Tingathe Kuchita Zimene Yehova Amafuna
1. Kodi nthaŵi zina timalimbana ndi maganizo otani, nanga chimachititsa zimenezo n’chiyani?
1 Njira yabwino koposa pa moyo wathu masiku ano ndiyo kutsata malamulo ndi mfundo zimene Yehova amapereka, ndipo zimenezi zimatithandiza kuyala maziko abwino a moyo wosatha m’tsogolo. (Sal. 19:7-11; 1 Tim. 6:19) Komabe, dziko la Satana limatidzetsera mavuto ambiri. Thupi lathu lopanda ungwiro limawonjezeranso mavutowo. Pofuna kukwanitsa maudindo athu a m’Malemba, nthaŵi zina tingatope. (Sal. 40:12; 55:1-8) Tingafike mpaka poganiza kuti kodi tingathe kuchita zonse zimene Yehova amafuna kuti tichite? Zinthu zikatere, kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe olimba mwauzimu?
2. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yehova sapitirira malire pa zimene amafuna kuti ife tichite?
2 Malamulo a Yehova Salemetsa: Yehova satipempha kuchita zinthu zimene sitingathe. Malamulo ake sali olemetsa. M’malo mwake, amatithandiza. (Deut. 10:12, 13; 1 Yoh. 5:3) Iye amazindikira kuti ife monga anthu tili ndi zofooka. Ee, “akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Sal. 103:13, 14) Mulungu mwachifundo amalandira zonse zimene timachita mwakhama pom’tumikira, ngakhale ngati n’zochepa chifukwa chakuti moyo wathu sutilola kuchita zambiri. (Lev. 5:7, 11; Marko 14:8) Amatipempha kum’senzetsa nkhaŵa zathu, ndipo amalonjeza kuti atithandiza kukhalabe okhulupirika.—Sal. 55:22; 1 Akor. 10:13.
3. Kodi Yehova amatilimbikitsa motani kuti tipirire?
3 M’pofunika Kupirira: Nkhani za m’Baibulo zokhudza anthu okhulupirika monga Eliya, Yeremiya, ndi Paulo zimasonyeza kuti tifunika kupirira. (Aheb. 10:36) Yehova anawathandiza nthaŵi ya mavuto ndiponso pamene iwo anagwa mphwayi. (1 Maf. 19:14-18; Yer. 20:7-11; 2 Akor. 1:8-11) Ndiponso kukhulupirika kwa abale athu masiku ano kumatilimbikitsa. (1 Pet. 5:9) Tikamasinkhasinkha zitsanzo ngati zimenezi, sitidzagwa mphwayi.
4. N’chifukwa chiyani m’pofunika kukumbukira malonjezo a Mulungu?
4 Chiyembekezo chakuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa chili ngati “nangula wa moyo.” (Aheb. 6:19) Chifukwa cha chiyembekezo chotero, Abrahamu ndi Sara anamvera pamene Yehova anawapempha kuchoka kudziko lawo ndi kukakhala ‘alendo kudziko la lonjezano.’ Mosenso chiyembekezo chinam’patsa mphamvu yoteteza kulambira koona mopanda mantha. Chinam’limbitsa mtima Yesu kuti apirire mtengo wozunzirapo. (Aheb. 11:8-10, 13, 24-26; 12:2, 3) Ngati lonjezo la Mulungu lakuti kudzakhala dziko latsopano lolungama lili lamphamvu m’mitima yathu, lidzatithandiza kusasunthika.—2 Pet. 3:11-13.
5. N’chifukwa chiyani kuganizira za kukhulupirika kwathu kwa m’mbuyomu kungakhale kolimbikitsa?
5 Ngati tiganizira za kukhulupirika kwathu kwa m’mbuyomu, kudzimana kwathu, ndi kulimba mtima kwathu, zingatithandizenso kupeza mphamvu mu utumiki wathu. (Aheb. 10:32-34) Tikamaganizira zimenezo, zimatikumbutsa za chimwemwe chimene timakhala nacho tikamachita zimene Yehova amafuna kwa ife, ndipo zimene amafuna ndizo kudzipereka kwathu kwa moyo wonse.—Mat. 22:37.