Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/04 tsamba 3-4
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 3/04 tsamba 3-4

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Okondedwa Abale ndi Alongo:

“CHISOMO kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.” (1 Akor. 1:3) Timalakalaka kwambiri nthaŵi imene zopuma zonse zidzapatsa Yehova ulemerero umene iye amafunikira. (Sal. 150:6) Poyembekeza tsiku lalikulu limeneli, timalengezabe uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi kupanga ophunzira.

Masiku ano ntchito yolalikira ndi imene ili yofunika kwambiri pantchito za Yehova zapadziko lapansi. (Marko 13:10) Chifukwa chakuti tikudziŵa bwino kuti maganizo a Yehova ali pantchitoyi, timapempha Mulungu kuti atithandize kugwira ntchitoyi, podziŵa kuti munthu aliyense ali ndi mwayi wopindula ndi dipo. (Chiv. 14:6, 7, 14, 15) N’zoona kuti timakumana ndi mavuto, koma timasangalala kwambiri ‘kuvekedwa mphamvu yochokera Kumwamba’ kuti tichite utumiki umenewu.—Luka 24:49.

N’zolimbikitsa kuona chaka chautumiki chapitachi ndi kulingalira zimene Yehova wachita kudzera mwa atumiki ake okhulupirika. Mwa mphamvu ya mzimu woyera, anthu a Mulungu asonyeza chikondi chofanana ndi cha Kristu, agonjetsa udani padziko lonse. Chikondi chimenechi chinaonekera pamisonkhano yathu yachigawo. Kuyambira June mpaka December 2003, nthumwi za m’mayiko oposa 100 zinapita ku misonkhano yamayiko 32 imene inachitika m’madera asanu ndi limodzi amene ndi Africa, Asia, Australia, Ulaya, North America, ndi South America. Amishonale, atumiki a m’mayiko ena, ndi otumikira pa Beteli m’dziko lina anafunsidwa pamisonkhano yachigawo ndi yamayiko imeneyi.

Pamisonkhano imeneyi, tinalandira bulosha la ‘Onani Dziko Lokoma’ ndi buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Komanso, analengeza kuti buku la Sukulu ya Utumiki Waupainiya limene lakonzedwanso liyamba kugwiritsidwa ntchito kumapeto kwa chaka chautumiki cha 2004. M’kupita kwa nthaŵi, amene achita upainiya kwanthaŵi yaitali ndipo analoŵa kale m’sukuluyi adzaloŵanso m’makalasi ndi apainiya atsopano.

Chifukwa cha thandizo la Mulungu ndiponso kuwoloŵa manja kwa anthu kwapangitsa kuti kukhale kotheka kumanga Nyumba za Ufumu zina zambiri, makamaka m’mayiko osauka. Chifukwa chakuti padziko lonse pakufunika chakudya chauzimu chambiri, ntchito zokulitsa nthambi zikuchitika m’mayiko ambiri. Bulosha lakuti Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! tsopano likupezeka m’zinenero 299, ndipo lasindikizidwa makope okwana 139 miliyoni; buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha lasindikizidwa makope oposa 93 miliyoni m’zinenero 161; ndipo makope oposa 200 miliyoni a bulosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? asindikizidwa m’zinenero 267.

Tikuwalandira ndi manja aŵiri anthu 258,845 amene anasonyeza kudzipatulira kwawo mwa ubatizo wa m’madzi m’chaka chautumiki chapitachi! Ngakhale kuti kuchirikiza Ufumu wa Mulungu kwakupangitsani kuti Satana azikudani kwambiri, kwakupangitsaninso kuti Yehova azikudalitsani kwambiri ndi kukutetezani mwauzimu pamene mukuthamanga makani anakuikiraniwo. (Aheb. 12:1, 2; Chiv. 12:17) Inde, khalani otsimikiza kuti ‘Iye amene akusungani sawodzera.’—Sal. 121:3.

Lemba la chaka chino cha 2004 lakuti, ‘Dikirani . . . Khalani okonzekeratu,’ ndi lapanthaŵi yake kwambiri. (Mat. 24:42, 44) Mawu a Mulungu amati Akristu ndi alendo m’dongosolo la zinthu limene likufali. (1 Pet. 2:11; 4:7) Chotero, tifunika kuganizira kwambiri zinthu zauzimu, kukhala ndi moyo wosalira zambiri, ndiponso kupenda mitima yathu mwachifatse. “Chinjoka chachikulu” chimafuna kutilikwira, kutiloŵetsa m’dongosolo lake la zinthu.—Chiv. 12:9.

Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku n’kofunika kwambiri kuti tikhalebe tcheru. Kungatithandize kuti ‘inde wathu akhale inde’ pankhani yokwaniritsa kudzipatulira kwathu ndiponso kuti ‘tigwiritse chiyambi cha kutama kwathu [“chidaliro chathu,” NW] kuchigwira kufikira chitsiriziro.’ (Yak. 5:12; Aheb. 3:14) Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kungatithandize kukumbukira pamene dziko lafika pankhani yosatsatira miyezo ya Mulungu yosasinthika. (Mal. 3:6; 2 Tim. 3:1, 13) Kudziŵa Baibulo kungatithandize kukana “miyambi yachabe” ndi kukhala wokhulupirika kwa Yehova.—2 Pet. 1:16; 3:11.

Makolo, pamene mukulera ana anu m’maleredwe ndi chilangizo cha Yehova, kodi mukuwathandiza kukhala ndi zolinga zauzimu ndiponso kukhala ‘odikira’? (Aef. 6:4) Kodi mukuwaphunzitsa kuona tsogolo lawo monga momwe munthu wanzeru woposa wina aliyense amene anakhalako padziko lapansi anaonera tsogolo lake? Yesu akanatha kukhala kalipentala, wopanga zinthu, kapena dokotala waluso kwambiri kuposa onse amene anakhalako, koma iye anachita utumiki wanthaŵi zonse. Chitsanzo chake chikulimbikitseni kuthandiza ana anu kuika zinthu za Ufumu patsogolo pamoyo wawo.

Bungwe Lolamulira limene likuimira gulu la kapolo wokhulupirika likuthokoza kwambiri “khamu lalikulu” polithandiza kukwaniritsa udindo wawo woti ‘uthenga uwu wabwino wa Ufumu ulalikidwe padziko lonse lapansi, ukhale mboni.’ (Chiv. 7:9; Mat. 24:14, 45) Anthu okondedwa inu khalani otsimikiza kuti Yehova amakumbukira “ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.” (Aheb. 6:10) Pamene mukuŵerenga zokumana nazo zosangalatsa komanso mukamaona zotsatira za ntchito yanu imene munagwira mogwirizana mu Yearbook ya 2004, dziŵani kuti mwachita mbali yofunika kwambiri popereka umboni wapadziko lonse umenewu.

Limbani mtima poyembekeza tsogolo ndipo pitirizani ‘kupenyerera chobwezera cha mphoto,’ musalole munthu wina kapena ziwanda kukulepheretsani kuilandira. (Aheb. 11:26; Akol. 2:18) Inde, dalirani Yehova, tsimikizani kuti adzathandiza onse amene amamukonda kuti apeze moyo wokwanira.—Yoh. 6:48-54.

Dziŵani kuti timasangalala kwambiri kutumikira nanu limodzi potamanda ulemerero wa Yehova.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena