Phindu Ndiponso Kupambana kwa Nzeru ya Mulungu
1 Anthu ena amaganiza kuti Mboni za Yehova ziyenera kulimbikira kwambiri kuthandiza anthu kuthetsa mavuto amene akukumana nawo lerolino. Anthu ngati amenewo saona kupambana kwa ntchito yathu yophunzitsa anthu Baibulo komanso phindu lake. Zikufanana ndi zimene mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu a mtanda [“mtengo wozunzirapo,” NW] ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.” (1 Akor. 1:18) Ndithudi, tikudziŵa kuti utumiki wachikristu ndiyo ntchito yofunika kwambiri pa ntchito zonse zimene zikuchitika padziko lapansi lerolino.
2 Moyo Wabwino Panopa: Kuyesayesa kwa anthu pofuna kuthetsa mavuto m’dzikoli sikukuthandiza kwenikweni. Malamulo sanaletse kuchuluka kwa umbanda. Mapangano a mtendere ndiponso asilikali osungitsa mtendere sanathetse nkhondo. Ntchito zothandiza anthu zalephera kuthetsa umphaŵi. (Sal. 146:3, 4; Yer. 8:9) Koma uthenga wa Ufumu wasintha miyoyo ya anthu mamiliyoni ambiri mwa kuwathandiza kuvala umunthu watsopano wovomerezeka kwa Mulungu. (Aroma 12:2; Akol. 3:9, 10) Anthuwo akatero, amakhala ndi moyo wabwino panopa kusiyana ndi kale.—1 Tim. 4:8.
3 Tsogolo Labwino: Kuwonjezera pa kutithandiza kuthana ndi mavuto a masiku ano, nzeru ya Mulungu imatithandiza kukonzekera bwino tsogolo lathu. (Sal. 119:105) Imatithandiza kupeŵa kulimbikira zinthu zosaphula kanthu zofuna kusintha zinthu m’dziko lamakonoli. (Mlal. 1:15; Aroma 8:20) Ndife oyamikira kwambiri kuti sitikuwonongera nthaŵi ya moyo wathu pa kufunafuna zinthu zosatheka. M’malo mwake, timalimbikira kuuza anthu za lonjezo lodalirika la Yehova lakuti kudzakhala “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” mmene mudzakhala chilungamo. Tsiku la Yehova lopereka chiweruzo likadzafika, zidzaonekeratu kuti amene anadalira nzeru ya Mulungu anasankha bwino.—2 Pet. 3:10-13; Sal. 37:34.
4 Ngakhale kuti nzeru ya Mulungu ingaoneke ngati yosathandiza kwa anthu amene amakonda “nzeru ya nthaŵi ino ya pansi pano,” kunena zoona ndiyo njira yokha yothandiza yofunika kuitsatira. (1 Akor. 1:21; 2:6-8) Choncho, sitisiya kulengeza padziko lonse lapansi uthenga wochokera kwa Mulungu ‘wanzeru yekhayo.’—Aroma 16:27.