Khalani ndi Zolinga Zauzimu
1 Udzakhala mwayi zedi kutamanda Yehova kwamuyaya! Kuti tithe kudzapeza mwayi umenewu, tingakhale ndi zolinga zauzimu zomwe tingathe kuzichita panopo nthaŵiyo isanafike ndiyeno n’kuyesetsa kuzikwaniritsa. Kuchita zimenezi kumatithandiza kugwiritsa ntchito mphamvu zathu mwanzeru. (1 Akor. 9:26) Kodi ndi zolinga ziti zimene mungakwanitse?
2 Kuphunzira Baibulo: Kodi mumakonzekera msonkhano wa mpingo uliwonse? Ngati mumakonzekera, kodi mumakhala ndi nthaŵi yofufuza ndi yosinkhasinkha pokonzekerapo? Mwachitsanzo, pokonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda ndiponso Phunziro la Buku la Mpingo la mlungu uliwonse, kodi mumangodula mizere kunsi kwa mayankho, kapena mumaŵerenganso malemba amene sanagwidwe mawu ndiponso kuganizira zifukwa zake nkhaniyo aifotokoza motero? Kodi mungakhale ndi cholinga chofufuza mfundo zingapo mlungu uliwonse kuchokera m’kuŵerenga Baibulo kwa mu Sukulu ya Utumiki wa Teokalase? Kufufuza zinthu zauzimu koteroko kumafuna nthaŵi ndiponso khama, koma n’kopindulitsa kwambiri.—Miy. 2:4, 5.
3 Misonkhano ya Mpingo: Cholinga china chingakhale chofika nthaŵi zonse pa misonkhano isanu yonse ya mpingo. Kufika mofulumira kuti ticheze ndi okhulupirira anzathu komanso kuti tiimbe nawo nyimbo yotsegulira ndi kupemphera nawo, kumalimbitsa mpingo. Tingayesetsenso kuti tiziyankha pa msonkhano uliwonse ndiponso kuyesetsa kukonza ndemanga zathu kuti zizikhala zabwino kwambiri. Mwina mungasonyeze kugwirizana kwa lemba la pandimepo ndi nkhani mukukambiranayo kapena mungatchule momwe tingagwiritsire ntchito zimene tikuphunzirazo pa moyo wa tsiku ndi tsiku.—Aheb. 10:24, 25.
4 Utumiki Wakumunda: Utumiki wathu umakhala wabwino zedi tikakhala ndi zolinga. Kodi munakonza chiŵerengero cha maola amene mumafuna kuthera mu utumiki mwezi uliwonse? Ena aona kuti kuchita zimenezi n’kothandiza. Kapena kodi mungawongolere mbali zina za utumiki wanu, monga kugwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba, kupanga maulendo obwereza ogwira mtima kwambiri, kuyesetsa kuyambitsa phunziro la Baibulo, kapena kuphunzitsa zomveka kwambiri pa maphunziro?
5 Makolo, kodi mukulimbikitsa ana anu kukhala ndi zolinga potumikira Yehova? Athandizeni kuona kuti kukhala mpainiya kapena pabanja la Beteli ndi njira yabwino kwambiri yosonyezera kuti amam’thokoza kwambiri Yehova.—Mlal. 12:1.
6 Pamene tipenda zochita zathu, kukhala ndi zolinga zauzimu, ndi kuyesetsa kuzikwaniritsa, tidzapeza chimwemwe chochuluka mu utumiki wathu ndiponso tidzalimbikitsa ena.—Aroma 1:12.