Kaonekedwe Kabwino Koyenera Akristu
1 Ndife “choonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu,” anatero mtumwi Paulo. (1 Akor. 4:9) Monga Mboni za Yehova timaona kuti ndi mwayi wapadera kwambiri kuimira Atate wathu, Yehova, ndipo timatero tili aukhondo komanso titavala modzilemekeza. (1 Akor. 10:31-33) Timadziŵa kuti khalidwe, kalankhulidwe, mmene timaonekera komanso masitayilo a zovala zathu, zingakhudze mmene ena amaonera nkhani ya kulambira Yehova moona.
2 Anthu ena akamatiyang’ana, kodi amaonanji? Kodi zovala zathu zimasonyeza kuti sitidzilemekeza? Kodi anthu ena angaone kuti zovala zathu ndiponso maonekedwe athu zimadzutsa chilakolako cha kugonana? Kodi anthu ena angadodometsedwe kapena kunyansidwa chifukwa cha mmene tikuonekera, mmene tikuyendera kapena khalidwe lathu? Malinga ndi malipoti amene talandira, zimenezi zachitikapo. Abale ena amabwera kumisonkhano atavala zovala zosayenera kuvala ku misonkhano ngati kuti akupita ku maseŵero—malaya ali osapisira, ndevu za pa mlomo wam’mwamba zili zosadulira mwinanso zosapesa n’komwe. Akristu sayenera kuchita zimenezi.
3 Nkhani ina pa Msonkhano Wachigawo wa mu 1981 wakuti “Chikhulupiriro ku Ufumu” inanena mwamphamvu kuti: ‘N’zovuta kumvetsa chifukwa chimene chingapangitse mtumiki wa Yehova Mulungu kufuna kutsatira masitayilo osonyeza makhalidwe oipa ndi opanduka a dziko la Satanali. N’chifukwa chiyani munthu angafune kufanana ndi dziko n’kumaoneka mosiyana ndi anthu a Yehova? Kodi sizingakhale bwino kuoneka monga anthu a Yehova, n’kumasiyana ndi anthu a dzikoli? Kodi tikufuna kusangalatsa ndani? Kodi tikufuna kukondedwa ndi ndani? Bwanji osatengera mmene abale okhwima mwauzimu omwe ali ndi maudindo mu mpingo amavalira ndi kuonekera bwino? Kodi sitingatengerepo phunziro ndi kutsanzira chitsanzo chawo chabwino?’
4 Pa 1 Timoteo 2:9, 10, Paulo ananena kuti akazi azivala “ndi manyazi, ndi chidziletso.” Amuna nawonso afunika kutsatira mfundo imeneyi. Kusatsatira malangizo ameneŵa kungasonyeze kuti sitilemekeza misonkhano yathu yachikristu, kuphatikizaponso phunziro la buku la mpingo, misonkhano ya akulu ndiponso zochitika ina.
5 Komanso, ganizirani za zinthu zimene timagwiritsira ntchito polalikira. Ngakhale kuti tingakonzekere zokakambirana ndi anthu za m’Malemba, zingatheke kukhala osakonzekera bwino zinthu zokagwiritsira ntchito. Magazini, mabulosha, ndiponso mathirakiti omwe ali m’chikwama chathu cha mu utumiki angakhale okwinyikakwinyika kapena ong’ambikang’ambika. Tingalephere kupeza pensulo kapena khadi lolembapo za kunyumba ndi nyumba chifukwa chakuti zinthu sizinalongedzedwe bwino m’chikwama chathu. M’pofunika kuonetsetsa kuti zinthu zathu zokagwiritsira ntchito zili bwino tisanaloŵe mu utumiki wakumunda.
6 N’chimodzimodzinso tikamapita ku misonkhano yathu yachikristu. Sitidzavutika kupeza zinthu zofunika pa mbali iliyonse ya msonkhano ngati zonse zimene timagwiritsira ntchito zalongedzedwa bwino m’chikwama chathu. Tikamagwiritsira ntchito chikwama chathu mu utumiki wakumunda, tizionetsetsa kuti chili bwino. Sikuti n’zolira chikwama chatsopano, koma chikwamacho chifunika kukhala chaukhondo ndiponso chosang’ambika.
7 Motero, m’pofunika kusamala kwambiri ndi mmene timavalira ndiponso mmene timaonekera kwa anthu ena! Kodi sizingakhale bwino kusonyeza khalidwe la Amene timalambira, m’malo moti tizidodometsa kapena kukhumudwitsa anthu chifukwa cha khalidwe kapena kaonekedwe kathu, kaya chifukwa chovala zovala zosayenera, kapenanso chifukwa chakuti zinthu zomwe timagwiritsira ntchito polalikira n’zosalongosoka ndiponso zong’ambika? (1 Akor. 14:33, 40) Kuvala ndiponso kaonekedwe kathu pamisonkhano komanso mu utumiki ziyenera kusonyeza ulemu womwe umafunika pa kulambira Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse, Yehova Mulungu.