Mmene Tingagwiritsire Ntchito Buku la “Chikondi cha Mulungu” Pochititsa Maphunziro a Baibulo
1. Kodi cholinga cha buku la “Chikondi cha Mulungu” n’chiyani?
1 Pamsonkhano wachigawo wamutu wakuti “Mzimu wa Mulungu Umatitsogolera,” tinasangalala kwambiri pamene tinalandira buku latsopano lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu.” Potulutsa bukuli, panalengezedwa kuti cholinga chake sikuphunzitsa ziphunzitso zikuluzikulu za m’Baibulo ayi, koma kutithandiza kudziwa komanso kukonda mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Choncho, sitidzagawira buku limeneli muutumiki wa khomo ndi khomo.
2. Kodi buku limeneli tidzaligwiritsa ntchito motani ndipo kwa ndani?
2 Tiziphunzira buku latsopanoli ndi ophunzira Baibulo tikamaliza kuphunzira nawo buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kumbukirani kuti anthu amamvetsa zinthu zauzimu mosiyanasiyana. Choncho chititsani phunziro mogwirizana ndi luso la wophunzira aliyense. Onetsetsani kuti wophunzirayo akumvetsa bwino zimene akuphunzira. Kwa anthu ambiri amene m’mbuyomo anaphunzirapo kale mabuku angapo koma sabwera kumisonkhano ya mpingo ndiponso safuna kusintha makhalidwe awo kuti agwirizane ndi choonadi cha m’Baibulo chimene anaphunzira, sikoyenera kuwayambitsa phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito buku limeneli.
3. Kodi tingatani ngati panopa tikuchititsa phunziro pogwiritsira ntchito buku la Lambirani Mulungu?
3 Ngati panopa mukuchititsa phunziro pogwiritsira ntchito buku la Lambirani Mulungu ndipo mwatsala ndi mitu yochepa kuti mumalize, zili ndi inu kusankha kumalizitsa bukulo ndi kumulimbikitsa wophunzirayo kuti awerenge buku la “Chikondi cha Mulungu” payekha. Koma ngati simunafike patali m’buku la Lambirani Mulungu, mungachite bwino kusiya ndi kuyamba buku latsopanoli. Monga mmene zilili ndi buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, mungasankhe nkhani za kumapeto zimene mungakambirane.
4. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati wophunzira wathu wabatizidwa asanamalize kuphunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani komanso buku la “Chikondi cha Mulungu”?
4 Ngati wophunzirayo wabatizidwa asanamalize kuphunzira mabuku awiriwa, muyenera kupitirizabe kuphunzira naye mpaka mutamaliza buku la “Chikondi cha Mulungu.” Ngakhale kuti wophunzirayo wabatizidwa, muyenera kuperekera lipoti nthawi, ulendo wobwereza ndi phunziro. Wofalitsa amene mungapite naye angawerengere nthawi ngati akutenga nawo mbali pa phunziropo.
5. Kodi buku la “Chikondi cha Mulungu” tingaligwiritsire ntchito motani kuti tithandize ofalitsa amene akhala asakulalikira kwa nthawi yaitali?
5 Ngati mwapemphedwa ndi m’bale wa mu Komiti ya Utumiki ya Mpingo kuti muphunzire ndi munthu amene anasiya kulalikira, angakusankhireni mitu yoti muphunzire naye m’buku la “Chikondi cha Mulungu.” Maphunziro ngati amenewa sayenera kuchititsidwa kwa nthawi yayitali. Buku latsopano limeneli ndi mphatso yamtengo wapatali, imene yakonzedwa kuti itithandize kukhalabe “m’chikondi cha Mulungu.”— Yuda 21.