Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/03 tsamba 4
  • Achinyamata—Konzani Maziko Abwino a Tsogolo Lanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achinyamata—Konzani Maziko Abwino a Tsogolo Lanu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Yosiya Anali ndi Anzake Abwino
    Phunzitsani Ana Anu
  • Yosiya Anachita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Yosiya Wodzichepetsayo Anayanjidwa Ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Yosiya Ankakonda Chilamulo cha Mulungu
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 9/03 tsamba 4

Achinyamata—Konzani Maziko Abwino a Tsogolo Lanu

1. Kodi n’chifukwa chiyani achinyamata achikristu akufunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba?

1 Kodi n’chiyani chimene mumada nacho nkhaŵa kwambiri? Kodi nthaŵi zambiri mukakhala mumaganiza za chiyani? Kodi maganizo anu nthaŵi zambiri amangokhala a zinthu zimene zilipo masiku ano, kapena kodi mumaganizanso za m’tsogolo, ndi zimene Mulungu walonjeza? (Mat. 6:24, 31-33; Luka 8:14) Pamafunika chikhulupiriro cholimba kuti munthu achite zinthu mogwirizana ndi malonjezo a Mulungu, monga momwe tikuonera pa chitsanzo cha Abrahamu ndi Mose. (Aheb. 11:8-10, 24-26) Kodi mungakhale bwanji ndi chikhulupiriro cholimba choncho kuti muthe kukonza “maziko okoma ku nyengo ikudzayi”?—1 Tim. 6:19.

2. Kodi chitsanzo cha Mfumu Yosiya chikutiphunzitsa chiyani?

2 Funafunani Yehova: Ndi chinthu chabwino kwambiri ngati inuyo ndi anthu a m’banja mwanu mumachitira limodzi zinthu zauzimu. Koma musaganize kuti kuchita zinthu zauzimu koteroko pakokha kungakupatseni chikhulupiriro cholimba. Kuti ‘mum’dziŵedi Mulungu,’ muyenera kufunafuna Yehova panokha. (Miy. 2:3-5; 1 Mbiri 28:9) Mfumu yachinyamata Yosiya anachita zimenezo. Ngakhale kuti panthaŵi imene amakula zinali zovuta kuti akule mwauzimu chifukwa cha malo amene amakhala, Yosiya ali ndi zaka 15 “anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake.”—2 Mbiri 34:3.

3. Kodi Akristu achinyamata masiku ano angafunefune bwanji Yehova?

3 Kodi mungafunefune bwanji Yehova? Mwa kusinkhasinkha mozama zimene mumakhulupirira ndi ‘kuzindikira, [‘kutsimikizira,’ NW]’ kuti chimenechidi ndi choonadi. (Aroma 12:2) Mwachitsanzo, kodi mungafotokoze zimene Baibulo limanena pankhani ya mwazi, kapena kodi mungapereke umboni wosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira kumwamba mu 1914? ‘Kuzindikira choonadi’ n’kofunika kwambiri pamene munthu akukonza maziko abwino a tsogolo lake.—1 Tim. 2:3, 4.

4. Kodi ofalitsa osabatizidwa angasonyeze bwanji kuti akupita patsogolo?

4 Yosiya atafunafuna Mulungu, zotsatirapo zake zinali zabwino. Asanakwanitse zaka 20, molimba mtima anachotsa kulambira konyenga m’dziko lake. (2 Mbiri 34:3-7) N’chimodzimodzinso ndi inuyo. Kupita patsogolo kwanu kwauzimu kudzaonekera mu zinthu zimene mumachita. (1 Tim. 4:15) Ngati ndinu wofalitsa wosabatizidwa, yesetsani kupita patsogolo mu utumiki wanu. Musangokhutitsidwa ndi kugaŵira mabuku. Khalani ndi cholinga chogwiritsa ntchito Baibulo, kukambirana ndi anthu, ndi kubwereranso kukaonjezera chidwi cha anthu amene mwakumana nawo. (Aroma 12:7) Zimenezi zidzakuthandizani kupita patsogolo mwauzimu.

5. Kodi Akristu obatizidwa ali ndi mwayi wotani woonjezera utumiki wawo?

5 M’patseni Yehova Zonse Zimene Mungathe: Mukasonyeza kudzipatulira kwanu kwa Yehova mwa kubatizidwa, mumakhala mtumiki woikidwa wa Mulungu. (2 Akor. 3:5, 6) Zimenezi zimakutsegulirani mwayi woti mutumikire Yehova mu utumiki wa nthaŵi zonse. Utumiki woterowo ndi monga upainiya, kutumikira pa Beteli, umishonale, ndi kutumikira ku mayiko akunja. Njira zinanso zoonjezera utumiki wanu ndi monga kuphunzira chinenero china kapena kusamukira ku dera limene kukufunika thandizo.

6. Kodi tonsefe tingakonze bwanji maziko abwino a tsogolo lathu?

6 N’zoona kuti si onse amene angathe kuchita nawo utumiki ngati umenewo, komabe aliyense wa ife angam’patse Yehova zonse zimene angathe. (Mat. 22:37) Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wanu, yesetsani kuti kutumikira Yehova kukhale chinthu choyamba nthaŵi zonse. (Sal. 16:5) Mukatero ndiye kuti mukukonza maziko abwino a tsogolo lanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena