Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndi mabuku awiri ati amene tiyenera kugwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu Baibulo?
Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi limene timaligwiritsa ntchito kwambiri poyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo. Ngakhale kuti sikulakwa kuyambitsa phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito zofalitsa zina, monga kapepala, tiyenera kuyesetsa kusintha mwamsanga n’kuyamba buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kuyambitsa maphunziro pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kwakhala ndi zotsatirapo zabwino kwambiri.
Tikamaliza kuphunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo wophunzirayo akupita patsogolo, tiyenera kuyamba kuphunzira naye buku la Lambirani Mulungu. (Akol. 2:7) Patsamba 2 la bukuli anafotokozapo cholinga chake. Anati: “Baibulo limalangiza onse amene amakonda Mulungu kuti azitha ‘kuzindikira . . . kukwera, ndi kuzama’ kwa mfundo za choonadi chake cha mtengo wapatali. (Aefeso 3:18, 19) Buku lino lakonzedwa kuti likuthandizeni kuchita zimenezo. Tikukhulupirira kuti lidzakuthandizani kuti mukule mwauzimu ndi kukhala okonzeka bwino kuyenda pa njira yopapatiza yopita ku moyo m’dziko latsopano lolungama la Mulungu.”
Ngati wophunzirayo wayenerera ubatizo asanamalize mabuku onse awiri, phunzirolo liyenera kupitirirabe mpaka atamaliza kuphunzira buku lachiwiri. Ngakhale kuti wophunzirayo wabatizidwa, wochititsa phunziroyo ayenera kuchitira lipoti maola, maulendo obwereza ndiponso phunzirolo. Wofalitsa wina amene angatsagane ndi wochititsa phunziroyo nayenso angawerengere maola.