Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu June: Buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji. Ngati eninyumba ali nazo kale zofalitsa tatchulazi, gaŵirani bulosha lililonse loyenera limene mpingo uli nalo. July ndi August: Gwiritsani ntchito bulosha lakuti Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza? Ngati mabulosha ameneŵa atha, gwiritsani ntchito bulosha la Mulungu Amafunanji. Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo akasonyeza chidwi. September: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja kapena Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako.
◼ Kuwonjezera pa zimene tinalengeza mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa October ndi December, 2002, pankhani ya zinthu za oda yapadera, monga mabaibulo a Chichewa ndi a Chitumbuka, tikufuna kukumbutsa mipingo kuti isamaitanitse mulu wa zimenezi. Aziitanitsa pakakhala amene aoda mwapadera.
◼ Zofalitsa Zimene Zilipo m’Chitumbuka
Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso
Chifukwa Chake Mungadalire Baibulo (Thirakiti Na. 13)
Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo (Thirakiti Na. 20)
Elementary Bible Teachings
Kodi Dzikoli Lidzapulumuka? (Thirakiti Na. 19)
Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Chiyani? (Thirakiti Na. 14)
Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? (Thirakiti Na. 26)
Kodi Muli ndi Mzimu Wosafa? (Thirakiti Na. 25)
Kodi Mulungu Amafunanji Kwa Ife?
Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko? (Thirakiti Na. 22)
Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Okondedwa Akufa? (Thirakiti Na. 16)
Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?
Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere (Thirakiti Na. 15)
Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?
Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!
Sangalalani ndi Moyo Wabanja (Thirakiti Na. 21)
Yehova—Kodi Iye Ndani? (Thirakiti Na. 23)
Yesu Kristu—Kodi Iye Ndani? (Thirakiti Na. 24)
Tikulimbikitsa mipingo kuitanitsa zimenezi kuti azigwiritsa ntchito mu utumiki.