Athandizeni Kuti ‘Akhazikike M’chikhulupiriro’
N’zosangalatsa kwambiri kuona kuti Yehova akudalitsa ntchito yathu yosonkhanitsa anthu, moti chaka chilichonse anthu oposa 250,000 amabatizidwa. (Deut. 28:2) Nthawi zambiri wofalitsa akathandiza wophunzira mpaka kubatizidwa, amaona kuti ayenera kusiya kuphunzira naye n’kuyamba kuthandizanso ena. Wophunzirayonso angaganize zosiya kuphunzira n’cholinga choti azipeza nthawi yambiri yochita utumiki. Komabe ndi bwino kuti wophunzira Baibulo akamasiya kuphunzira azikhala kuti wadziwa zambiri zokhudza choonadi. Ayenera ‘kuzikika’ mwa Khristu komanso ‘kukhazikika m’chikhulupiriro.’ (Akol. 2:6, 7; 2 Tim. 3:12) Choncho, wophunzira Baibulo akabatizidwa, ayenera kupitirizabe kuphunzira Baibulo mpaka atamaliza buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani komanso la “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu.”—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2011 tsamba 2.