Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 56 tsamba 134-tsamba 135 ndime 1
  • Yosiya Ankakonda Chilamulo cha Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yosiya Ankakonda Chilamulo cha Mulungu
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yosiya Anali ndi Anzake Abwino
    Phunzitsani Ana Anu
  • Yosiya Wodzichepetsayo Anayanjidwa Ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Mfumu Yabwino Yomaliza
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yosiya Anachita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 56 tsamba 134-tsamba 135 ndime 1
Safani akuwerengera Mfumu Yosiya mpukutu

MUTU 56

Yosiya Ankakonda Chilamulo cha Mulungu

Yosiya anayamba kulamulira ku Yuda ali ndi zaka 8. Pa nthawiyo, anthu ambiri ankakonda zamatsenga ndipo ankalambira mafano. Yosiya atakwanitsa zaka 16 anayesetsa kuphunzira za Yehova kuti azimulambira moyenera. Atakwanitsa zaka 20 anayamba kuphwanya mafano ndi kugumula malo onse amene anthu ankaperekerapo nsembe kwa mafanowo. Ndiyeno atakwanitsa zaka 26 anakonza zoti kachisi akonzedwenso.

Pokonza kachisiyo, mkulu wa ansembe dzina lake Hilikiya anapeza mpukutu wa Chilamulo cha Yehova. N’kutheka kuti umenewu unali mpukutu weniweni umene Mose analemba. Ndiyeno mlembi wa mfumu, dzina lake Safani, anatenga mpukutuwo kupita nawo kwa Yosiya n’kuyamba kumuwerengera mokweza. Yosiya atamva zimene zinali mumpukutuwo, anazindikira kuti anthu akhala asakumvera Yehova kwa zaka zambiri. Kenako anauza Hilikiya kuti: ‘Yehova watikwiyira kwambiri. Pitani mukalankhule naye kuti atiuze zoyenera kuchita.’ Yehova anayankha pogwiritsa ntchito mneneri wamkazi dzina lake Hulida ndipo anati: ‘Ayuda asiya kutsatira malamulo anga. Ndiwalanga ndithu. Koma sindichita zimenezi pa nthawi ya Yosiya chifukwa wadzichepetsa.’

Hilkiah finds the scroll containing Jehovah’s Law

Yosiya atamva zimenezi anapita kukachisi n’kuitanitsa Ayuda onse ndipo anawawerengera Chilamulo cha Yehova. Onse analonjeza kuti ayamba kumvera Yehova ndi mtima wonse.

Ayudawo anali atasiya kuchita Pasika kwa zaka zambiri. Koma Yosiya anamva m’Chilamulocho kuti iwo ayenera kuchita Pasika chaka chilichonse. Choncho anauza Ayudawo kuti: ‘Tiyeni tichitire Yehova Pasika.’ Yosiya anakonza zoti paperekedwe nsembe zambiri komanso kuti pakhale anthu oimba pakachisi. Ayudawo anachita Pasika ndipo kenako anachita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa kwa masiku 7. Panali pasanachitike Pasika ngati ameneyu chimwalirire Samueli. Izi zikusonyeza kuti Yosiya ankakonda kwambiri Chilamulo cha Yehova. Kodi iweyo umasangalala kuphunzira za Yehova?

“Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga, komanso kuwala kounikira njira yanga.”​—Salimo 119:105

Mafunso: Kodi Yosiya anatani atamva zimene zinali m’Chilamulo cha Mulungu? N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ankakonda Yosiya?

2 Mafumu 21:26; 22:1-20; 23:1-30; 2 Mbiri 34:1-33; 35:1-25

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena