Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/04 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 2/04 tsamba 7

Zilengezo

◼ February: Yandikirani kwa Yehova. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzachite zotheka kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Ngati anthu ali nalo kale buku limeneli, mungagaŵire buku la Samalani Ulosi wa Danieli! April ndi May: Gaŵirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, omwe ena mwa iwo angakhale amene anapezeka pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina zauzimu koma sasonkhana ndi mpingo mokhazikika, yesetsani kugaŵira buku la Lambirani Mulungu. Tidzachite zotheka kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba, makamaka ngati ena anamaliza kale kuphunzira buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa March 1, kapena patangodutsa masiku ochepa kuchoka pa detili. Akatha kuŵerengerako, mukalengeze kumpingo mutamaliza kuŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti. Ŵerengani kalata iliyonse yothokoza zopereka za mpingo zothandiza pa ntchito ya padziko lonse ndiponso zopita ku thumba lililonse la gulu.

◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki apende ntchito ya apainiya okhazikika onse. Ngati pali amene zikuwavuta kukwanitsa maola ofunikawo, akulu ayenera kukonza zowathandiza. Onani mfundo zina m’makalata apachaka a S-201.

◼ Mutu wa nkhani ya onse yapadera ya pa nyengo ya Chikumbutso cha 2004 udzakhala wakuti: “Khalani Wolimba Mtima Ndipo Khulupirirani Yehova.” Onani chilengezo chofanana ndi chimenechi mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2003.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena