Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira February 23, 2004. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya January 3 mpaka February 23, 2004. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziŵani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi tingachite chiyani kuti timveketse phindu la nkhani yomwe tikukamba kwa omvera athu ndiponso kuti iwapindulitse? [be-CN tsa. 158 ndime 2-4]
2. N’chifukwa chiyani tiyenera kusankha mosamala mawu athu? [be-CN tsa. 160 ndime 1 ndi bokosi lachiŵiri]
3. Kodi ndi chinthu chiti chofunika kwambiri pa kalankhulidwe kabwino chopezeka pa 1 Akorinto 14:9, chimene achitchula, nanga mfundo imeneyi tingaigwiritse ntchito motani pophunzitsa? [be-CN tsa. 161 ndime 1-4]
4. Monga mmene mawu olembedwa pa Mateyu 5:3-12 ndi Marko 10:17-21, akusonyezera ndi khalidwe lapadera liti la Yesu pophunzitsa limene tingalitsanzire? [be-CN tsa. 162 ndime 4]
5. Pamene tili mu utumiki kapena tikuyankha pamisonkhano ya mpingo, n’chifukwa chiyani tifunika kumagwiritsa ntchito mawu opereka mphamvu, okhudza mtima, ndi opereka bwino chithunzi? (Mat. 23:37, 38) [be-CN tsa. 163 ndime 3–tsa. 164 ndime 1]
NKHANI NA. 1
6. Kodi mutu wa nkhani n’chiyani, ndipo kodi kuuganizira mosamalitsa kungatithandize bwanji posankha ndi kuyala mfundo za nkhaniyo? [be-CN tsa. 39 ndime 6–tsa. 40 ndime 1]
7. (a) Kodi kumatanthauzanji kukhala waukhondo mwauzimu, nanga n’chifukwa chiyani ukhondo wauzimu uli wofunika kwambiri kuposa ukhondo wina uliwonse? (b) Kodi Akristu angapeŵe bwanji kutsatira makhalidwe oipa omwe afala m’dzikomu? [w02-CN 2/1 mas. 5-6]
8. Kodi mfundo za m’Baibulo zofunika kwambiri ndi ziti? [w02-CN 2/15 tsa. 5 ndime 1, 4, 6]
9. Kodi kumvera ena chisoni n’kutani, nanga Yesu anasonyeza motani khalidwe limeneli? [w02-CN 4/15 tsa. 25 ndime 4-5]
10. Kodi lemba la Miyambo 11:11 limagwira ntchito motani pa mipingo ya anthu a Yehova? [w02-CN 5/15 tsa. 27 ndime 1-3]
KUŴERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi “mtengo wa moyo” wotchulidwa pa Genesis 2:9 unaimira chiyani?
12. Kodi n’chifukwa chiyani mkazi wa Loti anataya moyo wake? (Gen. 19:26) [w90-CN 4/15 tsa. 18 ndime 10]
13. M’zochitika za ulosi za mu Genesis chaputala 24, kodi ndani akuimiridwa ndi (a) Abrahamu, (b) Isake, (c) Wantchito wa Abrahamu Eliezere, (d) ngamila khumi, ndi (e) Rabeka?
14. Kodi Mulungu analinganiziratu Yakobo ndi Esau? (Gen. 25:23)
15. Kodi Rakele anaonetsa chitsanzo chabwino chotani cha khama lomwe linadalitsidwa ndi Yehova? (Gen. 30:1-8) [w02-CN 8/1 mas. 29-30]