Muzigwiritsa Ntchito Bwino Buku Lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
Zinthu zimayenda bwino kwambiri ngati munthu amene tikuphunzira naye akumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa komanso kuzitsatira pa moyo wake. (Sal. 1:1-3) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kugwiritsa ntchito bwino zinthu zina zimene zili m’buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.
Mafunso a Kumayambiriro kwa Mutu: Kumayambiriro kwa mutu uliwonse kuli mafunso ndipo mayankho ake timawapeza tikamaphunzira mutuwo. Mungachite bwino kufunsa mafunsowa pamene mukuyamba kuphunzira mutuwo n’cholinga choti munthuyo adziwe zimene aphunzire m’mutuwo. Apo ayi mungamupemphe kuti ayankhepo. Ngati atapereka yankho lolakwika si bwino kumutsutsa. Zimene wanenazo zingakuthandizeni kudziwa mfundo zimene muyenera kuzifotokoza bwino mukamaphunzira naye.—Miy. 16:23; 18:13.
Zakumapeto: Ngati munthu wamvetsa mfundo za mu ndime, ndi bwino kumuuza kuti awerenge payekha mfundo zakumapeto zogwirizana ndi mutu umene mukuphunzirawo. Mukadzakumananso mungadzadutsemo mwachidule kuti mungotsimikizira ngati wazimvetsa. Koma ngati mukuona kuti n’zofunika kwa wophunzirayo, mungawerenge naye ndime zakumapetozo n’kumafunsa mafunso amene mwakonza nokha.
Bokosi la Kumapeto kwa Mutu: Bokosi la kumapeto kwa mutu uliwonse limakhala ndi mfundo zimene zimayankha mafunso a kumayambiriro kwa mutuwo. Mukhoza kugwiritsa ntchito mfundo zimenezi potsimikizira kuti wophunzira wanuyo wamvetsa mfundo zazikulu za m’mutu umene mwaphunzira. Ndi bwino kuwerenga limodzi mfundozo komanso malemba ake. Kenako mungapemphe munthuyo kuti agwiritse ntchito malembawo posonyeza kuti mfundozo n’zolondola.—Mac. 17:2, 3.