Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/02 tsamba 8
  • Onjezani Chimwemwe Chanu Polalikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Onjezani Chimwemwe Chanu Polalikira
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Tumikirani Yehova Mokondwera’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Anthu Achimwemwe—Nchifukwa Ninji?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Chimwemwe Ndi Khalidwe Limene Mulungu Amapereka
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Tumikirani Yehova ndi Chimwemwe cha Mtima
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 3/02 tsamba 8

Onjezani Chimwemwe Chanu Polalikira

1 Kodi polalikira mukupeza chimwemwe chifukwa chouza ena uthenga wabwino? Tikapanda kusamala, dziko loipali litha kutipatsa mantha olalikira ndi kutitayitsa chimwemwe chathu. Tingagwe ulesi chifukwa cholalikira m’gawo limene sitikuphulamo kanthu. Kodi ndi njira zothandiza ziti zimene tingatsatire kuti tiwonjeze chimwemwe chathu polalikira?

2 Khalani ndi Maganizo Abwino: Kukhala ndi maganizo abwino kumathandiza zedi. Kusinkhasinkha mwayi waukulu umene tili nawo wokhala “antchito anzake a Mulungu” ndi njira imodzi yochitira zimenezi. (1 Akor. 3:9) Ntchitoyi tikugwiranso ndi Yesu. (Mat. 28:20) Ndipo amatithandizanso mwa kutipatsa khamu la angelo. (Mat. 13:41, 49) Choncho, tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu ndi amene akutsogolera ntchito yathu. (Chiv. 14:6, 7) Ndipo kaya ena amatani nayo ntchito yathu, kumwamba amasangalala nayo kwambiri!

3 Konzekerani Bwino: Kukonzekera bwino kumawonjezeranso chimwemwe chathu. Kukonzekera ulaliki sikufunika kukhala chintchito. Kuona mfundo zimene mungakakambe za m’magazini atsopano kapena m’mabuku ofunika kugaŵira mwezi umenewo, kumatenga mphindi zochepa zokha. Sankhani ulaliki pa “Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini,” mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Onani mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002, pamutu wakuti “Maulaliki Amene Mungagwiritse Ntchito mu Utumiki wa Kumunda,” kapena onani mawu oyamba ogwira mtima mu buku la Kukambitsirana. Ngati mumalephera kupitiriza kukambirana chifukwa cha mawu otsutsa amene eninyumba amakonda kunena, konzekerani yankho losatsutsa ndemanga yawo koma loyambitsa nkhani ina yochititsa chidwi. Buku la Kukambitsirana limathandiza kwambiri kuchita zimenezi. Tikagwiritsa ntchito zida zimenezi tidzalimba mtima ndipo tidzakhala ndi chimwemwe polalikira.

4 Pempherani ndi Mtima Wonse: Kuti tipeze chimwemwe chokhalitsa, tifunika kupemphera. Popeza tikuchita ntchito ya Yehova, tifunika kumupempha kuti atipatse mzimu wake, umene chipatso chake china ndi chimwemwe. (Agal. 5:22) Yehova adzatipatsa mphamvu kuti tipitirize kulalikira. (Afil. 4:13) Kupempherera utumiki wathu kungatithandize kulingalira bwino pamene takumana ndi zokhumudwitsa. (Mac. 13:52; 1 Pet. 4:13, 14) Ngati tikuchita mantha, pemphero lingatithandize kupitiriza molimba mtima ndi mosangalala.—Mac. 4:31.

5 Pezani Mipata: Ndi zoona kuti utumiki wathu umasangalatsa kwambiri tikamapeza anthu ndi kuwalalikira. Kusintha ndandanda yanu ndi cholinga chofuna kupita ku ulaliki wa kunyumba ndi nyumba nthaŵi ina, monga masana ndithu kapena kutangoyamba kumene kuda, kungakhale ndi zotsatira zabwino kwambiri. Nthaŵi zonse mukamayenda pamsewu, mukapita kokagula zinthu, kapena mukakwera basi mumakumana ndi anthu. Bwanji osakonza mawu achidule amene mungayambire kukambirana ndi anthu amene akuoneka kuti ndi ochezeka? Kapena n’kutheka kuti muli pantchito kapena pasukulu, kumene tsiku lililonse mumalankhula ndi anthu. Mungapeze mpata wolalikira mwa kungoyambitsa nkhani ya m’Malemba yochititsa chidwi. Mfundo zabwino za mmene mungachitire zimenezi zikupezeka patsamba loyamba la mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002. Mukachita zilizonse mwa zinthu zimenezi, chimwemwe chanu polalikira chidzawonjezeka.

6 Tifunika kukhala ndi chimwemwe chifukwa chimatithandiza kupirira. Tikatero tidzapeza mphoto yaikulu ntchito imeneyi imene sidzachitikanso ikadzatha. Kungodziŵa zimenezi kungawonjeze chimwemwe chathu polalikira.—Mat. 25:21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena