Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu September: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja kapena Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji kwa anthu amene asonyeza chidwi ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. November: Gaŵirani buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji. Mukapeza eninyumba amene ali nalo kale buku ndi bulosha limeneli, agaŵireni bulosha lina lililonse. December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mulibe, mungagaŵire Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, ndi Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
◼ Ofesi ya nthambi silembera wofalitsa oda ya mabuku amene akuwafuna. Woyang’anira wotsogolera azikonza chilengezo mwezi uliwonse asanatumize ku nthambi oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo kuti onse amene akufuna mabuku auze mbale woyang’anira za mabuku. Chonde, kumbukirani zofalitsa zimene zili za oda yapadera.
◼ Tikukumbutsa akulu kutsatira malangizo a mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, masamba 21 mpaka 23, onena za anthu ochotsedwa kapena odzilekanitsa amene akufuna kubwezeretsedwa.
◼ Nkhani ya onse yapadera ya pa nyengo ya Chikumbutso cha 2004 idzakambidwa Lamlungu, pa April 18. Tidzalengeza mutu wa nkhaniyi m’tsogolo muno. Mipingo imene idzakhale ndi woyang’anira dera, msonkhano wadera, kapena tsiku la msonkhano wapadera mlungu umenewu, idzakhale ndi nkhani yapaderayi mlungu wotsatizana ndi mlungu umenewu. Mpingo uliwonse usakhale ndi nkhani yapaderayi pasanafike pa April 18, 2004.
◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:
Chidziŵitso—la Zilembo Zazikulu (kllp)—Chingelezi
Lambirani Mulungu Woona Yekha—la Zilembo Zazikulu (wtlp)—Chingelezi
Mapositikadi a Malawi—Chichewa Tikulimbikitsa mipingo kuti iyambe kuitanitsa zimenezi.
Yandikirani kwa Yehova—la Zilembo Zazikulu (cllp)—Chichewa, Chingelezi
◼ Monga mmene tinalengezera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2003 pankhani ya magazini ya Nsanja ya Olonda ya zilembo zazikulu, mabuku a Yandikirani kwa Yehova—la Zilembo Zazikulu (kllp), Lambirani Mulungu Woona Yekha—la Zilembo Zazikulu (wtlp), ndi Chidziŵitso—la Zilembo Zazikulu (kllp), akonzera makamaka anthu amene amavutika kuona. Choncho, alembi a mipingo akamasaina fomu yoitanitsira mabuku a mpingo ya (S-14) mwezi uliwonse azionetsetsa kuti anthu amene akuitanitsa mabuku ameneŵa alidi ndi vuto la maso.