Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tiziphunzira nthawi yotalika bwanji ndi wophunzira Baibulo amene akupita patsogolo?
Ndi bwino kwambiri kupitiriza kuphunzira Baibulo ndi wophunzira amene akupita patsogolo mpaka atamaliza buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndi lakuti, “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu.” Tizipitiriza kuphunzira naye ngakhale munthuyo atabatizidwa asanamalize kuphunzira mabuku awiriwa. Ngakhale atabatizidwa, tingapitirize kuchitira lipoti nthawi imene tachita naye phunziro, maulendo obwereza amene tachita ndiponso phunzirolo. Tikapita ndi wofalitsa wina ku phunzirolo, nayenso angawerengere nthawi ngati walankhulapo.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2009, tsamba 7.
Choonadi chiyenera kuzika mizu m’mitima ya anthu atsopano tisanasiye kuphunzira nawo. Ayenera kukhala “ozikika mozama” mwa Khristu ndiponso ‘okhazikika m’chikhulupiriro’ kuti athe kupirira mayesero amene adzakumane nawo. (Akol. 2:6, 7; 2 Tim. 3:12; 1 Pet. 5:8, 9) Komanso, kuti azitha kuphunzitsa anthu ena mogwira mtima, ayenera “kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Tikamaphunzira mabuku awiriwa ndi ophunzira athu mpaka kumaliza, timawathandiza kuti azitha kuyenda bwinobwino pa ‘msewu wopita ku moyo.’—Mat. 7:14.
Akulu asanavomereze munthu kuti abatizidwe, ayenera kutsimikizira kuti iye wamvetsetsa ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo ndipo akuzitsatira pa moyo wake. Akulu azisamala kwambiri povomereza wophunzira amene sanamalize kuphunzira buku loyamba. Ngati munthu sali woyenerera ubatizo, akulu azionetsetsa kuti munthuyo wathandizidwa kuti adzakhale woyenera kubatizidwa m’tsogolo.—Onani buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, tsamba 217 ndi tsamba 218.
[Mawu Otsindika patsamba 2]
Choonadi chiyenera kuzika mizu m’mitima ya anthu atsopano