Tsanzirani Mphunzitsi Waluso Pogwiritsa Ntchito Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
1. Kodi Yesu ankaphunzitsa motani?
1 Mphunzitsi Waluso, Yesu Khristu, nthawi zonse ankafotokoza zinthu m’njira yosavuta ndi yomveka bwino. Pofuna kuti omvera ake aziganizira mwakuya nkhani zomwe ankawauza, iye nthawi zina ankayamba ndi kufunsa mafunso ofuna kudziwa maganizo awo. (Mat. 17:24-27) Ankakambirana nawo nkhani za m’Mawu a Mulungu. (Mat. 26:31; Maliko 7:6) Iye ankasamala kuti asasokoneze ophunzira akewo ndi zinthu zambirimbiri, popeza ankadziwa kuti apitirizabe kuphunzira nawo. (Yoh. 16:12) Yesu ankafunanso kudziwa ngati ophunzira akewo akhulupirira ndi kumvetsetsa zinthu zimene iye wawaphunzitsa. (Mat. 13:51) Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani lakonzedwa kuti litithandize kuphunzitsa m’njira yofanana ndi njira imene Yesu ankaphunzitsira.
2. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mafunso a kumayambiriro kwa mutu uliwonse?
2 Mafunso a Kumayambiriro kwa Mutu: Mukamayamba kuphunzira mutu uliwonse, ndibwino kuyamba ndi kufunsa mafunso amene ali m’munsi mwa mutuwo. Funsani mafunsowo m’njira yoti munthuyo akhale ndi chidwi. Kapenanso mungam’pemphe kuti ayankhe mafunsowo mwachidule. N’zosafunika kuti mukambirane kwa nthawi yaitali zomwe wanenazo, kapena kukonza zilizonse zimene walakwitsa. Mukhoza kungomuthokoza chifukwa chonena maganizo ake kenaka n’kuyamba kuphunzira. Ndemanga zake pa mafunsowo zidzakuthandizani kuti mudziwe mbali zimene mungafunike kuzigogomezera kwambiri paphunzirolo.
3. Kodi tingachititse bwanji phunziro m’njira yosavuta?
3 Malemba: Malemba azikhala mbali yaikulu ya phunzirolo. (Aheb. 4:12) Komabe, sikuti muziwerenga lemba lililonse limene lili m’ndime. Werengani ndi kugogomezera mavesi ofotokoza mfundo zikuluzikulu za zikhulupiriro zathu za m’Malemba. Simungafunikire kuwerenga Malemba amene amangolongosola mmene zinthu zinazake zinachitikira, chifukwatu bukuli palokha limalongosola choonadi momveka bwino. Chititsani phunzirolo mosavuta. Kambiranani mfundo zikuluzikulu, ndipo pewani chizolowezi cholongosola zinthu zambirimbiri kapenanso cholowetsamo zinthu zosafunika ndiponso zosagwirizana ndi phunzirolo.
4. Kodi pochita phunziro, n’chiyani chimene chingatichititse kupatula kapena kusapatula nthawi yokambirana zakumapeto?
4 Zakumapeto: Zakumapeto za m’bukuli zili ndi mitu 14 imene imalongosola bwino nkhani za m’bukhumu. Mungasankhe kukambirana zakumapetozi kapena ayi. M’mitu ina, mukhoza kungom’limbikitsa munthu amene mukuphunzira nayeyo kuti akawerenge yekha zakumapeto. Mungatero makamaka ngati akumvetsa ndiponso kuvomereza mfundo za m’ndime zimene mukuphunzirazo. Mwachitsanzo, ngati wophunzirayo amakhulupirira kale kuti Yesu ndi Mesiya, mukamaphunzira naye mutu 4 wakuti, “Kodi Yesu Khristu Ndani?” m’posafunika kukambirana mutu wa zakumapeto wakuti “Mesiya Wolonjezedwayo Anali Yesu.” Komano nthawi zina, zingakhale zopindulitsa ngati paphunziro lanu mutapatula nthawi yokambirana zakumapeto, ngakhale zochepa chabe.
5. Ngati tasankha kukambirana mfundo zakumapeto, kodi tingakambirane m’njira yotani?
5 Ngati mwasankha kukambirana zakumapeto, mungakonzeretu mafunso oti mukambirane ndi wophunzirayo pambuyo powerenga ndime monga mmene mumachitira mukamakambirana ndime zophunziridwa. Kapenanso, mogwirizana ndi zimene wophunzirayo akufunikira, mungapatule mphindi zochepa mukamachita phunzirolo kuti mukambirane naye mwachidule mfundo zakumapetozo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mutsimikize ngati wophunzirayo wamvetsetsadi zakumapeto zomwe anawerenga yekhazo.
6. Kodi bokosi la kubwereza limene lili kumapeto kwa phunziro lililonse lingagwiritsidwe ntchito bwanji?
6 Bokosi la Kubwereza: Bokosi lomwe lili kumapeto kwa mutu uliwonse lili ndi mfundo zimene kawirikawiri zimayankha mafunso a kumayambiriro kwa mutu. Mukamamaliza phunziro, mungagwiritse ntchito mfundo za m’bokosi limeneli pobwereza mfundo zikuluzikulu zimene mwaphunzira. Ofalitsa ena aona kuti n’zothandiza kuwerenga pamodzi ndi wophunzirayo mfundo iliyonse ya m’bokosili ndiponso malemba ake. Ndiyeno amapempha wophunzirayo kuti alongosole mwachidule kuti malembawo akugwirizana motani ndi mfundozo. Zimenezi zimathandiza mphunzitsi kuti aone ngati wophunzirayo wamvetsadi mfundo zikuluzikulu m’phunzirolo ndiponso ngati wamvetsa kuti zikugwirizana bwanji ndi Baibulo. Mphunzitsi angaonenso ngati wophunzirayo akuvomerezadi mfundozo kapena ayi. Kuchita zimenezi kumathandiza wophunzira kuti azigwiritsa ntchito Baibulo pofotokozera ena choonadi.
7. Kodi timagwiritsa ntchito bwanji buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pokwaniritsa utumiki wathu?
7 Njira yabwino koposa yokwaniritsira utumiki wathu wophunzitsa anthu ndiponso kupanga ophunzira n’kutsanzira mmene Yesu ankaphunzitsira. (Mat. 28:19, 20) Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani lingatithandize kuti tichite zimenezo. Gwiritsani ntchito bwino buku limeneli pophunzitsa ena choonadi momveka, mosavuta, ndiponso mosangalatsa.