Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 39 tsamba 176-tsamba 179
  • “Ngati Nʼkufa, Ndife”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ngati Nʼkufa, Ndife”
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Phunzirani Zambiri
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 39 tsamba 176-tsamba 179

39 ESITERE

“Ngati Nʼkufa, Ndife”

Losindikizidwa
Losindikizidwa

MTSIKANA wina dzina lake Esitere ankayenda pabwalo la nyumba yachifumu ndipo ankalowera komwe mfumu inakhala. Iye ankadziwa kuti akhoza kuphedwa chifukwa chokaonekera kwa mfumuyo asanaitanidwe. Ankachita mantha komabe anapitiriza ulendo wake. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti achite zimenezi?

Makolo a Esitere anamwalira iye ali wamng’ono ndipo wachibale wake, dzina lake Moredikayi, “anamʼtenga nʼkumakhala naye ngati mwana wake.” Moredikayi anali wamkulu kwambiri kuyerekeza ndi iyeyo. Iwo ankakhala mumzinda wa Susani. Mfumu ya Perisiya inkakhalanso mumzindawu ndipo Moredikayi ankagwira ntchito kunyumba yachifumu. Esitere “anali wooneka bwino ndiponso wokongola kwambiri.”

Tsiku lina Mfumu Ahasiwero (yemwe ayenera kuti anali Sasita Woyamba) anaganiza kuti asankhe mkazi wina. Choncho anthu anayamba kufufuza anamwali okongola mu ufumu wonsewo. Anthuwo anaona kuti Esitere anali wokongola ndipo anapita naye kunyumba ya mfumu. Koma asanamutenge, Moredikayi “anali atamulangiza kuti asauze aliyense” zoti ndi Myuda.

Esitere atafika kunyumba yachifumu, ‘aliyense womuona ankamukonda.’ Miyezi 12 imene anakonza kuti amukongoletse itatha, anapita naye kwa mfumu. Mfumuyo “inakonda kwambiri Esitere” ndipo inasankha iyeyo. Choncho anakhala mkazi wa mfumu yamphamvu padziko lonse. Koma Esitere anapitiriza kumvera malangizo a Moredikayi akuti asauze aliyense zoti ndi Myuda.

Pa nthawiyi, mfumu inasankha munthu wina dzina lake Hamani kuti akhale wachiwiri wake. Hamani ankadana kwambiri ndi Moredikayi chifukwa choti ankakana kumuweramira. Moredikayi ankakana chifukwa choti anali mtumiki wa Yehova wokhulupirika. Zikuoneka kuti Hamani anali wochokera mumtundu umene Yehova ankauona kuti ndi adani ake. Kaya Moredikayi ankakanadi pa chifukwa chimenechi kapena ayi, Hamani anakwiya koopsa. Choncho anakonza zopha Moredikayi komanso Ayuda onse omwe ankakhala mu ufumuwu. Moredikayi atadziwa zimenezi, anamva chisoni kwambiri. Moti anatumiza uthenga kwa Esitere womuuza kuti apite kwa mfumu kukaipempha kuti ipulumutse Ayuda. Amenewatu anali mayesero aakulu kwa Esitere.

Esitere anauza Moredikayi kuti ngati angapite kwa mfumu asanaitanidwe, akhoza kuphedwa. Mfumuyi inkadziwika kuti inali yosachedwa kupsa mtima. Komabe Moredikayi anamulimbikitsa pomukumbutsa kuti n’kutheka kuti anakhala mfumukazi n’cholinga choti adzateteze anthu a Yehova. Choncho Esitere analimba mtima moti ananena kuti: “Ngati nʼkufa, ndife.” Iye anangopempha kuti Ayuda asale kudya kwa masiku atatu. N’zosakayikitsa kuti iye anapemphera kambirimbiri komanso Ayuda ankamupempherera. Kenako anapita kwa mfumu.

Mfumukazi Esitere akupemphera chamumtima pakhomo la nyumba yachifumu. Iye waima pamalo omwe Mfumu Ahasiwero yemwe wakhala pampando wake wachifumu sakumuona. Alonda ena akunyumba yachifumu akumuyang’ana pamene iye akupemphera.

Ahasiwero ataona Esitere ataima m’bwalo la nyumba ya mfumu sanakwiye ndipo sanalamule kuti aphedwe. M’malomwake anamufunsa chomwe ankafuna. Poyankha, Esitere anaitanira mfumuyo komanso Hamani kuphwando lomwe anawakonzera. Kuphwandoko anachita zinthu mosamala komanso mwanzeru. Sananene zoti Hamani anali ndi pulani yopha Ayuda. Koma anangoitana mfumu ndi Hamani kuti abwerenso kuphwando lina tsiku lotsatira. Pa nthawiyi, Hamani anapitiriza kukonza chiwembu choti Moredikayi apachikidwe pamtengo. Koma zimenezi zinangochititsa kuti iyeyo akumane ndi mavuto pambuyo pake.

Ankafunika kulankhula mwanzeru kwa mwamuna wake kuti mwamuna wakeyo, yemwe anali mfumu yamphamvu, apulumutse anthu a Mulungu

Paphwando lachiwirilo, Ahasiwero anafunsanso Esitere chimene ankafuna. Pa nthawiyi ananena zomwe ankafuna. Mwaulemu, Esitereyo anauza mfumu kuti munthu wina wakonza chiwembu choti aphe anthu amtundu wake. Iye ananena kuti sakanalankhulapo, zikanakhala kuti chiwembuchi sichibweretsa mavuto kwa mfumuyo. Modabwa, Ahasiwero anafunsa kuti: “Wachita zimenezo ndi ndani?” Esitere anauza mfumuyo kuti anali Hamani. Mfumuyo inakwiya kwambiri ndipo inalamula kuti Hamani apachikidwe pamtengo. Mtengo umene Hamani anapachikidwapo ndi umene iyeyo anakonzera Moredikayi.

Hamani ankayembekezera kuti Moredikayi komanso anthu onse a Mulungu omwe anali mu ufumu wa Perisiya, aphedwa. Koma iyeyo, anthu amtundu wake ndiponso adani ambiri a Yehova ndi amene anaphedwa. Apatu Yehova anagwiritsa ntchito mtsikana wolimba mtimayu komanso wachikhulupiriro populumutsa anthu ake.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Esitere 1:1–9:​1, 5, 13-17

Funso lokambirana:

Kodi Esitere anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Kodi pali umboni wotani wa m’mbiri yakale wosonyeza kuti nkhaniyi ndi yolondola? (ia 138, bokosi) A

    Ungnad, Arthur. “Neubabylonische Privaturkunden aus der Sammlung Amherst.” Archiv für Orientforschung, vol. 19, 1959, pp. 74–82

    Chithunzi A: Mwala wakalekale wa ku Perisiya, pomwe pali dzina la Marduka (Moredikayi)

  2. 2. N’kutheka kuti n’chiyani chinachititsa Moredikayi kuti asamaweramire Hamani? (ia 131 ¶18)

  3. 3. N’chiyani chikusonyeza kuti Satana ndi ziwanda zake ankafuna kuwononga Ayuda onse? (g02 9/8 23 ¶3–24 ¶2) B

    Cube. Lot of Yahali, puru. Neo-Assyrian Clay. (YPM BC 021122). Courtesy of the Peabody Museum, Division of Anthropology, Babylonian Collection, Yale University; peabody.yale.edu

    Chithunzi B: Kanthu kakale komwe ankachitira maere

  4. 4. Kodi ndi ulosi uti umene Esitere ndi Moredikayi anathandiza nawo kuti ukwaniritsidwe? (ia 142, bokosi)

Phunzirani Zambiri

  • Esitere anali wanzeru komanso womvera ngakhale pamene anali kutali ndi Ayuda anzake. Kodi achinyamata masiku ano angaphunzire chiyani kwa Esitere?

  • Mwamuna wa Esitere anamvera zimene Esitereyo ananena chifukwa analankhula moleza mtima, mwaluso komanso moona mtima. Kodi alongo angamutsanzire bwanji? C

    Mlongo akulankhula ndi mwamuna wake yemwe si wa Mboni pamene akumwa khofi uku akuotha moto. Mlongoyo watenga Baibulo lotsegula ndipo akuloza chilengedwe chokongola.

    Chithunzi C

  • Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Esitere m’njira zinanso ziti?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Esitere akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Munyimbo yotsatirayi, onani zimene ana angaphunzire kwa Esitere.

Esitere Anali Wolimba Mtima (2:09)

Kodi abale ena masiku ano anatsanzira bwanji Esitere pa nthawi imene Akhristu anzawo ankafunika kutetezedwa?

Muzitsanzira Anthu Amene Anadalitsidwa Chifukwa cha Kuleza Mtima—Moredekai ndi Esitere (3:05)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena