Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira October 11
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 20: Khalani ndi Mtima Wokonda Kugaŵira Magazini! Tchulani chiŵerengero cha magazini amene mpingo unagaŵira mwezi watha. Kodi chiŵerengerocho chikufanana motani ndi chiŵerengero cha magazini amene mumalandira kuchokera ku ofesi ya nthambi? Ngati pali kusiyana kwakukulu, ndiye kuti pakufunika kuchita chiyani? Pemphani omvera kupereka ndemanga zawo pa mfundo zotsatirazi: (1) Wofalitsa aliyense ayenera kulembetsa magazini okwanira osati opitirira muyeso. (2) Onani tsiku Loŵeruka lililonse monga Tsiku la Magazini. (3) Pa pulogalamu yanu yoloŵera mu utumiki phatikizanipo zogaŵira magazini mwezi uliwonse. (4) Konzani zochita ulaliki wamwamwayi kaŵirikaŵiri pogwiritsa ntchito magazini kuyambitsira makambirano. (5) Gaŵirani magazini kwa anthu amene mitu ya nkhani zake ikhoza kuwachititsa chidwi mogwirizana ndi ntchito yawo. (6) Sungani chiŵerengero cholondola cha magazini amene mwagaŵira ndiponso pezani anthu oti muziwagaŵira magazini atsopano alionse a mwezi ndi mwezi. (7) Gwiritsani ntchito bwino magazini onse akale kuti pasapezeke ongounjikana. Sonyezani omvera magazini onse aposachedwapa ndi kutchula mitu ya nkhani imene ingawachititse chidwi. Sonyezani chitsanzo cha wachikulire ndi wachinyamata ndipo aliyense wa iwo asonyeze mwachidule mmene tingagaŵire magazini.—Onani mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 1995.
Mph. 15: Kondani Kuthandiza Ena. (Yoh. 4:34) Kufunsa. Zimasangalatsa kuona nkhope ya munthu ili yosangalala pophunzira choonadi cha Mawu a Mulungu. (w94-CN 3/1 tsa. 29 ndime 6 ndi 7) Funsani ofalitsa kapena apainiya aŵiri kapena atatu amene amagwiritsa ntchito Baibulo mogwira mtima mu utumiki ndiponso kuyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo. Kodi amatani kuti akulitse chidwi chimene amapeza? Ndi chimwemwe chotani chimene amapeza pochita zimenezo? Auzeni afotokoze kapena achite chitsanzo cha zokumana nazo zawo za mu utumiki.
Nyimbo Na. 69 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 18
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 40: “Msonkhano Wachigawo Watilimbikitsa Kuyenda ndi Mulungu.” Yokambidwa ndi mkulu. Mutakamba mawu oyamba kwa mphindi imodzi kapena kucheperapo, kambiranani ndi omvera za pulogalamu ya msonkhano wachigawo pogwiritsa ntchito mafunso amene ali m’nkhaniyo. Kuti funso lililonse liyankhidwe mokwanira bwino m’pofunika kuti mugaŵe bwino nthaŵi yanu, mwina kungolola yankho limodzi lokha pa mafunso ena. Mogwirizana ndi nthaŵi imene yaperekedwayo, si malemba onse osagwidwa mawu amene mungaŵerenge, malembawo aikidwa kuti athandize kupeza mayankho mosavuta. Ndemanga zifunika kuti zizikhudza kwambiri phindu la kugwiritsa ntchito zinthu zimene tinaphunzira.
Nyimbo Na. 165 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 25
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu), sonyezani chitsanzo cha mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya November 1 ndi Galamukani! ya November 8. M’chitsanzo chilichonse sonyezani njira zosiyana za mmene tingachitire ndi munthu amene sakufuna kuti tikambirane ponena kuti ‘Sindifuna Mboni za Yehova.’—Onani buku la Kukambitsirana masamba 17 ndi 18. (Ngati magazini ameneŵa asanafike pampingopo, chonde gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 18: Perekani Umboni Kuchirikiza Mawu a Mulungu. Kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki masamba 256 mpaka 257. Kodi tingagwiritse ntchito motani maumboni ena osakhala a m’Baibulo kuthandiza anthu kuzindikira kuti Malemba ali olondola? Pemphani omvera kupereka ndemanga pa mafunso otsatirawa: Kodi ndi zitsanzo ziti kuchokera m’chilengedwe chimene timachionachi zimene tingaloze monga umboni wonena za Mlengi? (rs-CN mas. 74 ndi 75) Kodi tingagwiritse ntchito motani ndemanga za anthu ena ophunzira kapena za akatswiri kuthandizira ena kuona kuti Baibulo lilidi Mawu a Mulungu? (rs-CN mas. 52 mpaka 54) Kodi ndi mafanizo kapena zoyerekeza ziti zimene tingagwiritse ntchito kuthandiza ena kuona chifukwa chimene Mulungu walolera kuipa? (rs-CN tsa. 183) Kodi ndi zochitika kapena zitsanzo zotani zimene mwagwiritsapo ntchito kuthandizira ena kuzindikira phindu lotsatira malangizo a m’Baibulo?
Mph. 15: “Ukwati Wolemekezeka Uli ndi Phindu Lake.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mkulu woyenerera. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Ŵerengani ndi kugogomezera malemba onse ofunika.
Nyimbo Na. 62 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 1
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa onse kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda. M’mwezi wa November tidzagaŵira buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Mwachidule kambiranani mfundo za mmene tingagaŵire bukuli kuchokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2004 tsamba 3, ndi kusonyeza chitsanzo chimodzi cha maulaliki amene ali pamenepo. Ngati pali ulaliki wina umene ungakhale wothandiza kwambiri m’gawo lanu, mungakambirane umenewo ndi kusonyeza chitsanzo chake. Ngati nthaŵi ilipo, pemphani omvera kupereka ndemanga za mmene agwiritsira ntchito bukuli mu utumiki.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: Kupirira pa Ntchito Zabwino. (Agal. 6:10) Funsani anthu aŵiri kapena atatu amene ndi apainiya okhazikika kapena amene amachita upainiya wothandiza nthaŵi ndi nthaŵi. Ndi zovuta zotani zimene akumana nazo potumikira Yehova, ndipo azigonjetsa motani? N’chiyani chimene chawathandiza kupirira pochitira ena zabwino? Kodi iwo ndi ena apindula motani ndi khama lawo mu utumiki wachikristu? Phatikizanipo ndemanga za zimene mwachita kuti mufikire ena amene amalankhula zinenero zina ndi uthenga wabwino ngati zikugwira ntchito kwanuko. Yamikirani onse chifukwa cha ‘ntchito zawo za chikhulupiriro ndi ntchito zawo zachikondi ndi chipiriro chawo.’—1 Ates. 1:2, 3.
Nyimbo Na. 175 ndi pemphero lomaliza.