Tingawathandize Bwanji Osakhulupirira Amene Ali Pabanja ndi Mboni?
1 Amuna kapena akazi a atumiki ambiri a Yehova amakhala ochezeka kwa abale ndipo amachita chidwi ndi mpingo koma safuna kukhala atumiki a Mulungu. Mwamuna wina wotero anati: “Nkhani yopita kunyumba ndi nyumba inali kundivuta kwambiri.” Ena angakhale ndi zizoloŵezi zotsutsana ndi Malemba zimene afunikira kusiya, kapena angaganize kuti sangakwanitse kuchita zinthu zauzimu zochuluka zimene mwamuna kapena mkazi wawo amachita. Kodi tingawathandize bwanji?
2 Asonyezeni Chidwi: Ngati tichita chidwi ndi anthu ena ndi kuzindikira zimene zimawadetsa nkhaŵa, iwo angathe kulandira choonadi cha m’Baibulo. (Afil. 2:4) Nthaŵi zambiri anthu amene kale chikhulupiriro chawo chinali chosiyana ndi cha mwamuna kapena mkazi wawo amasimba za chikondi chimene ena anawaonetsa. Mwachitsanzo, mwamuna tatchula poyamba uja anafotokoza kuti: “José, mkulu mu mpingo, anandionetsa chidwi chapadera. Ndikukhulupirira kuti ndinayamba kuphunzira mwakhama chifukwa cha kundilimbikitsa kwake.” Mwamuna wina anafotokoza kuti abale amene anali kum’chezera anayesetsa kukambirana naye zimene iye amakonda. Iye anati: “Ndinayamba kuona chipembedzo [cha mkazi wanga] mosiyana kwambiri ndi kale. Anzake anali anthu anzeru kwambiri ndipo anatha kulankhula za nkhani zosiyanasiyana.”—1 Akor. 9:20-23.
3 Athandizeni: Anthu osakhulupirira amene ali pabanja ndi Mboni angakopekenso chifukwa chowathandiza mokoma mtima. (Miy. 3:27; Agal. 6:10) Pamene galimoto ya mwamuna wina wosakhulupirira inawonongeka, mnyamata wina wa Mboni anam’thandiza. “Zimenezi ndinachita nazo chidwi kwambiri,” iye anatero. Mbale wina anatenga tsiku lonse kuthandiza mwamuna wosakhulupirira wa mlongo wina kumanga mpanda wa nyumba yake. Mmene amagwira ntchito ndi kukambirana, ubwenzi wawo unalimba. Patapita milungu iŵiri, mwamunayo anapita kwa mbaleyo ndi kumuuza kuti: “Nthaŵi yakwana tsopano yakuti ndisinthe zina n’zina pamoyo wanga. Kodi mungandiphunzitse Baibulo?” Mwamuna ameneyu anafulumira kupita patsogolo ndipo tsopano ndi Mboni yobatizidwa.
4 Mmene tikufunafuna oyenerera m’gawo lathu, tisaiwale kufikira anthu amene ali pabanja ndi okhulupirira anzathu.—1 Tim. 2:1-4.