Tiyenera Kulemekeza Ulamuliro wa Yehova
Mukamva za mayina a anthu akale monga Kora, Datani, ndi Abiramu, kodi ndi nkhani yotani imene imabwera m’maganizo mwanu? Kupandukira! Kupandukira chiyani? Ulamuliro wa Mulungu. Nkhani yawo yonse yomvetsa chisoni imapezeka m’chaputala 16 cha Numeri, ndipo zina zimene zili m’nkhaniyo anazifotokoza m’nkhani yakuti “Gonjerani Mokhulupirika Ulamuliro Umene Mulungu Waika” mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2002. Kuŵerenga nkhani imeneyi kudzakuthandizani. Mudzatha kuona mkangano umene unabuka pakati pa ana okhulupirika a Kora ndi tate wawo wopandukayo, amene anali kukangana ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. (Num. 26:9-11) Nkhani ya zochitika zenizeni imeneyi iyenera kutilimbikitsa tonsefe kukhala okhulupirika kwambiri kwa Yehova.
Pamene mukuŵerenga nkhani ya m’chaputala 16 cha Numeri imeneyi, yesani kuona umboni wosonyeza kuti Kora limodzi ndi anzake opandukawo analephera mayeso a kukhulupirika pambali zofunika kwambiri zokwanira zisanu ndi imodzi: (1) Kodi sanalemekeze bwanji ulamuliro wa Mulungu? (2) Kodi zinatheka bwanji kuti iwo alole kudzikuza, mtima wofunitsitsa kutchuka, ndi nsanje kuwalamulira? (3) Kodi anakuza motani zolakwa za anthu amene Yehova anawasankha? (4) Kodi ndi mzimu wodandaula wotani umene anakhala nawo? (5) N’chifukwa chiyani anayamba kukhala ndi mtima wosakhutira ndi maudindo a utumiki amene anali nawo? (6) Kodi analola bwanji mabwenzi ndi banja kukhala zofunika kwambiri kuposa kukhulupirika kwawo kwa Mulungu?
Lingalirani za mmene mfundo zophunziridwa m’seŵero la Baibulo limeneli zikukhudzira mmene ifeyo patokha timaonera ulamuliro wa Mulungu masiku ano: (1) Kodi tiyenera kuchita chiyani ndi zimene akulu mu mpingo agamula, ndipo n’chifukwa chiyani? (2) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisiye maganizo olakwika alionse amene tingakhale nawo? (3) Kodi tiyenera kuchita motani ndi zolakwa zimene anthu oikidwa kutsogolera gulu angakhale nazo? (4) Tingachite chiyani ngati mu mtima mwathu tiyamba kukhala ndi mzimu wodandaula? (5) Kodi tiyenera kuwaona motani maudindo alionse amene tapatsidwa? (6) Pankhani ya kukhulupirika kwathu kwa Mulungu, ndani amene sitiyenera kuwaika patsogolo, ndipo ndi liti pamene zimenezi zingakhale chiyeso chovuta kwambiri kwa ife?
Pambuyo pakuti nkhani imeneyi yakambidwa kumpingo, bwanji osakaŵerenganso kachiŵiri chaputala 16 cha Numeri ndi nkhani yakuti “Gonjerani Mokhulupirika Ulamuliro Umene Mulungu Waika,” mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2002? Lolani kuti ikhomereze kwambiri m’maganizo mwanu zifukwa zimene tiyenera kulemekezera ulamuliro wa Yehova!—Sal. 18:25; 37:28.