Sangalalani Pophunzira Buku Lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
1 Chinthu china chimene chinali chosangalatsa kwambiri pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Kumvera Mulungu” chinali kutulutsidwa kwa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Posachedwapa tidzayamba kuligwiritsa ntchito kwambiri mu utumiki wathu wa kumunda, makamaka pamene tikuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Choncho, tikufunikira kulidziwa bwino kwambiri buku latsopano limeneli. Zimenezo zitheka ndithu chifukwa chakuti tidzayamba kuphunzira bukuli pa Phunziro la Buku la Mpingo kuyambira mlungu woyamba ndi April 17, 2006.
2 Woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo adzafunikira kufunsa mafunso amene ali pachiyambi pa mutu uliwonse. Kenako n’kuyamba kuchititsa phunziro pogwiritsa ntchito mafunso amene ali pansi pa tsamba lililonse. Mudzafunikira kuwerenga Malemba ofotokoza mfundo zofunika ndi kuwakambirana. Ndiyeno mudzafunikira kubwereza phunzirolo pogwiritsa ntchito mafunso akumapeto kwa mutu uliwonse akuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa.” Mabokosi a mafunso amenewa adzakhala othandiza chifukwa chakuti ali ndi mayankho a m’malemba a mafunso amene anafunsidwa kumayambiriro kwa mutu uliwonse. Kuyankha mafunso a m’bukuli kudzakhala kosangalatsa kwambiri chifukwa chakuti likufotokoza nkhani momveka bwino, mosavuta ndi mosangalatsa.
3 M’bukuli muli nkhani za kumapeto zimene zikufotokoza mwakuya nkhani zosiyanasiyana. Tizidzagwiritsa ntchito nkhani zimenezi ngati wophunzira Baibulo akufuna kudziwa zambiri pankhani inayake. Mbali zina za nkhani za kumapeto zimenezi tidzazikambirana pa Phunziro la Buku la Mpingo. Wowerenga pa phunziro la buku ndiye amene azidzawerenga nkhani za kumapeto ndipo nkhani zazitali mungadzazikambirane mu zigawozigawo. Chigawo chimenechi chilibe mafunso ophunzirira, koma woyang’anira phunziro azidzafunsa mafunso ofuna kuti anthu afotokoze mfundo zazikulu zimene zili m’nkhaniyo.
4 Tidzaphunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani mofulumira kwambiri pa Phunziro la Buku la Mpingo. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti tizidzathamanga chimodzimodzi pophunzira ndi anthu ena. Ngati tikuphunzira ndi anthu amene sadziwa zambiri zokhudza Baibulo kapena amene sadziwiratu kalikonse, tidzafunikira kuwaphunzitsa pang’onopang’ono. (Mac. 26:28, 29) Pochititsa phunziro la Baibulo la panyumba, tikufunikira kukambirana malemba bwinobwino, kufotokoza zitsanzo, ndi zina zotero. Choncho, musajombe mlungu uliwonse ndiponso konzani zoti muzidzayankha nawo pophunzira buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? pa phunziro la buku.