Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu September: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. October: Gaŵirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kwa amene aonetsa chidwi, asonyezeni bulosha la Mulungu Amafunanji, ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo. November: Gaŵirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati eninyumba anena kuti alibe ana, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Pogaŵira buloshali khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo. December: Gaŵirani buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati palibe gaŵirani, Buku Langa la Nkhani za Baibulo.
◼ Pulogalamu ya pa vidiyo yakuti No Blood—Medicine Meets the Challenge yatulutsidwa m’Chingelezi pa kaseti ya vidiyo. Ngati mungaifune, muyenera kuitanitsa kudzera ku mpingo.
◼ Nkhani ya onse yapadera ya panyengo ya Chikumbutso cha 2005 idzakambidwa Lamlungu, pa April 10. Tidzalengeza mutu wa nkhaniyi m’tsogolo muno. Mipingo imene idzakhale ndi woyang’anira dera, msonkhano wadera, kapena tsiku la msonkhano wapadera mlungu umenewu, idzakhale ndi nkhani yapaderayi mlungu wotsatizana ndi mlungu umenewu. Mpingo uliwonse usakhale ndi nkhani yapaderayi lisanafike Lamlungu, pa April 10, 2005.
◼ Pamene woyang’anira dera achezera mpingo wanu, adzaonanso mpambo wa Malangizo Okonzera Nyumba ya Ufumu. Ngati pali mbali zina zofunika kukonza, akulu ayenera kuonetsetsa kuti Nyumba ya Ufumuyo yakonzedwanso moyenerera. Ngati woyang’anira dera aona kuti pali zinthu zikuluzikulu zofunika kukonzetsa, nthaŵi yomweyo adzadziŵitsa ofesi ya nthambi.
◼ Tikukumbutsa akulu kutsatira malangizo a mu Nsanja ya Olonda ya April 15,1991 masamba 21 mpaka 23, onena za anthu ochotsedwa kapena odzilekanitsa amene akufunika kuwayendera.
◼ Mipingo ifunika kuti izipereka kwa abale magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akangofika. Zimenezi zidzathandiza kuti ofalitsa athe kuŵerenga ndi kudziŵiratu bwino nkhani zimene zili m’magaziniwo asanapite mu utumiki wa kumunda.
◼ Mwezi wa October udzakhala mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza, chifukwa uli ndi mapeto a mlungu asanu athunthu.