Ukwati Wolemekezeka Uli ndi Phindu Lake
1. Kodi Yesu anati chiyani pogogomezera kufunika kwa kukonzekera?
1 Kumanga nyumba kumafuna kukonzekera mokwanira bwino. Kuyala maziko kusanayambike, pamafunika kupeza kaye malo ndiponso kukonza pulani yake. Komabe, pali chinthu china chofunika kwambiri. Yesu anati: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?”—Luka 14:28.
2. Ndi mbali iti pamoyo imene imafunika kukonzekera?
2 Zimene zimafunika pomanga nyumba, n’zofanananso ndi zimene zimafunika pokonzekera kumanga ukwati wolemekezeka. Malemba amati tifunika kumvera lamulo la Kaisara. (Aroma 13:1-4) M’mayiko ambiri, boma limafuna kuti okwatirana akhale ndi mtchato wa ukwati wawo kuti ukhale wodziŵika ndi boma. Pachifukwa chimenechi, mwamuna ndi mkazi asanayambe kukhalira limodzi monga banja ayenera kuonetsetsa kuti alembetsa ukwati wawo kuboma.—Marko 12:17.
3. Kodi pangafunike zotani potsata dongosolo lolembetsa mtchato ku boma?
3 Nthaŵi zina, zimenezi zimafuna khama, nthaŵi, ndiponso ndalama kuti papezeke onse amene amafunikira, akuchikazi ndi akuchimuna, kuti atsate dongosolo lonse lovomerezeka lolembetsa mtchato. N’chifukwa chake ndi nzeru ‘kukhala pansi ndi kuŵerengera mtengo wake.’—Luka 14:28.
4. (a) Kodi ndi mfundo ziti za Mulungu zimene zimakhudza okwatirana? (b) Kodi mawu a pa Ahebri 13:4 akuti “pogona” tiyenera kuwamva motani?
4 Atalowa mu ukwati m’njira yolemekezeka, Akristu amatsatira mfundo za Mulungu m’banja lawolo. Amakondana ndi kulemekezana. (Aef. 5:28-30, 33) Kuti akhale ndi chimwemwe chenicheni, ayenera kukhala okhulupirika kwa wina ndi mnzake. Paulo analemba kuti: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse; ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.” (Aheb. 13:4) Mawu akuti “pogona” amatanthauza kugonana kwa mwamuna ndi mkazi okwatirana mwalamulo. Kugonana kwina kulikonse, monga ngati kwa mitala, sikunganenedwe kuti ndi kwa ‘ulemu ndi onse.’—1 Akor. 7:2.
5. Kodi akulu achikristu amakhala ndi udindo wotani ngati wina akufuna kulembetsa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu kapena kukhala wofalitsa wosabatizidwa, ndipo n’chifukwa chiyani?
5 Chifukwa chakuti Mulungu ndi amene anayambitsa ukwati, akulu mu mpingo ayenera kuonetsetsa ngati amene akufuna kulembetsa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, komanso amene akufuna kukhala ofalitsa osabatizidwa, ali ndi mtchato wovomerezeka. Ngati mwamuna ndi mkazi akukhalira limodzi ngati banja, koma alibe mtchato, ndiye kuti akuchita dama, ndipo zimenezi n’zosalemekezeka pamaso pa Mulungu. Baibulo limaletsa kugonana anthu asanakwatirane—1 Akor. 6:18.
6. Kodi ukwati wolemekezeka uli ndi phindu lanji?
6 Kodi phindu la ukwati wolemekezeka n’lotani? Okwatiranawo amakhala ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso pakati pawo. Onse aŵiri amakhala ndi chikumbumtima chabwino. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti amakhala osangalala kudziŵa kuti ukwati wawo umalemekeza Yehova, woyambitsa ukwati.—Aef. 3:14, 15.