38 AHEBERI ATATU
“Sanapse Ndi Moto”
HANANIYA, Misayeli ndi Azariya ankakhala ku Babulo ndipo Ababulowo anawapatsa mayina akuti Shadireki, Misheki ndi Abedinego. Pa nthawi ina, iwo anakumana ndi mayesero ndipo ankalakalaka Danieli, yemwe anali mnzawo kwambiri komanso anali ndi chikhulupiriro cholimba, akanakhalapo.
Mayeserowa anayamba pamene Nebukadinezara anapanga fano lalikulu kwambiri. Linali lalitali pafupifupi mamita 27 ndipo m’mbali mwake linali pafupifupi mamita atatu. Mfumuyo inakonza mwambo wotsegulira fanolo ndipo inkafuna kuti akuluakulu onse a boma apezekepo. Aheberi atatu aja anamvera lamulo la mfumuli ndipo anapezeka pamwambowu.
Mmodzi wa atumiki a mfumu anauza anthuwo zoyenera kuchita. Anawauza kuti choyamba amva kulira kwa nyimbo. Mfumu inakonza zoti pakhale nyimbo pofuna kupangitsa anthu kuti achite zimene inkafuna. Kenako anthu ankafunika ‘kugwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo kufika pansi kulambira fanolo.’ Anyamata atatuwa ankadziwa bwino lamulo la Yehova loletsa kulambira mafano. (Eks. 20:4, 5) Ndiye kodi iwo akanatani?
Pagulu lalikulu la anthu, anaopsezedwa kuti aphedwa ngati salambira fano
Nyimbo zinayamba. Kenako anthu onse anagwada n’kuyamba kulambira fanolo. Koma anyamata atatu aja anangoima ndipo n’zosachita kufunsa kuti anthu onse anawaona. Anthu ena anakauza Nebukadinezara kuti: “Iwo sakukumverani inu mfumu ndipo sakutumikira milungu yanu moti akukana kulambira fano lagolide limene mwaimika.” Choncho mfumuyo inaitanitsa anyamata atatuwo, ndipo mokwiya inawafunsa ngati zinalidi zoona. Koma asanayankhe, anayamba kuwaopseza. Anawauza kuti awapatsa mpata woti amvere ndipo akapanda kumvera ‘nthawi yomweyo aponyedwa mungʼanjo yoyaka moto.’ Anawauzanso kuti palibe mulungu amene angawapulumutse.
Koma anyamata atatu onsewa anali atatsimikiza mtima kuti akhalabe okhulupirika kwa Yehova. Moti anauza mfumu kuti ngati ‘angawaponyere mungʼanjo yoyaka moto,’ Mulungu wawo adzawapulumutsa. Anawonjezera kuti: “Koma ngakhale atapanda kutipulumutsa, dziwani mfumu kuti ife sititumikira milungu yanu kapena kulambira fano lagolide limene mwaimika.” Nebukadinezara anakwiya kwambiri. Analamula kuti ng’anjoyo aisonkhezere kwambiri kuposa mmene ankachitira nthawi zonse, kenako amange anyamatawo n’kuwaponyamo. Ng’anjoyo inatentha kwambiri moti anthu amene ankaponyamo anyamatawa anafa ndi malawi a moto.
Koma kenako Nebukadinezara anaona zodabwitsa. Atasuzumira mung’anjomo anaona anthu 4 osati atatu. Ankayendayenda pamotowo koma osapsa. Ponena za munthu wa 4, mfumu inanena kuti “akuoneka ngati mwana wa milungu.” Mfumuyo inayandikira ng’anjoyo n’kuuza anyamatawo kuti atuluke.
Taganizirani mmene anthu anadabwira ataona anyamata atatuwo atatuluka osapsa. Zovala zawo komanso matupi awo anali bwinobwino ndipo sankamveka ngakhale fungo la utsi. Maunyolo awo okha ndi amene anaduka. Nebukadinezara, yemwe anali mfumu yamphamvu, anadabwa kwambiri. Anayamikira Aheberi atatuwo chifukwa chomvera Mulungu wawo. Iye ananena kuti iwo “anamudalira ndipo sanamvere lamulo la mfumu, moti anali okonzeka kufa m’malo motumikira kapena kulambira mulungu wina aliyense kupatulapo Mulungu wawo.”
Mfumuyi inalamula kuti aliyense mu ufumu wake amene anganene zinthu zotsutsana ndi Yehova aziphedwa. Komanso anakweza pa udindo anyamata atatuwo. Koma Yehova anawachitira zoposa pamenepo, sanawaiwale. Mwachitsanzo, patatha zaka zambiri, Yehova anauzira mtumwi Paulo kuti alembe za anthu amene “sanapse ndi moto” chifukwa choti anali ndi chikhulupiriro cholimba. Ayenera kuti ankaganizira za Hananiya, Misayeli ndi Azariya.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Hananiya, Misayeli ndi Azariya anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi zimene ofukula zinthu zakale anapeza zimasonyeza bwanji kuti nkhani ya mu Danieli chaputala 3 ndi yolondola? (w23.07 31) A
© The Trustees of the British Museum. Licensed under CC BY-NC-SA 4.0. Source. Modifications: Box added
Chithunzi A: Njerwa yomwe panalembedwa dzina la Nebukadinezara
2. Kodi n’kutheka kuti mayina amene Ababulo anapatsa Aheberi atatu aja amatanthauza chiyani? (dp 36 ¶14)
3. N’chiyani chikusonyeza kuti Nebukadinezara ankakonda zachipembedzo? (dp 69 ¶3) B
Chithunzi B: Nebukadinezara anamanga ndi kukonzanso akachisi a milungu yambirimbiri ya Ababulo
4. N’chifukwa chiyani “anthu a mitundu yosiyanasiyana komanso olankhula zinenero zosiyanasiyana,” omwe mwinanso anali ndi milungu yawo, sanadandaule atauzidwa kuti alambire fano la Nebukadinezara? (Dan. 3:7; dp 73 ¶10)
Zomwe Tikuphunzirapo
Aheberi atatu aja anakhala okhulupirika atayesedwa pa nkhani ya zakudya. Patapita nthawi anakhalanso okhulupirika ataopsezedwa kuti aphedwa. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani pa nkhani yokhala okhulupirika pa zinthu zooneka ngati zazing’ono? (Luka 16:10) C
Chithunzi C
Tikamazunzidwa, kodi tingatsanzire bwanji Aheberi atatu aja pa nkhani yosonyeza makhalidwe otsatirawa? (Dan. 3:16-18)
Kudzichepetsa
Kufatsa
Kukhulupirika
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Aheberi atatuwa m’njira ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Hananiya, Misayeli komanso Azariya akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi Mkhristu angasonyeze bwanji ulemu koma osatenga nawo mbali pamene anthu akuchita mwambo wosonyeza kukhulupirika ku dziko lawo?
Tisamachite Zinthu Zosonyeza Kuti Tili Mbali ya Dziko Tikakhala Pagulu (4:25)
Yerekezerani kuti mukuona zimene zikuchitika ndipo ganizirani mfundo zina zimene mukuphunzirapo.
“Anapulumutsidwa Mung’anjo Yamoto” (Nkhani zapawebusaiti, “Zoti Muchite Pophunzira Baibulo”)