Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira November 10
Mph. 7: Zilengezo za pampingo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 18: “Khalani Okonzekeratu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kufotokoza zomwe zimawathandiza kuti nkhaŵa ndiponso zopinga za moyo uno zisawawonongere nthaŵi yomwe angaigwiritse ntchito bwino pa zinthu zauzimu.
Mph. 20: Kodi Mumasankha Motani Anthu Ocheza Nawo? Kukambirana ndi omvera mfundo za m’buku la Lambirani Mulungu, masamba 47-9. Mwa kugwiritsa ntchito mafunso ndi malemba osagwidwa mawu a m’ndime 13, pemphani omvera kufotokoza mfundo za m’Baibulo zomwe tiyenera kutsatira posankha anthu ocheza nawo.
Nyimbo Na. 127 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 17
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Funsani ofalitsa aŵiri kapena atatu omwe apeza zotsatira zabwino mu utumiki wa kumunda pogwiritsa ntchito buku limene tikugaŵira panopo. N’kutheka kuti ena ayambitsa maphunziro a Baibulo.
Mph. 15: Khalani ndi Mtima Wopatsa. Nkhani yokambidwa ndi mkulu, kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2003, masamba 27-30.
Mph. 18: “Kuyamikiridwa Kumalimbikitsa.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo mfundo za m’buku la Chimwemwe cha Banja, masamba 49-50, ndime 21. Pemphani ndemanga zachidule kuchokera kwa anthu omwe analimbikitsidwa anthu ena atawayamikira.
Nyimbo Na. 58 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 24
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Khalani ndi zitsanzo ziŵiri za zinthu zomwe zingachitikedi zosonyeza mmene mungagwiritsire ntchito mfundo za patsamba 4 pogaŵira Nsanja ya Olonda ya November 15 ndi Galamukani! ya November 8 m’gawo lanu. M’zitsanzo zonse ziŵirizo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana. M’chitsanzo chimodzi afotokoze kumene kumachokera ndalama zoyendetsera ntchito yathu ya padziko lonse.—Onani Nsanja ya Olonda, tsa. 2, kapena Galamukani! tsa. 5.
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambidwa ndi mkulu.
Mph. 23: “Kupanga Ubwenzi Wolimba ndi Yehova.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Pemphani omvera kuti anene mmene malembawo akugwirira ntchito. Konzeranitu zoti munthu mmodzi kapena aŵiri afotokoze zimene zawathandiza kukonza phunziro lawo la Baibulo laumwini kuti likhale labwino kwambiri.
Nyimbo Na. 202 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 1
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a November. Tchulani mabuku ogaŵira mu December. Khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za patsamba 4 pogaŵira Nsanja ya Olonda ya December 1 ndi Galamukani! ya November 8. Angagwiritse ntchito lemba lina osati lomwe laperekedwa patsamba 4. M’zitsanzo zonse ziŵirizo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana. M’chitsanzo chimodzi sonyezani kugaŵira magazini mwamwayi pa zoyendera za anthu onse kapena m’malo ena mogwirizana ndi kwanuko.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: Odziŵa Kuphunzitsa Ena. Kukambirana ndi omvera mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 2000, masamba 16-17, ndime 9-13. Cholinga chachikulu mu utumiki wathu ndicho kuphunzitsa mogwira mtima. Kuti tithe kuthandiza bwino anthu onga nkhosa zikudalira luso lathu lofotokoza uthenga wa Ufumu moti iwo azindikire ndi kuwalimbikitsa kuchitapo kanthu. Kambiranani mafunso aŵa: (1) Kodi kulalikira kumasiyana bwanji ndi kuphunzitsa? (2) N’chifukwa chiyani ena amachita mantha kuchititsa phunziro la Baibulo? (3) Kodi tingakulitse motani luso lathu la kuphunzitsa? (4) Kodi tingatani kuti titsimikize kuti munthu amene tikuphunzira naye akumvetsa zimene akuphunzirazo? (5) Kodi tiyenera kuyesetsa kuthandiza wophunzirayo kukwaniritsa cholinga chotani?
Nyimbo Na. 70 ndi pemphero lomaliza.