Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2003
Malangizo
Dongosolo lotsatirali ndilo lidzagwiritsidwe ntchito pochititsa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu mu 2003.
MABUKU OPHUNZIRA: Revised Nyanja (Union) Version [bi53-CN], Nsanja ya Olonda [w-CN], Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu [be-CN], Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako [gt-CN], ndi Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN].
Sukulu iyenera kuyamba PANTHAŴI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje, ndiyeno n’kupitirira motere:
LUSO LA KULANKHULA: Mphindi 5. Woyang’anira sukulu, mlangizi wothandiza, kapena mkulu wina woyenerera adzafotokoza luso la kulankhula kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki. (Mipingo imene ili ndi akulu ochepa, ingagwiritse ntchito mtumiki wotumikira woyenerera.) Fotokozaninso zimene zili m’mabokosi amene ali m’nkhani imene yaperekedwayo ngati sitinanene kuti musafotokoze. Musaphatikizepo mbali ya zochita. Mbali imeneyi kwenikweni ndi yoti munthu aziigwiritsa ntchito payekha ndiponso popereka malangizo am’seri.
NKHANI NA. 1: Mphindi 10. Mkulu kapena mtumiki wotumikira ndi amene ayenera kukamba nkhani imeneyi, ndipo izitengedwa mu Nsanja ya Olonda, m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kapena m’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Imeneyi ndi nkhani yolangiza imene ayenera kuikamba kwa mphindi khumi popanda mafunso obwereza. Cholinga chake sichiyenera kukhala kungokamba nkhaniyo koma kusonyeza phindu la mfundo zimene akufotokoza, ndi kutsindika mfundo zomwe zidzathandiza kwambiri mpingowo. Agwiritse ntchito mutu wosonyezedwa. Abale amene apatsidwa nkhani imeneyi azionetsetsa kuti akusunga nthaŵi. Malangizo am’seri angaperekedwe ngati pakufunika kutero.
MFUNDO ZAZIKULU ZA KUŴERENGA BAIBULO: Mphindi 10. Mkulu kapena mtumiki wotumikira woyenerera afotokoze kwa mphindi zisanu ndi imodzi zoyambirira mfundo za kuŵerenga Baibuloku zimene zingathandize pa zofunika za mpingowo. Angafotokoze mbali ina iliyonse ya chigawo cha kuŵerenga Baibulo cha mlunguwo, popeza mbale amene adzakamba nkhani Na. 2 sadzafotokozera mavesi amene iye adzaŵerenga. Isakhale chidule chabe cha gawo loŵerenga mlunguwo. Cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvera kuzindikira chifukwa chake komanso mmene mfundozo zilili zaphindu. Ndiyeno akatero, wokamba nkhaniyo adzapempha omvera kulankhulapo kwa mphindi zinayi mwa kufotokoza mfundo zachidule (kwa masekondi 30 kapena kucheperapo) pa mafunso aŵiri otsatiraŵa: “Kodi n’chiyani mwapeza pa kuŵerenga Baibulo kwa mlungu uno chimene chingakupindulitseni muutumiki wanu kapena pa moyo wanu?” ndiponso “N’chiyani chalimbitsa chikhulupiriro chanu ndi kukulitsa kuyamikira kwanu Yehova?” Ndiyeno woyang’anira sukulu apemphe ophunzira amene ali m’makalasi ena kupita ku makalasi awo.
NKHANI NA. 2: Mphindi 4. Iyi ndi nkhani yoti mbale aŵerenge. Nthaŵi zambiri aziŵerenga m’Baibulo. Koma kamodzi pamwezi, wopatsidwa nkhaniyi adzaŵerenga nkhani ya mu Nsanja ya Olonda. Wophunzira aŵerenge nkhani imene wapatsidwa popanda kukamba mawu oyamba kapena omaliza. Kutalika kwa nkhani yoŵerenga kuzisiyana pang’ono mlungu uliwonse koma ayenera kuŵerenga mphindi zinayi kapena kucheperapo. Woyang’anira sukulu aziona nkhaniyo asanagaŵire munthu, kuti pogaŵa aigwirizanitse ndi misinkhu ndiponso luso la ophunzira. Woyang’anira sukulu makamaka adzaonetsetsa kuti akuthandiza wophunzira kumvetsa zimene akuŵerengazo, kuŵerenga mosadodoma, kutsindika ganizo moyenera, kusinthasintha mawu, kupuma moyenera, ndiponso kuŵerenga mwachibadwa.
NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhani imeneyi azikamba ndi mlongo. Wophunzira amene wapatsidwa nkhani imeneyi azisankha yekha kapena azipatsidwa mtundu wa makambirano kuchokera pa mndandanda umene uli pa tsamba 82 m’buku la Sukulu ya Utumiki. Wophunzira agwiritse ntchito mutu wa nkhani umene wapatsidwa ndipo agwirizanitse ndi mbali ya utumiki wa kumunda yomwe ndi yotheka ndiponso yothandiza m’gawo la mpingowo. Ngati sitinasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhani imeneyi mwa kufufuza m’zofalitsa za gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Ophunzira atsopano azipatsidwa nkhani zimene tasonyeza buku limene nkhaniyo yachokera. Woyang’anira sukulu adzaonetsetsa makamaka mmene wophunzira akufotokozera nkhaniyo ndiponso mmene akuthandizira mwininyumba kulingalira pa Malemba ndi kumvetsa mfundo zazikulu za nkhaniyo. Ophunzira amene angapatsidwe nkhani imeneyi ayenera kukhala odziŵa kuŵerenga. Woyang’anira sukulu adzasankha wothandiza mmodzi.
