Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira October 14
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe za mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 17: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: “Njira Zimene Oyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo Amasonyezera Kuganizira Ena.” Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo. Konzekeretsani ofalitsa aŵiri kapena atatu kuti afotokoze momwe apindulira chifukwa chakuti anali kuwaganizira pa Phunziro la Buku la Mpingo.
Nyimbo Na. 65 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 21
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 35: “Tinapindula Kwambiri ndi Msokhano Wachigawo Wakuti ‘Olengeza Ufumu Achangu.’” Ikambidwe ndi wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Akakamba mawu oyamba osapitirira mphindi imodzi, akambirane ndi omvetsera pulogalamu ya msonkhano wachigawo, agwiritse ntchito mafunso amene ali m’nkhaniyi. Gaŵani bwino nthaŵi yanu. Mukhoza kumawonjezera mawu achidule kuti mukumbutse omvetsera mfundo zikuluzikulu. Ngati n’koyenera, funsani omvetsera momwe agwiritsira ntchito zimene anaphunzira ndipo apindula chiyani chifukwa chochita zimenezo.
Nyimbo Na. 194 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 28
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Pokonzekera nkhani ya mu Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wamaŵa, limbikitsani onse kukaŵerenga zimene analemba papulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera wapitawo. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo ziŵiri za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya October 15 ndi Galamukani! ya October 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizi, sonyezani njira zosiyana za mmene tingayankhire munthu akanena mawu otsekereza kukambirana naye akuti: “Ndili wozoloŵerana kale ndi ntchito yanu.”—Onani buku la Kukambitsirana, patsamba 20.
Mph. 15: Zokumana nazo. Pemphani anthu pampingopo kusimba zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo popita ndi pochokera ku msonkhano wachigawo, kaya pamsonkhanopo, kapena pamene anali kuchita ulaliki wa mwamwayi kuntchito, kusukulu, pokagula zinthu kapenanso pochita zinthu zina.
Mph. 20: Kambiranani “Bokosi la Mafunso.”
Nyimbo Na. 41 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 4
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Pendani mwachidule mfundo zingapo za mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002 za momwe tingagaŵire bulosha la Mulungu Amafunanji ndiponso buku la Chidziŵitso. Chitani chitsanzo chimodzi pamenepa. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a mu utumiki wakumunda a October. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, mlongo asonyeze momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya November 1 ndipo mbale asonyeze momwe tingagaŵire Galamukani! ya October 8. Akatha chitsanzo chilichonse, tchulani mbali zabwino za ulaliki wa chitsanzowo.
Mph. 13: Osachita Manyazi ndi Uthenga Wabwino. (Aroma 1:16) Wachinyamata auze bambo ake vuto limene ali nalo. Wachinyamatayo safuna kudziŵika kuti ndi wa Mboni za Yehova chifukwa amaopa kuti anzake angamamuseke. Bambo athokoze mwanayo chifukwa chonena zoona pankhaniyo. Amuuze zimene Petro nthaŵi ina anachita chifukwa cha zonena za anthu. (Mat. 26:69-74) Bambowo amulangize izi: Tisamachite manyazi ndi zimene timakhulupirira monga Akristu. (Marko 8:38) N’kopindulitsa kuwadziŵitsa akusukulu kwanu kuti ndiwe Mboni. Aphunzitsi ambiri akadziŵa kuti ndiwe wa Mboni adzalemekeza zikhulupiriro zako ndipo sadzakuphatikiza m’zochitika zimene umaona kuti n’zoipa. Mwachionekere achinyamata opanda m’khalidwe sadzakukakamiza kuchita zinthu zosalongosoka. Anzako ena am’kalasi mwako adzamvetsa mosavuta chifukwa chake suchita nawo zibwenzi, maseŵera osakhudzana ndi maphunziro, kapena zimene amachita akaŵeruka. Ngati nthaŵi ilipo, bambo ndi wachinyamatayo akambirane mfundo za m’buku la Achichepere Akufunsa, pamutu wakuti “Kulengeza Poyera Unansi Wanu ndi Mulungu,” masamba 315-318. Wachinyamatayo ayamikire malangizo abwino amene amuuzawo.
Mph. 22: Gonjerani Mulungu—Kanizani Mdyerekezi. (Yak. 4:7) Mogwiritsa ntchito mafunso ali pompaŵa, mkulu akambirane mosangalatsa ndi omvetsera za pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera umene unachitika chaka chautumiki chathachi. Pemphani anthu a pampingopo kusimba momwe agwiritsira ntchito zimene anaphunzira. (Mukhoza kuwapatsiratu anthu mbali zimenezi.) Kambiranani mbali za msonkhano izi: (1) “Kugonjera Mulungu m’Dziko Laukapolo.” N’chifukwa chiyani tifunika kukhala tcheru kuti tipeŵe kukodwa m’misampha yadzikoli? (2) “Kugonjera Mulungu Monga Anthu Okhala M’banja.” N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuti mabanja a m’gulu la Yehova alimbitse unansi wawo? Kodi tingachite motani zimenezi? (3) “Thandizani Ophunzira Atsopano Kuima Zolimba ku Mbali ya Yehova.” Kodi tingawathandize bwanji atsopano kugonjetsa zopinga zimene zimayesa chikhulupiriro chawo? (4) “Tanthauzo la Kukaniza Mdyerekezi.” Kodi chofunika kwambiri n’chiyani kuti tipambane polimbana ndi Mdyerekezi? Kodi zida zauzimu zotchulidwa pa Aefeso 6:11-18 zingatiteteze bwanji? (w92-CN 5/15 21-23) (5) “Achinyamata Omwe Akupambana Pogonjetsa Woipayo” ndi “Achinyamata Omwe Akupindula Chifukwa Chogonjera Mulungu.” Kodi misampha ina ya Satana imene achinyamata ayenera kupeŵa ndi iti? Kodi achinyamata akupindula chiyani chifukwa chogonjera Yehova? (w90-CN 8/1 13-14, ndime 15-17) (6) “Phindu la Kugonjera Mulungu.” Fotokozani momwe Akristu amasonyezera kugonjera maulamuliro a boma, owalemba ntchito, m’banja ndi mu mpingo wachikristu. Kodi ndi makhalidwe ati amene angatithandize kuchita zimenezi?
Nyimbo Na. 185 ndi pemphero lomaliza.