Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. November: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?, kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Ngati anthu ali nawo kale mabuku ameneŵa, mungagaŵire ena alionse. Ngati mpingo wanu ulibe mabuku alionse mukhoza kukafufuza kumipingo imene mwayandikana nayo ngati ili nawo mabuku akale ochuluka. December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati palibe mungagaŵire Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kapena Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Ngati mpingo ulibe mabuku tatchulaŵa, chonde kafufuzeni kumipingo imene mwayandikana nayo ngati ili nawo ochuluka oti ingakupatseni kuti mugwiritse ntchito. January: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
◼ Mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu uno ndi “Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2003,” isungeni kuti mudzaigwiritse ntchito chaka chonse cha 2003.
◼ Abale ndi alongo akumbutsidwe momwe ayenera kugwiritsira ntchito mabuku athu moyenera. “Zinthu Zaoda Yapadera,” monga Mabaibulo a Chicheŵa ndi a Chitumbuka sayenera kuzigaŵira mu utumiki wathu wanthaŵi zonse, wakunyumba ndi nyumba. Zimenezi amatumizira ofalitsa ndi ana awo okha basi kudzera ku mpingo. Tiyeneranso kuyamba talankhula kaye ndi anthu kuti tione ngati ali ndi chidwi, tisanawagaŵire buku, magazini kapena thirakiti. Ngakhale kuti si koyenera kuti anthu azipereka kaye chopereka kuti atenge mabuku, tizikumbukira kuwauza bwinobwino makonzedwe a chopereka, kuti ngati angathe kupereka chopereka apereke. Kuti mumve zambiri pankhani ya momwe tingagwiritsire ntchito bwino mabuku athu ndiponso momwe tinganenere za makonzedwe a chopereka, onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa January ndi May 2000 ndiponso wa May 2001.
◼ Chaka chino mpingo uliwonse tiutumizira chikwangwani cha Lemba la Chaka cha 2003. Sosaite imawononga ndalama pafupifupi K50.00, kuti isindikize ndi kutumiza lemba la chakali. Muyenera kukumbukira zimenezi potumiza chopereka chanu ku ofesi ya nthambi. Mipingo idzalandira zikwangwani zimenezi chakumapeto kwa chaka chino. Ngati n’kotheka, ndi bwino kudzakhoma chikwangwanichi pa January 1, 2003.