NKHANI NA. 4: Mphindi 5. Wophunzira akambe nkhani ya mutu umene wapatsidwa. Ngati sitinasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhaniyi mwa kufufuza m’zofalitsa za gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Akapatsidwa mbale, aziikamba ngati nkhani ndipo akumbukire kuti omvera ake ndi anthu amene asonkhana m’Nyumba ya Ufumuyo. Mlongo akapatsidwa nkhani imeneyi, nthaŵi zonse aziikamba mofanana ndi Nkhani Na. 3. Onetsetsani kuti nkhani imene ili ndi nyenyezi iziperekedwa kwa mbale basi kuti aikambe ngati nkhani.
KUSUNGA NTHAŴI: Nkhani iliyonse isadye nthaŵi. Chimodzimodzinso ndi ndemanga za mlangizi. Nkhani Na. 2 mpaka Na. 4 ziziimitsidwa mwaluso nthaŵi yake ikatha. Ngati abale amene akamba nkhani yotsegulira ya luso la kulankhula, Nkhani Na. 1, kapena mfundo zazikulu za kuŵerenga Baibulo adya nthaŵi, azilangizidwa m’seri. Aliyense ayenera kusamala kwambiri nthaŵi. Pulogalamu yonse izitenga mphindi 45, osaphatikizapo nthaŵi ya nyimbo ndi pemphero.
MALANGIZO: Mphindi 1. Wophunzira aliyense akamaliza nkhani yake, woyang’anira sukulu adzanena mfundo zolimbikitsa za mbali ya nkhaniyo zimene wophunzirayo wachita bwino. Asapitirire mphindi imodzi pofotokoza zimenezi. Cholinga chake sindicho kungonena kuti “mwachita bwino” koma kutchula zifukwa zenizeni zimene mbali za nkhaniyo zimene watchulazo zinali zogwira mtima. Malinga ndi zimene wophunzira aliyense akufunikira, malangizo ena othandiza angaperekedwe m’seri misonkhano itatha kapena panthaŵi ina.
MLANGIZI WOTHANDIZA: Bungwe la akulu lingasankhe mkulu waluso, ngati alipo, kuphatikiza pa woyang’anira sukulu, kuti akhale mlangizi wothandiza. Udindo wake udzakhala wopereka malangizo am’seri, ngati angafunike, kwa abale amene akamba Nkhani Na. 1 ndi mfundo zazikulu za Baibulo. N’kosafunika kuti azipereka malangizo kwa mkulu mnzake aliyense kapena mtumiki wotumikira aliyense akakamba nkhani zimenezi. Dongosolo limeneli ligwira ntchito mu 2003 ndipo mwina lingasinthidwe m’tsogolo.
FOMU YOLANGIZIRA: Ili m’buku momwemo.
KUBWEREZA KWA PAKAMWA: Mphindi 30. M’miyezi iŵiri iliyonse, woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza kwa pakamwa. Kudzatsatira pambuyo pa kukambirana luso la kulankhula ndi mfundo zazikulu za kuŵerenga Baibulo monga mmene tafotokozera kale. Kubwereza kwa pakamwaku kudzakhala kwa nkhani zimene zinakambidwa m’sukulu m’miyezi iŵiri yapita, kuphatikizapo mlungu wa kubwerezaku.
NDANDANDA
Jan. 6 Kuŵerenga Baibulo: Mateyu 1- 6 Nyimbo Na. 91
Luso la Kulankhula: Takulandirani ku Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (be-CN tsa. 5 ndime 1–tsa. 8 ndime 1)
Na. 1: Kondwerani ndi Mawu a Mulungu (be-CN tsa. 9 ndime 1–tsa. 10 ndime 1)
Na. 2: Mateyu 4:1-22
Na. 3: Kodi Chizindikiro cha Masiku Otsiriza Chimakhudza Bwanji Akristu Oona? (rs-CN tsa. 265 ndime 2-3)
Na. 4: Kodi Yesu Akuchita Chiyani Pakalipano?
Jan. 13 Kuŵerenga Baibulo: Mateyu 7-11 Nyimbo Na. 40
Luso la Kulankhula: Ŵerengani Baibulo Tsiku ndi Tsiku (be-CN tsa. 10 ndime 2−tsa. 12 ndime 3)
Na. 1: “Motero Thamangani” (w01-CN 1/1 mas. 28-31)
Na. 2: Mateyu 9:9-31
Na. 3: Chifukwa Chake Timalalikira kwa Ena
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Zimati Masiku Otsiriza Anayamba mu 1914? (rs-CN tsa. 266 ndime 2–tsa. 267 ndime 1)
Jan. 20 Kuŵerenga Baibulo: Mateyu 12-15 Nyimbo Na. 133
Luso la Kulankhula: Kuŵerenga Molondola (be-CN tsa. 83 ndime 1-5)
Na. 1: Mungathe Kupitirizabe Polefulidwa! (w01-CN 2/1 mas. 20-3)
Na. 2: Mateyu 13:1-23
Na. 3: Kodi Alipo Adzakhala Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Dongosolo Ladziko Lilipoli Likadzatha? (rs-CN tsa. 267 ndime 2–tsa. 268 ndime 1)
Na. 4: Kodi Mulungu Amasinthasintha?
Jan. 27 Kuŵerenga Baibulo: Mateyu 16-21 Nyimbo Na. 129
Luso la Kulankhula: Mmene Mungaŵerengere Molondola (be-CN tsa. 84 ndime 1–tsa. 85 ndime 3)
Na. 1: Phunziro m’Chifundo (gt-CN mutu 40)
Na. 2: w01-CN 1/15 tsa. 20 ndime 20–tsa. 21 ndime 24
Na. 3: Kodi N’chiyani Chidzagwirizanitsa Anthu M’dziko Lapansi?
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Nthaŵi Yaitali Kupita Asanawononge Anthu Oipa? (rs-CN tsa. 268 ndime 2-4)
Feb. 3 Kuŵerenga Baibulo: Mateyu 22-25 Nyimbo Na. 139
Luso la Kulankhula: Kulankhula Momveka Bwino (be-CN tsa. 86 ndime 1-6)
Na. 1: “Yang’anirani Mamvedwe Anu” (be-CN tsa. 13 ndime 1–tsa. 14 ndime 5)
Na. 2: Mateyu 22:15-40
Na. 3: Mmene Tikudziŵira Kuti Chizindikiro cha Masiku Otsiriza Chikugwirizana ndi Nthaŵi Imene Tikukhala Ino (rs-CN tsa. 268 ndime 6–tsa. 269 ndime 2)
Na. 4: Kodi Ndani Alidi Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru?
Feb. 10 Kuŵerenga Baibulo: Mateyu 26-28 Nyimbo Na. 27
Luso la Kulankhula: Mmene Mungalankhulire Momveka Bwino (be-CN tsa. 87 ndime 1–tsa. 88 ndime 3)
Na. 1: Mmene Mungapezere Chimwemwe Chenicheni (w01-CN 3/1 mas. 4-7)
Na. 2: Mateyu 26:6-30
Na. 3: Chifukwa Chimene Sindigwiritsira Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo
Na. 4: Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani? (rs-CN tsa. 290 ndime 1–tsa. 291 ndime 1)
Feb. 17 Kuŵerenga Baibulo: Marko 1- 4 Nyimbo Na. 137
Luso la Kulankhula: Kutchula Mawu Molondola—Mfundo Zofunika Kuzidziŵa (be-CN tsa. 89 ndime 1–tsa. 90 ndime 3)
Na. 1: Yesu ndi Phata la Mkangano (gt-CN mutu 41)
Na. 2: w01-CN 2/15 tsa. 25 ndime 10–tsa. 26 ndime 14
Na. 3: Kodi Anthu Anawapanga Kuti Akhale ndi Moyo kwa Nthaŵi Yochepa Chabe Kenako Afe? (rs-CN tsa. 291 ndime 2-4)
Na. 4: Chifukwa Chake Kutchova Njuga N’kolakwika
Feb. 24 Kuŵerenga Baibulo: Marko 5-8 Nyimbo Na. 72
Luso la Kulankhula: Njira Zothetsera Vuto la Katchulidwe ka Mawu (be-CN tsa. 90 ndime 4–tsa. 92)
Kubwereza kwa Pakamwa
Mar. 3 Kuŵerenga Baibulo: Marko 9-12 Nyimbo Na. 195
Luso la Kulankhula: Kulankhula Mosadodoma (be-CN tsa. 93 ndime 1–tsa. 94 ndime 3)
Na. 1: Kumvetsera Nkhani, Pamakambirano, Pamisonkhano Ikuluikulu (be-CN tsa. 15 ndime 1–tsa. 16 ndime 5)
Na. 2: Marko 10:1-22
Na. 3: Mmene Tingapezere Mphamvu kwa Mulungu
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Tingayembekezere Kudzakhala ndi Moyo Kosatha? (rs-CN tsa. 292 ndime 7-9)
Mar. 10 Kuŵerenga Baibulo: Marko 13-16 Nyimbo Na. 187
Luso la Kulankhula: Mmene Mungathetsere Vuto la Kudodoma (be-CN tsa. 94 ndime 4–tsa. 96 ndime 2, kupatulapo bokosi limene lili pa tsa. 95)
Na. 1: Kodi Paradaiso Wauzimu N’chiyani? (w01-CN 3/1 mas. 8-11)
Na. 2: Marko 13:1-23
Na. 3: Kodi Ziyembekezo za Moyo wa M’tsogolo Zidzakwaniritsidwa Bwanji? (rs-CN tsa. 293 ndime 1-3)
Na. 4: Kodi Mulungu Amathandizira Gulu Lina la Nkhondo Likamamenyana ndi Linzake?
Mar. 17 Kuŵerenga Baibulo: Luka 1-3 Nyimbo Na. 13
Luso la Kulankhula: Kuthana ndi Chibwibwi (be-CN tsa. 95, bokosi)
Na. 1: “Wodala Munthu Wopeza Nzeru” (w01-CN 3/15 mas. 25-8)
Na. 2: Luka 3:1-22
Na. 3: Kodi N’koyenera Kulambira Yesu?
Na. 4: aKodi N’kofunika Kutsatira Malamulo a Boma Pokwatira? (rs-CN tsa. 383 ndime 1-4)
Mar. 24 Kuŵerenga Baibulo: Luka 4- 6 Nyimbo Na. 156
Luso la Kulankhula: Kupuma pa Zizindikiro Zopumira Ndiponso Posintha Ganizo (be-CN tsa. 97 ndime 1–tsa. 98 ndime 5)
Na. 1: Kodi Mumaona Kuti Anthu Sakumvetsetsani? (w01-CN 4/1 mas. 20-3)
Na. 2: Luka 6:1-23
Na. 3: Kodi Chikumbutso Chili ndi Tanthauzo Lotani? (rs-CN tsa. 70 ndime 3–tsa. 71 ndime 2)
Na. 4: Kodi Akristu Angayembekezere Mulungu Kuwatetezera?
Mar. 31 Kuŵerenga Baibulo: Luka 7-9 Nyimbo Na. 47
Luso la Kulankhula: Kupuma Kotsindika, Kupuma Komvetsera (be-CN tsa. 99 ndime 1–tsa. 100 ndime 3)
Na. 1: ‘Opani Mulungu Woona, Sungani Malamulo Ake’ (be-CN tsa. 272 ndime 1–tsa. 275 ndime 3)
Na. 2: w01-CN 3/15 tsa. 18 ndime 17–tsa. 19 ndime 20
Na. 3: Mmene Timadziŵira Kuti Baibulo Linachokera kwa Mulungu
Na. 4: Kodi Zizindikiro za Pachikumbutso Zimaimira Chiyani? (rs-CN tsa. 71 ndime 3–tsa. 72 ndime 1)
Apr. 7 Kuŵerenga Baibulo: Luka 10-12 Nyimbo Na. 68
Luso la Kulankhula: Kutsindika Ganizo Moyenerera (be-CN tsa. 101 ndime 1–tsa. 102 ndime 3)
Na. 1: ‘Kuchitira Umboni za Yesu’ (be-CN tsa. 275 ndime 4–tsa. 278 ndime 4)
Na. 2: Luka 10:1-22
Na. 3: Kodi Ndani Ayenera Kudya pa Mgonero wa Ambuye? (rs-CN tsa. 72 ndime 3-4)
Na. 4: Kodi Panali Mwambo Wotani pa Ukwati Woyambirira? (rs-CN tsa. 384 ndime 1-2)
Apr. 14 Kuŵerenga Baibulo: Luka 13-17 Nyimbo Na. 208
Luso la Kulankhula: Mmene Mungakulitsire Luso la Kutsindika Ganizo (be-CN tsa. 102 ndime 4–tsa. 104 ndime 3)
Na. 1: “Uthenga Uwu Wabwino Waufumu” (be-CN tsa. 279 ndime 1–tsa. 281 ndime 4)
Na. 2: Luka 15:11-32
Na. 3: Mmene Tingadzitetezere ku Ziwanda
Na. 4: Kodi Mwambo wa Chikumbutso Uyenera Kuchitika Kangati? (rs-CN tsa. 73 ndime 2–tsa. 74 ndime 1)
Apr. 21 Kuŵerenga Baibulo: Luka 18-21 Nyimbo Na. 23
Luso la Kulankhula: Kutsindika Malingaliro Ofunika Kwambiri (be-CN tsa. 105 ndime 1–tsa. 106 ndime 1)
Na. 1: Yesu Adzudzula Afarisi (gt-CN mutu 42)
Na. 2: w01-CN 4/15 tsa. 6 ndime 19–tsa. 7 ndime 22
Na. 3: Mmene Kuyembekezera Kuuka kwa Akufa Kumakhudzira Moyo Wathu
Na. 4: bKodi Baibulo Limavomereza Mitala? (rs-CN tsa. 384 ndime 3–tsa. 385 ndime 3)
Apr. 28 Kuŵerenga Baibulo: Luka 22-24 Nyimbo Na. 218
Luso la Kulankhula: Mphamvu ya Mawu Yoyenerera kwa Omvera Anu (be-CN tsa. 107 ndime 1–tsa. 108 ndime 4)
Kubwereza kwa Pakamwa
May 5 Kuŵerenga Baibulo: Yohane 1- 4 Nyimbo Na. 31
Luso la Kulankhula: Mmene Mungakulitsire Luso Lolankhula ndi Mphamvu Yoyenera (be-CN tsa. 108 ndime 5–tsa. 110 ndime 2)
Na. 1: Mukhoza Kunola Luso Lanu Lokumbukira Zinthu (be-CN tsa. 17 ndime 1–tsa. 19 ndime 1)
Na. 2: Yohane 2:1-25
Na. 3: Kodi Mulungu Amaletsa Kumwa Moŵa?
Na. 4: cKodi Mulungu Amakuona Bwanji Kupatukana? (rs-CN tsa. 385 ndime 4)
May 12 Kuŵerenga Baibulo: Yohane 5-7 Nyimbo Na. 150
Luso la Kulankhula: Sinthasinthani Mphamvu ya Mawu Anu (be-CN tsa. 111 ndime 1–tsa. 112 ndime 2)
Na. 1: Mungachite Moyenera Ngakhale Sanakulereni Bwino (w01-CN 4/15 mas. 25-8)
Na. 2: Yohane 5:1-24
Na. 3: Chifukwa Chake Chiphunzitso Chakuti Zimene Zimachitika Zinakonzedweratu N’chabodza
Na. 4: dKodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Kusudzulana ndi Kukwatiranso? (rs-CN tsa. 386 ndime 1-387 ndime 1)
May 19 Kuŵerenga Baibulo: Yohane 8-11 Nyimbo Na. 102
Luso la Kulankhula: Kusinthasintha Mawu—Sinthani Liŵiro Lanu (be-CN tsa. 112 ndime 3–tsa. 113 ndime 1)
Na. 1: ‘Ndi Nzeru Masiku Athu Adzachuluka’ (w01-CN 5/15 mas. 28-31)
Na. 2: Yohane 10:16-42
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kale Mulungu Ankalola Mwamuna Kukwatira Mlongo Wake? (rs-CN tsa. 387 ndime 2-3)
Na. 4: Zimene Tingachite Kuti Tithane ndi Nkhaŵa
May 26 Kuŵerenga Baibulo: Yohane 12-16 Nyimbo Na. 24
Luso la Kulankhula: Kusinthasintha Mawu—Siyanitsani Mamvekedwe a Mawu Anu (be-CN tsa. 113 ndime 2–tsa. 114 ndime 3)
Na. 1: Mafanizo Asanu Ali M’bwato (gt-CN mutu 43 ndime 1-8)
Na. 2: w01-CN 5/1 tsa. 14 ndime 4–tsa. 15 ndime 7
Na. 3: Kodi ‘Kusakhala Mbali ya Dziko’ Kumatanthauza Chiyani?
Na. 4: Kodi N’chiyani Chingathandize Kuwongolera Ukwati? (rs-CN tsa. 388 ndime 1-4)
June 2 Kuŵerenga Baibulo: Yohane 17-21 Nyimbo Na. 198
Luso la Kulankhula: Lankhulani ndi Mzimu wa Nkhaniyo (be-CN tsa. 115 ndime 1–tsa. 116 ndime 4)
Na. 1: Mmene Mzimu Woyera Umatithandizira Kukumbukira (be-CN tsa. 19 ndime 2–tsa. 20 ndime 3)
Na. 2: Yohane 20:1-23
Na. 3: Kodi N’chiyani Chingathandize Kuwongolera Ukwati? (rs-CN tsa. 388 ndime 5-8)
Na. 4: Kodi Chipembedzo Chiyenera Kukhala Cholinganizika?
June 9 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 1- 4 Nyimbo Na. 92
Luso la Kulankhula: Kulankhula Mwaumoyo Koyenerana ndi Nkhaniyo (be-CN tsa. 116 ndime 5–tsa. 117 ndime 4)
Na. 1: Limbikitsani Chikhulupiriro Chanu mwa Yehova (w01-CN 6/1 mas. 7-10)
Na. 2: Machitidwe 4:1-22
Na. 3: Kodi Tingaphunzire Chiyani pa Nkhani ya M’Baibulo ya Mariya? (rs-CN tsa. 254 ndime 2–tsa. 255 ndime 2)
Na. 4: Kodi Mulungu Zimamukhudza Mmene Timalambirira?
June 16 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 5-7 Nyimbo Na. 2
Luso la Kulankhula: Kusonyeza Mzimu Waubwenzi (be-CN tsa. 118 ndime 1–tsa. 119 ndime 5)
Na. 1: Kulapa Komwe Kumachiritsa (w01-CN 6/1 mas. 28-31)
Na. 2: Machitidwe 7:1-22
Na. 3: Mmene Mboni za Yehova Zimasiyanirana ndi Zipembedzo Zina
Na. 4: Kodi Mariya Analidi Namwali Pamene Anabala Yesu? (rs-CN tsa. 255 ndime 3-4)
June 23 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 8-10 Nyimbo Na. 116
Luso la Kulankhula: Kusonyeza Kukhudzika Mtima (be-CN tsa. 119 ndime 6–tsa. 120 ndime 5)
Na. 1: Samalirani Ana ndi Akazi Amasiye M’mayesero Awo (w01-CN 6/15 mas. 9-12)
Na. 2: w01-CN 6/1 tsa. 12 ndime 1–tsa. 13 ndime 5
Na. 3: Kodi Mariya Anali Namwali Nthaŵi Zonse? (rs-CN tsa. 255 ndime 5–tsa. 256 ndime 2)
Na. 4: eChifukwa Chake Kupezeka Pamisonkhano N’kofunika Kwambiri Kuti Munthu Akule Mwauzimu
June 30 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 11-14 Nyimbo Na. 167
Luso la Kulankhula: Kufunika kwa Manja ndi Nkhope Polankhula (be-CN tsa. 121 ndime 1-4)
Kubwereza kwa Pakamwa
July 7 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 15-17 Nyimbo Na. 38
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Manja ndi Nkhope Polankhula (be-CN tsa. 121 ndime 5–tsa. 123 ndime 2)
Na. 1: N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuchita Khama pa Kuŵerenga? (be-CN tsa. 21 ndime 1–tsa. 23 ndime 3)
Na. 2: Machitidwe 15:1-21
Na. 3: Mmene Timasonyezera Kuti Tili Kumbali ya Ulamuliro wa Mulungu
Na. 4: Kodi Mariya Anali Amayi a Mulungu? (rs-CN tsa. 256 ndime 3–tsa. 257 ndime 2)
July 14 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 18-21 Nyimbo Na. 32
Luso la Kulankhula: Kuyang’ana Omvera Muutumiki (be-CN tsa. 124 ndime 1–tsa. 125 ndime 4)
Na. 1: Musalole Kuti Kukayika Kuwononge Chikhulupiriro Chanu (w01-CN 7/1 mas. 18-21)
Na. 2: Machitidwe 19:1-22
Na. 3: fKodi Mariya Anabadwa Ali Wangwiro? (rs-CN tsa. 257 ndime 3–tsa. 258 ndime 1)
Na. 4: Tanthauzo la ‘Kupitiriza Kufunafuna Ufumu Choyamba’
July 21 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 22-25 Nyimbo Na. 222
Luso la Kulankhula: Kuyang’ana Omvera Pokamba Nkhani (be-CN tsa. 125 ndime 5–tsa. 127 ndime 1)
Na. 1: Kodi Mulidi Ololera? (w01-CN 7/15 mas. 21-3)
Na. 2: Machitidwe 24:1-23
Na. 3: Kodi Mdyerekezi Alipodi?
Na. 4: gKodi Mariya Anakwera Kumwamba ndi Thupi Lake Laumunthu? (rs-CN tsa. 258 ndime 2-3)
July 28 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 26-28 Nyimbo Na. 14
Luso la Kulankhula: Kulankhula Kwachibadwa Muutumiki (be-CN tsa. 128 ndime 1–tsa. 129 ndime 1)
Na. 1: Mmene Ophunzira Akupindulira ndi Zophunzitsa za Yesu (gt-CN mutu 43 ndime 9-19)
Na. 2: w01-CN 7/1 tsa. 14 ndime 5-8
Na. 3: Kodi N’koyenera Kupemphera kwa Mariya Monga Mtetezi? (rs-CN tsa. 258 ndime 4–tsa. 259 ndime 1)
Na. 4: Mmene Timasonyezera Kulemekeza Mphatso ya Moyo
Aug. 4 Kuŵerenga Baibulo: Aroma 1- 4 Nyimbo Na. 106
Luso la Kulankhula: Kulankhula Mwachibadwa Papulatifomu (be-CN tsa. 129 ndime 2–tsa. 130 ndime 1)
Na. 1: Mmene Mungachitire Khama pa Kuŵerenga (be-CN tsa. 23 ndime 4–tsa. 26 ndime 4)
Na. 2: Aroma 2:1-24
Na. 3: Kodi Munakhalapo ndi Moyo Kalelo Musanakhale ndi Moyo Umene Muli Nawo Pakalipano?
Na. 4: Kodi Mariya Ankamulemekeza Mwapadera Mumpingo Wachikristu Woyambirira? (rs-CN tsa. 259 ndime 3–tsa. 260 ndime 3)
Aug. 11 Kuŵerenga Baibulo: Aroma 5-8 Nyimbo Na. 179
Luso la Kulankhula: Kulankhula Mwachibadwa Poŵerenga Pamaso pa Anthu (be-CN tsa. 130 ndime 2-4)
Na. 1: ‘Madalitso Ali pa Wolungama’ (w01-CN 7/15 mas. 24-7)
Na. 2: Aroma 5:6-21
Na. 3: hKodi Mumakhulupirira Namwali Mariya? (rs-CN tsa. 260 ndime 4–tsa. 261 ndime 1)
Na. 4: Kodi Mungakhulupirire Chiphunzitso Chakuti Munthu Akamwalira Amabadwanso?
Aug. 18 Kuŵerenga Baibulo: Aroma 9-12 Nyimbo Na. 206
Luso la Kulankhula: Ukhondo Umakometsera Uthenga (be-CN tsa. 131 ndime 1-3)
Na. 1: Pindulani ndi Zomwe Munazoloŵera Kuchita (w01-CN 8/1 mas. 19-22)
Na. 2: w01-CN 8/15 tsa. 21 ndime 10–tsa. 22 ndime 13
Na. 3: Kodi Anthu Asintha Baibulo?
Na. 4: Kodi N’zoona Kuti Mkate ndi Vinyo Zimasandulikadi Kukhala Thupi ndi Mwazi wa Kristu? (rs-CN tsa. 280 ndime 2–tsa. 282 ndime 1)
Aug. 25 Kuŵerenga Baibulo: Aroma 13-16 Nyimbo Na. 43
Luso la Kulankhula: Mmene Kudzichepetsa ndi Kudziletsa Kumakhudzira Kavalidwe ndi Kapesedwe ka Munthu (be-CN tsa. 131 ndime 4–tsa. 132 ndime 3)
Kubwereza kwa Pakamwa
Sept. 1 Kuŵerenga Baibulo: 1 Akorinto 1-9 Nyimbo Na. 48
Luso la Kulankhula: Phindu la Kuvala Moyenera (be-CN tsa. 132 ndime 4–tsa. 133 ndime 1)
Na. 1: Kaphunziridwe Koyenera (be-CN tsa. 27 ndime 1−tsa. 31 ndime 2)
Na. 2: 1 Akorinto 3:1-23
Na. 3: Kodi Yohane 6:53-57 Amatanthauza Chiyani? (rs-CN tsa. 282 ndime 2-3)
Na. 4: Kodi Munthu Akaba Chifukwa cha Umphaŵi Ndiye Kuti Sanalakwe?
Sept. 8 Kuŵerenga Baibulo: 1 Akorinto 10-16 Nyimbo Na. 123
Luso la Kulankhula: Kuoneka Bwino Kumathandiza Kuti Ena Asakhumudwe (be-CN tsa. 133 ndime 2-4)
Na. 1: Gonjetsani Zinthu Zokulepheretsani Kupita Patsogolo! (w01-CN 8/1 mas. 28-30)
Na. 2: 1 Akorinto 12:1-26
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Zinthu Zoipa Kuchitika?
Na. 4: Kodi Yesu Anakhazikitsa Phwando la Misa? (rs-CN tsa. 282 ndime 4–tsa. 284 ndime 4)
Sept. 15 Kuŵerenga Baibulo: 2 Akorinto 1-7 Nyimbo Na. 16
Luso la Kulankhula: Kaimidwe Kabwino ndi Zida za Ntchito Zosamalika (be-CN tsa. 133 ndime 5–tsa. 134 ndime 4)
Na. 1: Mmene Mungapambanire pa Unyamata Wanu (w01-CN 8/15 mas. 4-7)
Na. 2: 2 Akorinto 6:1–7:1
Na. 3: Mmene Akristu Amaonera Olamulira a Boma (rs-CN tsa. 368 ndime 2–tsa. 369 ndime 2)
Na. 4: Kodi Mulungu Amasamala za Kuipitsidwa kwa Dziko Lapansi?
