Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Ena Kupeza Njira ya ku Moyo Wosatha?
1 Kuyesetsa Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo Apanyumba: Mu July ndi August tidzakhala ndi mwayi wogaŵira bulosha latsopano lakuti Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza? Pogaŵira buloshali tikufuna kuyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
2 Kodi Bulosha Latsopanoli Tiligwiritse Ntchito Bwanji? Panopo mpingo wanu uyenera kuti unalandira mabulosha ameneŵa. Dziŵani kuti buloshali sikuti likuloŵa m’malo mwa bulosha la Mulungu Amafunanji, koma kuti n’longothandizira anthu kumvetsetsa mmene Mulungu amaonera miyambo ina. M’buloshali muli nkhani ngati izi: “Ali Kudziko la Mizimu Ndani?” “Kodi Makolo Athu Ali Kuti?” ndiponso “Zoona Zake za Matsenga ndi Ufiti.” Buloshali lingagwiritsidwe ntchito monga poyambira kuphunzira bulosha la Mulungu Amafunanji, kenako buku la Chidziŵitso. Mungaligwiritse ntchitonso buloshali kuthandiza ophunzira Baibulo anu kumvetsa nkhani zimenezi. Tikatha ndaŵala imeneyi, mpingo uliwonse ukupemphedwa kuitanitsa mabulosha ameneŵa kuti azigwira ntchito akafunika.
3 Pogaŵira Buloshali: Munganene kuti: “Anthu amalambira mosiyanasiyana. Tikanena kuti zipembedzo zili ngati njira, kodi Mulungu amayanja njira za chipembedzo zonsezo? Yesu mneneri wa Mulungu ananena kuti pali njira ziŵiri zokha basi. Anatsimikizira zimenezi pa Mateyu 7:13, 14. [Ŵerengani m’Baibulo lanu.] Mawu a Yesu ameneŵa akusonyeza kuti pali zipembedzo ziŵiri zokha: china chimapita kumoyo ndipo chinacho kuchiwonongeko. Bukuli lakonzedwa kuti likuthandizeni kupeza njira ya ku moyo wosatha.” Mungaone kuti ulaliki umenewu ungakonzedwe pogwiritsa ntchito zimene zili pa tsamba loyamba kumanzere kwa chithunzi chili pamenepo.
4 Yehova kudzera mwa Mboni zake akuwapatsa anthu mpata kulikonse ‘wolowa pa chipata chopapatiza’ ndiponso woyenda panjira ya ku moyo wosatha. Tichitetu zotheka kuthandiza anthu ambiri mmene tingathere kuti akhale pagulu la anthu achimwemwe amene avomera pempholi ndi kusangalala ndi madalitso a Yehova kosatha.—Mat. 7:13, 14.