Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu May: Gaŵirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, amene ena mwa iwo angakhale amene anabwera pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina koma sasonkhana ndi mpingo, yesetsani kuwagaŵira bulosha la Mulungu Amafunanji. Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. June: Gaŵirani buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji. Ngati eninyumba ali nazo kale zofalitsa zimenezi, gwiritsirani ntchito bulosha lina loyenerera limene mpingo uli nalo. Chogaŵira Chapadera mu July ndi August: Dziŵani kuti pa chilengezo chomwe chili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March ndi April pali kusintha uku: Mu July ndi August tidzagaŵira bulosha la Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza? Mabuloshaŵa tikuwatumiza ku mipingo. Mukamaliza kugaŵira mabulosha onse a Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wamusankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa June 1 kapena patangodutsa masiku ochepa kuchoka pa detili. Mukatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo mukamaliza kuŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Kuti tidzaimbe bwino nyimbo pa misonkhano yachigawo, taika mndandanda wa nyimbo zimene zidzaimbidwe kuti anthu onse athe kuzikonzekera misonkhanoyi isanafike. Nyimbozo ndi izi: 96, 79, 63, 111, 160, 4, 59, 193, 202, 18, 12, 164, 175, 157, 92, 201, 113, 212. Motero tikulimbikitsa mipingo yonse kuti ipeze nthaŵi yoti anthu aziphunzira nyimbo zimenezi misonkhano ikatha. Mipingo imene muli abale amene angalole kuti wailesi zawo za kaseti ndi matepi awo a nyimbo za Ufumu zigwiritsidwe ntchito ikulimbikitsidwa kuti anthu akamakonzekera nyimbozi azigwiritsira ntchito makasetiwo kuti azoloŵere kuimba motsatira malimba kuti asamakavutike pa misonkhano yachigawo.