Sept. 22 Kuŵerenga Baibulo: 2 Akorinto 8-13 Nyimbo Na. 207
Luso la Kulankhula: Mmene Mungachepetsere Nkhaŵa Polankhula (be-CN tsa. 135 ndime 1–tsa. 137 ndime 2)
Na. 1: Mmene Mungasankhire Mwanzeru (w01-CN 9/1 mas. 27-30)
Na. 2: 2 Akorinto 8:1-21
Na. 3: Zomwe Zimachitikira Mzimu Munthu Akamwalira
Na. 4: Malemba Omwe Amachititsa Akristu Kusamenya Nawo Nkhondo za Anthu (rs-CN tsa. 369 ndime 3–tsa. 370 ndime 1)
Sept. 29 Kuŵerenga Baibulo: Agalatiya 1–6 Nyimbo Na. 163
Luso la Kulankhula: Zimene Mungachite Kuti Mukhale Wodekha (be-CN tsa. 137 ndime 3–tsa. 138 ndime 4)
Na. 1: Yesu Apatsa Ophunzira Ake Malangizo Enanso (gt-CN mutu 43 ndime 20-31)
Na. 2: w01-CN 9/1 tsa. 15 ndime 8–tsa. 17 ndime 11
Na. 3: Kodi ndi M’zochitika Zotani Pamene Mulungu Ankalola Aisrayeli Kumenya Nkhondo? (rs-CN tsa. 370 ndime 2–tsa. 371 ndime 3)
Na. 4: Mmene Tikudziŵira Kuti Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
Oct. 6 Kuŵerenga Baibulo: Aefeso 1–6 Nyimbo Na. 99
Luso la Kulankhula: Ubwino Wokuza Mawu (be-CN tsa. 139 ndime 1–tsa. 140 ndime 1)
Na. 1: Kuphunzira Kumapindulitsa (be-CN tsa. 31 ndime 3–tsa. 32 ndime 4)
Na. 2: Aefeso 2:1-22
Na. 3: Mpake Kukhulupirira Mulungu
Na. 4: Kodi Ndi Malemba Ati Amene Amachititsa Akristu Kusaloŵerera M’nkhani za Ndale? (rs-CN tsa. 371 ndime 4–tsa. 372 ndime 2)
Oct. 13 Kuŵerenga Baibulo: Afilipi 1–Akolose 4 Nyimbo Na. 105
Luso la Kulankhula: Gwiritsani Ntchito Bwino Maikolofoni (be-CN tsa. 140 ndime 2–tsa. 142 ndime 1)
Na. 1: Yendani ‘M’njira Yowongoka’ (w01-CN 9/15 mas. 24-8)
Na. 2: Afilipi 2:1-24
Na. 3: Kodi Ndi Malemba Ati Amene Amachititsa Akristu Kusachita Nawo Miyambo Yosonyeza Kukonda Dziko Lako? (rs-CN tsa. 372 ndime 3–tsa. 374 ndime 1)
Na. 4: Zimene Yehova Amafuna kwa Ife Masiku Ano
Oct. 20 Kuŵerenga Baibulo: 1 Atesalonika 1–2 Atesalonika 3 Nyimbo Na. 145
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Baibulo Popereka Mayankho (be-CN tsa. 143 ndime 1-3)
Na. 1: Yesu Atontholetsa Namondwe Wochititsa Mantha (gt-CN mutu 44)
Na. 2: w01-CN 10/15 tsa. 23 ndime 6–tsa. 24 ndime 9
Na. 3: Kodi Ndani Amapita Kumwamba?
Na. 4: Kodi Kusaloŵerera mu Ndale kwa Akristu Kukusonyeza Kuti Iwo Safunira Zabwino Anthu Anzawo? (rs-CN tsa. 374 ndime 2)
Oct. 27 Kuŵerenga Baibulo: 1 Timoteo 1–2 Timoteo 4 Nyimbo Na. 46
Luso la Kulankhula: Mmene Mungachitire Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Baibulo (be-CN tsa. 144 ndime 1-4)
Kubwereza kwa Pakamwa
Nov. 3 Kuŵerenga Baibulo: Tito 1–Filemoni Nyimbo Na. 30
Luso la Kulankhula: Kulimbikitsa Omvera Kugwiritsa Ntchito Baibulo (be-CN mas. 145-6)
Na. 1: Mmene Mungafufuzire Pogwiritsa Ntchito Baibulo (be-CN tsa. 33 ndime 1–tsa. 35 ndime 2)
Na. 2: Filemoni 1-25
Na. 3: Kodi Kukhala Mwangwiro Kudzakhala Kotopetsa?
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Dzina la Yehova Aligwiritsa Ntchito M’Baibulo la New World Translation M’Malemba Achigiriki Achikristu? (rs-CN tsa. 329 ndime 1-3)
Nov. 10 Kuŵerenga Baibulo: Ahebri 1-8 Nyimbo Na. 149
Luso la Kulankhula: Ubwino Wotchula Malemba Moyenerera (be-CN tsa. 147 ndime 1–tsa. 148 ndime 2)
Na. 1: Enoke Anayenda ndi Mulungu M’dziko la Anthu Osapembedza (w01-CN 9/15 mas. 29-31)
Na. 2: Ahebri 2:1-18
Na. 3: iKuyankha Anthu Amene Amanena Kuti, ‘Muli ndi Baibulo Lanulanu’ (rs-CN tsa. 330 ndime 1- 4)
Na. 4: Kodi Anthu Oukitsidwa Adzawaweruza Bwanji Malinga ndi Zochita Zawo?
Nov. 17 Kuŵerenga Baibulo: Ahebri 9-13 Nyimbo Na. 144
Luso la Kulankhula: Kusankha Mawu Oyambira Abwino Potchula Malemba (be-CN tsa. 148 ndime 3–tsa. 149 ndime 2)
Na. 1: Kodi Kukhulupirika Kumatanthauzanji? (w01-CN 10/1 mas. 20-3)
Na. 2: Ahebri 9:11-28
Na. 3: Kodi Zolengedwa za Mulungu Zakumwamba N’zolinganizika? (rs-CN tsa. 139 ndime 3–tsa. 140 ndime 1)
Na. 4: N’chifukwa Chiyani N’kopindulitsa Kutsatira Makhalidwe Amene Amalemekeza Mulungu?
Nov. 24 Kuŵerenga Baibulo: Yakobo 1-5 Nyimbo Na. 88
Luso la Kulankhula: Kutsindika Koyenera Kumaphatikizapo Mmene Mukumvera (be-CN tsa. 150 ndime 1-2)
Na. 1: Munthu Amene Anali ndi Ziwanda Akhala Wophunzira (gt-CN mutu 45)
Na. 2: w01-CN 11/1 tsa. 12 ndime 15–tsa. 13 ndime 19
Na. 3: Phindu la Kudzichepetsa
Na. 4: Kodi Mulungu Anali Kupereka Bwanji Malangizo kwa Atumiki Ake Padziko Lapansi Kalelo? (rs-CN tsa. 140 ndime 2-3)
Dec. 1 Kuŵerenga Baibulo: 1 Petro 1–2 Petro 3 Nyimbo Na. 54
Luso la Kulankhula: Tsindikani Mawu Oyenera (be-CN tsa. 150 ndime 3–tsa. 151 ndime 2)
Na. 1: Kuphunzira Kugwiritsa Ntchito Zida Zina Zofufuzira (be-CN tsa. 35 ndime 3–tsa. 38 ndime 4)
Na. 2: 1 Petro 1:1-16
Na. 3: Kodi Baibulo Limasonyeza Kuti Akristu Oona Anali Kudzakhala Olinganizika? (rs-CN tsa. 141 ndime 2–142 ndime 2)
Na. 4: Mmene Nsembe ya Dipo ya Kristu Iyenera Kukhudzira Moyo Wathu
Dec. 8 Kuŵerenga Baibulo: 1 Yohane 1-5; 2 Yohane 1-13; 3 Yohane 1-14–Yuda 1-25 Nyimbo Na. 22
Luso la Kulankhula: Njira Zotsindikira Malemba (be-CN tsa. 151 ndime 3–tsa. 152 ndime 5)
Na. 1: Tetezani Chikumbumtima Chanu (w01-CN 11/1 mas. 4-7)
Na. 2: 1 Yohane 3:1-18
Na. 3: Chifukwa Chake Sitinganene Kuti Baibulo N’limene Lachititsa Kuti Akazi Asamalemekezedwe
Na. 4: Kodi Atumiki Okhulupirika a Mulungu Angomwazikana M’Matchalitchi Achikristu? (rs-CN tsa. 142 ndime 3-5)
Dec. 15 Kuŵerenga Baibulo: Chivumbulutso 1-6 Nyimbo Na. 219
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Malemba Moyenera (be-CN tsa. 153 ndime 1–tsa. 154 ndime 2)
Na. 1: Chikhulupiriro cha Nowa Chimatsutsa Dziko Lapansi (w01-CN 11/15 mas. 28-31)
Na. 2: Chivumbulutso 2:1-17
Na. 3: Kodi Gulu Looneka la Yehova Lingadziŵike Bwanji? (rs-CN tsa. 143 ndime 1-7)
Na. 4: Chifukwa Chake Akristu Sakondwerera Khirisimasi
Dec. 22 Kuŵerenga Baibulo: Chivumbulutso 7-14 Nyimbo Na. 6
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Malemba Momveka Bwino (be-CN tsa. 154 ndime 3–tsa. 155 ndime 3)
Na. 1: Mungathe Kupeŵa Matenda a Mtima Wauzimu (w01-CN 12/1 mas. 9-13)
Na. 2: w01-CN 12/15 tsa. 17 ndime 10–tsa. 18 ndime 13 (kuphatikizapo mawu a m’munsi)
Na. 3: Zimene Tingachite Kuti Tithane ndi Kusonkhezeredwa ndi Anzathu
Na. 4: Kodi Tingalemekeze Bwanji Gulu la Yehova? (rs-CN tsa. 143 ndime 8-12)
Dec. 29 Kuŵerenga Baibulo: Chivumbulutso 15-22 Nyimbo Na. 60
Luso la Kulankhula: Lingalirani Nawo Kuchokera M’Malemba (be-CN tsa. 155 ndime 4–tsa. 156 ndime 4)
Kubwereza kwa Pakamwa
[Mawu a M’munsi]
a Nkhani imeneyi muipereke kwa mbale basi.
b Nkhani imeneyi muipereke kwa mbale basi.
c Nkhani imeneyi muipereke kwa mbale basi.
d Nkhani imeneyi muipereke kwa mbale basi.
e Nkhani imeneyi muipereke kwa mbale basi.
f Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
g Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
h Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
i Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.