonkhanowo, namenya anthu ambiri, ndi kuwotcha msasa umene ankafuna kuchitiramo msonkhanowo. Nthaŵi zina, anthu achipembedzo amenya abale athu mwankhanza ndi zibonga zokhomerera misomali.

Mazunzo oterewo ndi omvetsa chisoni kwambiri koma si achilendo. Mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” (2 Tim. 3:12) M’zaka za zana loyamba, Akristu anapirira kunyozedwa ndi kumenyedwa, ndipo ena anaphedwa kumene. (Mac. 5:40; 12:2; 16:22-24; 19:9) Zimenezi zinachitikanso m’ma 1900, ndipo mosakayikira zipitirira kuchitika m’zaka za m’ma 2000 zino. Komabe, Yehova akutiuza kuti: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula.” (Yes. 54:17) N’zolimbikitsatu kwambiri zimenezi! Zoona, ndife amtengo wapatali kwambiri kwa Yehova moti mwa mneneri wake Zakariya, iye anati: ‘Iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m’diso langa.’ (Zek. 2:8) Amene amadana ndi olambira Yehova sangapambane n’komwe. Kulambira koona kudzapambana.

Mwachitsanzo, m’dziko tatchula lija, ofalitsa a Mboni za Yehova anawonjezereka kaŵiri m’chaka chautumiki cha 2001. Inde, abale athu kumeneko, monga kwina kulikonse, akulimbikira mosasamala kanthu za mavuto. Padziko lonse m’chaka chautumiki chapitacho, mlungu uliwonse anthu 5,066 anali kubatizidwa posonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova. Panopa, atsopano ameneŵa pamodzi ndi ena tonse, talimba mtima ‘kuima amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.’—Akol. 4:12, NW.

Onaninso zimene zachitika posachedwapa ku Greece. Mosasamala kanthu kuti Tchalitchi cha Greek Orthodox chinali kutsutsa kwambiri, Mboni za Yehova tsopano n’zodziŵika ndi boma monga “chipembedzo chovomerezeka.” Kalata ya chilolezo chimenechi inapitiriza kunena kuti nyumba ya Beteli ku Greece ndi “malo opatulika ndi oyera, amene anawapatulira kuti agwire ntchito yolambirira Mulungu.” Tilinso osangalala kukuuzani kuti m’chaka chautumiki chathachi, makhoti agamula milandu yokhudza kulambira kwathu mokomera chipembedzo chathu ku Bulgaria, Canada, Germany, Japan, Romania, Russia, ndi United States. Tikuthokoza kwambiri Yehova posiya khomo la ntchito lili lotsegula m’mayiko ameneŵa.

Pamene tikuona njira zimene Yehova amathandizira anthu ake m’masiku otsiriza ano, timaona kuti iye ndi bwenzi lapamtima loposa onse amene tingakhale nawo. Timasangalala kuti ndi bwenzi lathu, podziŵa kuti amatikonda, amatiphunzitsa ndiponso amatidzudzula. Inde, tipitiriza kukumana ndi ziyeso za chikhulupiriro. Koma kukhulupirira Yehova zolimba kudzatithandiza. Yakobo analemba kuti: “Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, mmene mukugwa m’mayesero a mitundumitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.” (Yak. 1:2, 3) Komanso, kupirira kwathu kumasonyeza kuti timakonda Yehova, ndipo zimenezi zimatibweretsera chimwemwe chochuluka. Abale okondeka, khalani otsimikiza kuti Yehova adzathandiza aliyense wa ife. Ngati tikhalabe okhulupirika, ndithudi adzatithandiza kuti tikafike m’dziko latsopano. N’zimene iye akufuna.

Chotero, tikukulimbikitsani abale ndi alongo, achinyamata ndi achikulire, kukumbukira madalitso abwino kwambiri amene ali patsogolo pathu. Tiyeni tikhale ndi maganizo ofanana ndi a mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.” (Aroma 8:18) Kaya mukumane ndi mavuto a mtundu wanji, dalirani Yehova. Pirirani, ndipo musasiye. Simudzadandaula m’pang’ono pomwe. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.”—Hab. 2:4.

Ndife Abale Anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena