36 YOSIYA
Anathandiza Anthu Kuti Ayambirenso Kulambira Yehova
YOSIYA anali ndi zaka 6 zokha pamene Mfumu Manase, omwe anali agogo ake, ankamwalira. Iye ayenera kuti ankadziwa kuti agogo akewa anasintha n’kuyambiranso kutumikira Yehova. Zimenezi ziyenera kuti zinamukhudza kwambiri Yosiya. Manase atamwalira, Amoni, yemwe anali bambo ake a Yosiya, anakhala mfumu. Amoni anali munthu woipa ndipo anachititsa kuti anthu ayambirenso kulambira mafano. Iye anamwalira atangolamulira zaka ziwiri zokha. Yosiya anakhala mfumu ndipo pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka 8.
Yosiya ayenera kuti anathandizidwa ndi anthu azitsanzo zabwino monga mneneri Zefaniya, mneneri Yeremiya, mneneri wamkazi Hulida komanso Mkulu wa Ansembe Hilikiya. Baibulo limati: “Akadali mnyamata, [pafupifupi zaka 16], Yosiya anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide kholo lake.” Ali ndi zaka pafupifupi 20, anayamba ntchito yothandiza anthu ku Yuda kuti ayambirenso kulambira Yehova. Yehova anagwiritsa ntchito mfumu yanzeru komanso yachinyamatayi kuthetsa kulambira mafano komanso zinthu zoipa zimene zinkachitika.
Yosiya anakafikanso mpaka kudera lomwe linkalamuliridwa ndi ufumu wakumpoto wa Isiraeli wa mafuko 10. Aisiraeli ambiri akumeneko anali atatengedwa n’kupita nawo ku ukapolo, ndipo anthu ambiri omwe ankakhala kuderali sanali Aisiraeli. Komabe Yosiya anaphwanya maguwa ansembe omwe anthuwa ankalambirirapo mafano.
Ngakhale kuti anali wachinyamata, Mfumu Yosiya analimba mtima n’kuthandiza anthu kuti ayambirenso kulambira Yehova
Patadutsa zaka zingapo, Yosiya anadalitsidwa m’njira imene sankayembekezera. Pamene anthu ankagwira ntchito yokonza kachisi wa Yehova, Mkulu wa Ansembe Hilikiya anapeza mpukutu wa Chilamulo chimene Yehova anapatsa Mose. Mpukutuwu unali wakale kwambiri, mwina wolembedwa ndi Mose. Anaupititsa kwa Yosiya ndipo iye ankamvetsera mwachidwi pamene unkawerengedwa mokweza. Zimene Yosiya anamva zinali zomvetsa chisoni. Anamvetsa bwino kuti anthuwo anali atasochera kwambiri pa nkhani yotsatira Chilamulo cha Mulungu. Yosiya anazindikira kuti machimo a anthuwo anali osawerengeka ndipo Yehova anawakwiyira kwambiri. Kodi Yosiya akanalimba mtima n’kuchita mogwirizana ndi zimene anamvazo?
Nthawi yomweyo, Yosiya anatuma anthu 5 kuti akafunsire kwa Yehova ndipo anapita kwa mneneri wamkazi dzina lake Hulida. Mneneriyu anawauza kuti Yehova analidi wokwiya chifukwa cha kusamvera kwa Ayuda ndipo tsoka linali kubwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu. Koma Yehova anaona kuti Yosiya anali munthu wabwino komanso wolimba mtima pa nkhani yolimbikitsa kulambira koona. Choncho ananena kuti sadzapereka chiweruzo pa nthawi ya mfumuyi.
Komabe Yosiya anapitiriza kuthandiza anthu ake kuti abwerere kwa Yehova. Iye ndi anthuwo anachita pangano kuti azitsatira Chilamulo cha Mulungu. Anakhazikitsa ntchito yowononga mafano onse m’dzikolo komanso kuthetsa kulambira kwabodza. Pofuna kulimbikitsa kulambira koona, anakonza chikondwerero cha Pasika. Yosiya ndi akalonga ake anapereka ziweto zambiri zoti ziperekedwe nsembe ndipo oimba anaimba nyimbo zotamanda Yehova. Chimenechi chinali chimodzi mwa zikondwerero zazikulu kwambiri za Pasika zomwe anthu a Mulungu anachita.
Yosiya anapitirizabe kusonyeza kulimba mtima komanso chikhulupiriro cholimba pamene ankathandiza anthu omwe kwa nthawi yaitali, sankatsatira malamulo a Mulungu. Pa nthawi ina, pamene anaphwanya limodzi la maguwa amenewa n’kuwotchapo mafupa a anthu, anakwaniritsa ulosi womwe unanenedwa zaka 300 m’mbuyomo. (1 Maf. 13:2) Ku Yuda, Yosiya anaphwanyanso maguwa ansembe amene anthu ankagwiritsa ntchito polambira mafano kuyambira nthawi imene Mfumu Solomo inasiya kutumikira Yehova mokhulupirika. Komabe pa nthawi ina, Yosiya sanasankhe zinthu mwanzeru. Anapita kuti akamenyane ndi Farao Neko wa ku Iguputo. Kudzera mwa Neko, Yehova anachenjeza Yosiya kuti asamenye nkhondoyo. Koma zikuoneka kuti Yosiya sanafunsire kwa aneneri kuti adziwe ngati zimene Neko ananena, zinalidi zochokera kwa Mulungu. M’malomwake anamenyabe nkhondoyo. Kumenyana ndi Neko ndi asilikali ake kukanaoneka ngati kulimba mtima, koma zoona zake ndi zoti kunali kuika moyo pangozi komanso kupanda nzeru. Moti zimenezi zinachititsa kuti Yosiya afe ali ndi zaka 39 zokha.
Kodi Yehova anaiwala zabwino zonse zimene Mfumu Yosiya anachita? Ayi ndithu. Mneneri Yeremiya analemba nyimbo yachisoni yonena za mfumu yabwinoyi. Zikuoneka kuti kwa zaka zambiri anthu a Mulungu ankaimba nyimboyi. Yosiya akadzaukitsidwa, n’kutheka kuti adzawerenga mawu ouziridwa amenewa okhudza ufumu wake komanso mawu omutamanda amunyimboyi. Apatu n’zoonekeratu kuti Yehova ankakonda Yosiya komanso sanaiwale kulimba mtima ndiponso chikhulupiriro chake.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Yosiya anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi tikudziwa zotani zokhudza Safani, yemwe anali wokopera malemba komanso mlembi wa Yosiya? (w02 12/15 19 ¶2-6)
2. N’chifukwa chiyani Yosiya anang’amba zovala zake pamene ankamuwerengera Chilamulo? (w14 4/15 32)
3. Mogwirizana ndi akatswiri a mbiri yakale, kodi Farao Neko anakhalakodi? (2 Mbiri 35:22; it “Neko[h]” ¶2-wcgr) A
StockStudio/Alamy Stock Photo
Chithunzi A: Ku Megido, kumene Yosiya anamenyana ndi Farao Neko
Chithunzi A: Ku Megido, komwe Yosiya anamenyana ndi Farao Neko
StockStudio/Alamy Stock Photo
4. Hulida analosera kuti Yosiya ‘adzaikidwa m’manda ake mwamtendere.’ Popeza Yosiya anafera kunkhondo, kodi ulosiwu unakwaniritsidwa bwanji? (2 Maf. 22:20; w00 9/15 30 ¶2-3-wcgr)
Zomwe Tikuphunzirapo
Akhristu ena analeredwa ndi makolo omwe sankalambira Mulungu, kodi angaphunzire chiyani kwa Yosiya yemwe bambo ake anali a mpatuko?
Yosiya anayesetsa kuti amvetse bwino Malemba. (2 Mbiri 34:21) Kodi tingamutsanzire bwanji? B
Chithunzi B
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Yosiya m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yosiya akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Ganizirani zomwe mukuphunzirapo pa zimene anasankha Yosiya komanso achinyamata ena awiri omwe anakhala mafumu a Yuda.
“Achinyamata, Kodi Mudzachita Chiyani pa Moyo Wanu?” (w23.09 8-13)
Kodi Yosiya anakwanitsa kuphwanya mafano ndi mphamvu zake? Pezani yankho muvidiyo iyi.