Kuphunzira buku la Lambirani Mulungu
Buku la Lambirani Mulungu Woona Yekha analikonza kuti tiziliphunzira ndi anthu atsopano akamaliza kuphunzira buku la Chidziŵitso. Kuphunzira buku limeneli pa Phunziro la Buku la Mpingo kutithandiza kuti tithe kuligwiritsa bwino ntchito mu utumiki komanso kuti tikulitse chikondi ndi chiyamikiro chathu pa Yehova ndi gulu lake. Kodi tingapindule bwanji ndi kuphunzira kwathu m’buku la Lambirani Mulungu?
Kuchititsa Phunzirolo: Popeza tiziphunzira mutu wathunthu mlungu uliwonse, oyang’anira maphunziro a buku ayenera kugaŵa bwino nthaŵi. Sakufunika kuchedwa kwambiri pa ndime zoyambirira za phunzirolo kuti akhale ndi nthaŵi yokwanira yokambirana mfundo zofunika kwambiri, zimene nthaŵi zambiri zimakhala chakumapeto kwa mutuwo. Kukambirana mwachidule bokosi la kubwereramo pamapeto pa phunziro lililonse kudzathandiza anthu amene alipo kukumbukira mfundo zofunika.
Pafupifupi theka la mitu yonse ya m’buku la Lambirani Mulungu ili ndi mafunso amene alembedwa mkati pang’ono kuchokera kumanzere oti musinkhesinkhe ndi kukambirana. Chitsanzo cha mafunso otereŵa chili pa tsamba 48. Sipofunika kuŵerenga mafunso ameneŵa mukamaŵerenga pandime. Akamakambirana mafunsoŵa ndi gulu lake, woyang’anira phunziro ayenera kupempha anthu kuŵerenga malemba amene atchulidwa ndipo akambirane malemba ameneŵa ndi anthuwo mogwirizana ndi nthaŵi imene ilipo.
Kukonzekereratu: Kukonzekera bwino phunzirolo kumafuna zambiri, osati kungolemba mzere kunsi kwa mayankho. Kusinkhasinkha mozama za malemba amene atchulidwa komanso kupemphera kudzatithandiza kukonzekera osati mayankho okha, komanso kukonzekeretsa mtima wathu, kumene kuli kofunika kwambiri. (Ezara 7:10) Tonsefe tingathandize kuti tilimbikitsane mwa kupereka ndemanga momasuka komanso moganizira ena.—Aroma 1:11, 12.
Kuphunzira buku la Lambirani Mulungu kutithandiza kuti tiyandikane ndi Yehova ndipo kutithandiza kudziŵa mmene tingathandizire anthu oona mtima kuti abwere kudzalambira Yehova limodzi nafe. (Sal. 95:6; Yak. 4:8) Tiyeni tonsefe tipindule kwambiri ndi mphatso yauzimu imeneyi.