Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 37 tsamba 166-tsamba 169
  • ‘Sanadzidetse’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Sanadzidetse’
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • Ayesedwa—Koma Akhulupirikabe kwa Yehova!
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Buku la Danieli ndi Inu
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Yehova Amafupa Chikhulupiriro ndi Kulimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Danieli
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 37 tsamba 166-tsamba 169

37 DANIELI

‘Sanadzidetse’

Losindikizidwa
Losindikizidwa

DANIELI anatengedwa n’kupita naye kudziko lakutali. Banja lawo linali limodzi mwa mabanja ambiri omwe anatengedwa kwawo ku Yuda n’kupita nawo ku Babulo komwe kunali kutali, ulendo woyenda miyezi pafupifupi 4. Ali kumeneko, Danieli ndi achinyamata ena anawatenga n’kupita nawo kunyumba yachifumu moti sankakhalanso ndi anthu am’banja lawo. Danieli anayamba kugwirizana kwambiri ndi anyamata ena atatu a Chiheberi omwe anali Hananiya, Misayeli ndi Azariya. Ababulo anayamba kuphunzitsa anyamatawa nzeru za ku Babulo n’cholinga choti akhale ngati Ababulowo.

Danieli ali kutali ndi anthu am’banja lake, anakumana ndi mayesero amene akanachititsa kuti asakhale wokhulupirika

Mwachitsanzo, anyamatawa atangofika kunyumba yachifumu, Mfumu Nebukadinezara anauza Asipenazi, mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu, kuti awasinthe mayina. Mayina ambiri a Chiheberi anali otamanda Mulungu woona. Mwachitsanzo, dzina lakuti “Danieli” limatanthauza “Woweruza Wanga ndi Mulungu.” Koma mayina ambiri a Chibabulo ankatamanda milungu yawo. Choncho Danieli anapatsidwa dzina la Chibabulo lakuti Belitesazara. N’zodziwikiratu kuti dzinali linali mbali ya pemphero lopempha mulungu wabodza Beli kuti aziteteza moyo wa mfumu. Anawasinthanso mayinawa chifukwa choti mfumu inkafuna kuti anyamatawa aziganiza komanso kuchita zinthu ngati anthu a ku Babulo. Mfumuyi inalamulanso kuti Danieli ndi anzakewa aphunzitsidwe kulankhula ndi kulemba chilankhulo cha Akasidi kuti azikatumikira kunyumba yachifumu. Komatu si zokhazi.

Mfumu inasankha Asipenazi kuti aziyang’anira zonse zokhudza maphunziro a anyamatawa. Ankafunika kumadya chakudya cha mfumu komanso kumwa vinyo wabwino kwambiri. Mwina anyamata ena anaona kuti umenewu ndi mwayi wamtengo wapatali. Koma Danieli anaona kuti iyeyo ndi anzake atatu aja anafunika kukhala osamala kwambiri. Chifukwa chiyani?

Mwina Danieli anaganizira mfundo izi: ‘Ababulowa amadziwa kuti sitidya zakudya zina chifukwa chotsatira Chilamulo cha Yehova. Kodi akutipatsa chakudya chimene Yehova amaona kuti ndi chodetsedwachi n’cholinga choti atilepheretse kumumvera? Ngati angatipatse nyama, kodi izikhala yozinga bwino, kapena akufuna kutipusitsa kuti tiphwanye lamulo la Yehova loletsa magazi? Kapena kodi kudya chakudyachi ndi mbali imodzi ya kulambira mulungu wabodza? Komanso ngati angatipatse vinyo wambiri, kodi sangatilepheretse kuti tiziganiza bwino?’a

Danieli akulankhula ndi anzake atatu a Chiheberi m’chipinda chodyera cha kunyumba yachifumu. Asipenazi, mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu akuwayang’ana, pamene achinyamata ena akumwa vinyo, kudya nyama yankhumba komanso zakudya zina.

N’zosachita kufunsa kuti Danieli anapemphera kwambiri komanso anakambirana ndi anzakewo. Ndiye “anatsimikiza mumtima mwake” zoyenera kuchita kuti asangalatse Yehova. Kenako anapita kwa Asipenazi ndipo analankhula naye mwaulemu n’kumupempha kuti iye ndi anzake aja asamapatsidwe zakudya zomwe zingawadetse. Yehova anali ndi Danieli moti anachititsa kuti Asipenazi amukomere mtima. Komabe Asipenazi anada nkhawa kuti mwina zimenezi zingachititse kuti Danieli ndi anzakewo asakhale athanzi. Ankadziwa kuti ngati zimenezi zitachitika, Nebukadinezara adzamuimba mlandu. Danieli sanachite makani. Koma kenako molimba mtima anafotokozera pulani yake munthu amene Asipenazi anamuika kuti aziwayang’anira. Anamuuza kuti awalole kuti kwa masiku 10 azingodya zakudya zamasamba ndiponso kumwa madzi okha kenako adzayerekezere mmene iwowo akuonekera ndi mmene anyamata enawo akuonekera. Munthu amene ankawayangʼanirayo anavomera.

Patatha masiku 10, anyamata 4 amenewa ankaoneka bwino kwambiri kuposa ena onse. Ndipotu ankaoneka athanzi kwambiri moti anawalola kuti apitirize kudya zakudya zomwezo. N’zoonekeratu kuti Yehova anadalitsa Danieli ndi anzakewo chifukwa cha chikhulupiriro komanso kulimba mtima kwawo. Iwo sanaiwale zimene zinawachitikirazi.

Monga tionere m’mutu wotsatira, patapita nthawi anzake a Danieli atatu aja anakumana ndi mayesero ndipo ankafunika kuchita zinthu molimba mtima. Danieli anakhala ndi moyo zaka 100 ndipo nayenso anakumana ndi mayesero moti ankafunikanso kulimba mtima. Pa nthawi ina, anayenera kumasulira maloto omwe Yehova analotetsa Nebukadinezara, ngakhale kuti malotowo ankalosera zinthu zoipa zokhudza mfumu yodzikuzayi ndi ufumu wake. Pa nthawi ya Mfumu Belisazara, Danieli anamasulira mawu omwe analembedwa pakhoma ngakhale kuti uthenga wake unali wotsutsa mfumuyo. Atakalamba, anaponyedwa m’dzenje la mikango yolusa. Pa nthawi yonseyi, Danieli anasonyeza kulimba mtima ngati mmene ankachitira ali mnyamata. N’chifukwa chake mngelo wa Yehova anatchula Danieli kuti “munthu wokondedwa kwambiri.”

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Danieli 1:​1-21; 5:12; 10:11

Funso lokambirana:

Kodi Danieli anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Kodi lemba la Danieli 1:1 limatsutsana ndi la Yeremiya 25:1? (dp 18-19 ¶14-15)

  2. 2. Kodi zolemba za ku Babulo zimatsimikizira bwanji kuti kunalidi ‘nyumba yosungiramo chuma ya mulungu [wa Nebukadinezara]’? (Dan. 1:2; it “Chuma” ¶3-wcgr) A

    © The Trustees of the British Museum. Licensed under CC BY-NC-SA 4.0. Source. Modifications: Box added

    Chithunzi A: Zolemba za Nebukadinezara zotchula ‘nyumba yosungiramo chuma’ m’kachisi wa Merodaki

  3. 3. Kodi ‘ansembe ochita zamatsenga’ anali ndi udindo wotani? (Dan. 1:20; it “Matsenga Komanso Kulosera” ¶2-6-wcgr) B

    Chithunzi B: Mwala wa ku Babulo pamene panalembedwa mawu ofotokoza mmene “angachiritsire” munthu woganiziridwa kuti wagwidwa ndi chiwanda

  4. 4. Kodi zakudya zamasamba zimene ankapatsa Danieli ndi anzake ziyenera kuti zinkaphatikizapo zinthu ziti? (Dan. 1:12; dp 40 ¶25)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Kodi achinyamata angaphunzire chiyani kwa Danieli pa nkhani yokhala okhulupirika ngakhale pamene sali ndi anthu am’banja lawo?

  • Kodi ‘kutsimikiziratu mumtima mwake’ kunathandiza bwanji Danieli kukhala wolimba mtima? (Dan. 1:8) Nanga tingamutsanzire bwanji? C

    Zithunzi: 1. Mlongo woyembekezera akugwiritsa ntchito Baibulo, tabuleti, khadi la DPA komanso kope pofufuza mfundo zomuthandiza kukonzekera kubadwa kwa mwana wake. 2. Kenako iye ndi mwamuna wake ali muofesi mwa adokotala ndipo akufotokoza zimene amakhulupirira zokhudza kuikidwa magazi. Adokotala akumumvetsera, uku akuyang’ana khadi lake lija.

    Chithunzi C

  • Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Danieli m’njira zinanso ziti?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Danieli akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Onerani vidiyo ya nkhani ya m’Baibulo.

Danieli Anali Munthu Wachikhulupiriro Cholimba—Mbali Yoyamba—Kachigawo Kake (13:07)

Kodi masiku ano achinyamata angatsanzire bwanji Danieli pa nkhani ya kulimba mtima komanso kukhulupirika?

“Muziphunzira pa Chitsanzo cha Danieli” (w23.08 2-7)

a Onani Ekisodo 34:15; Levitiko 7:26; 11:​1-7; Numeri 25:2; Miyambo 20:1.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena