Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira January 12
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 15: “Phindu Ndiponso Kupambana kwa Nzeru ya Mulungu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ngati nthaŵi ilola, pemphani omvera kuperekapo ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.
Mph. 22: Mabuku Atsopano Amene Tinasangalala Kuwalandira! Kukambirana ndi omvera. Tinasangalala kwambiri kulandira mabuku atsopano aŵiri pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Patsani Mulungu Ulemerero.” Buku lakuti ‘Onani Dziko Lokoma’ likusiyana ndi mabuku ena onse amene tili nawo. Mukatsegula tsamba lililonse, mumaona mbali inayake yopatsa phunziro kwambiri ya Dziko Lolonjezedwa. Tchulani zina mwa zinthu zimene zili pa mapu osiyanasiyana. Nenani njira zogwiritsira ntchito bukuli zimene abale angathe. Buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso lidzalimbitsa moyo wauzimu wa ana athu. Tchulani nkhani zina za panthaŵi yake zimene bukulo likufotokoza, kusonyeza phindu limene makolo ndi ana awo angapeze. Pemphani omvera kufotokoza zimene akuchita pofuna kugwiritsa ntchito bwino mabuku ameneŵa.
Nyimbo Na. 186 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 19
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambidwa ndi mkulu.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 15: “Tingawathandize Bwanji Osakhulupirira Amene Ali Pabanja ndi Mboni?” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Funsani munthu mmodzi kapena aŵiri amene anakhala atumiki a Yehova chifukwa cha chitsanzo chabwino chimene anaona kwa mnzawo m’banja amene anali atalandira choonadi.
Nyimbo Na. 73 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 26
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti a utumiki wa kumunda a January. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 4, sonyezani zitsanzo za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya January 15 ndi Galamukani! ya January 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi, ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana. Akamaliza chitsanzo, tchulani mbali zothandiza za chitsanzocho.
Mph. 15: Tsatirani Mawu a Mulungu pa Moyo Wanu Tsiku Lililonse. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Limbikitsani onse kugwiritsa ntchito bwino kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2004. Kambiranani ndemanga zotengedwa pa mawu oyamba, masamba 3 mpaka 4. Pemphani omvera anene nthaŵi imene iwo amaiona kukhala yabwino kukambirana lemba la tsiku. Kambiranani ndi mpingo lemba ndi ndemanga za tsikulo. Pemphani omvera afotokoze mmene tingagwiritsire ntchito mfundozo. Alimbikitseni onse kuti akamakambirana lemba la tsiku, azionanso mmene angagwiritsire ntchito mfundozo pa moyo wawo.
Mph. 18: Kupanga Ubwenzi ndi Okhulupirira Anzathu. (Miy. 18:24; 27:9) Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Yachokera mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2000, masamba 22 mpaka 23. Madalitso ena amene timapeza pa kulambira koona ndiwo mwayi wokhala ndi mabwenzi enieni. Kuyanjana kwathu pamisonkhano, mu utumiki wa kumunda, ndi panthaŵi zina kumatilimbikitsa kwambiri. Kodi tingachite chiyani kuti tikhale ndi mabwenzi mumpingo? Kambiranani bokosi lakuti “Njira Zisanu ndi Imodzi Zopezera Mabwenzi Okhalitsa,” ndipo pemphani omvera afotokoze mmene tingagwiritsire ntchito mfundozo, imodzi ndi imodzi, pamene tili ndi abale athu.
Nyimbo Na. 177 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 2
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Tchulani mabuku ogaŵira mu February. Pendani maulaliki amene tingagwiritse ntchito pogaŵira buku la Yandikirani kwa Yehova amene ali mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2003, tsamba 3. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 4, sonyezani zitsanzo za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya February 1 ndi Galamukani! ya January 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi, ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana. Chimodzi mwa zitsanzozo chisonyeze mmene mungagaŵire magazini kwa munthu amene mumakhala naye pafupi.
Mph. 15: “Penyani Bwino Mmene Mumagwiritsira Ntchito Nthaŵi Yanu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera anene zimene amachita kuti asalole zinthu zosafunika kwenikweni kudodometsa zinthu zauzimu.
Mph. 15: Tsanzirani Paulo Monga Iye Anatsanzira Kristu. (1 Akor. 11:1) Kukambirana ndi omvera. Mofanana ndi Yesu, Paulo anagwiritsa ntchito mipata imene anapeza kulalikira kwa “iwo amene anakomana nawo.” (Mac. 17:17) Kodi ndi mipata yotani m’gawo lathu imene timakhala nayo yochitira zimenezi? Kodi ndani amene ‘timakumana nawo’ tikapita kokagula zinthu, kuntchito kapena kusukulu, kapenanso tikakwera basi? Kodi ndani amene tingaonane naye tili panyumba pathu? Pemphani omvera kusimba zimene akumana nazo polalikira anthu amene anakumana nawo pa zochitika za masiku onse.
Nyimbo Na. 151 ndi pemphero lomaliza.