Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 25, 2004. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya September 6 mpaka October 25, 2004. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziŵani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi tingachite chiyani kuti mawu athu azimveka olimbikitsa tikamakamba nkhani yokhudza mbali inayake ya ntchito yathu yachikristu? [be-CN tsa. 203 ndime 3-4]
2. Kodi kubwereza komveketsa mfundo n’kutani, ndipo n’chifukwa chiyani kuli kofunika? [be-CN tsa. 206 ndime 1-4]
3. Kodi tingaunike bwanji mutu wa nkhani zathu? [be-CN tsa. 210 ndime 1-5, bokosi]
4. Kodi tingadziŵe bwanji mfundo zofunika mu nkhani imene tapatsidwa kuti tikambe? [be-CN tsa. 212 ndime 1-4]
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kuti tisachulukitse mfundo zazikulu? [be-CN tsa. 213 ndime 3-5]
NKHANI NA. 1
6. Kodi panali zinthu zotani Chigumula chisanachitike zimene zingakhale kuti zinapangitsa kukhala kovuta kwa anthu kukhulupirira kuti zinthu zonse zimene anali kuziona zidzatha? [w02-CN 3/1 mas. 5-6]
7. Kodi n’chifukwa chiyani n’zochititsa chidwi kuona kuti anthu a mu nthaŵi ya Yesu anamutchula kuti “Mphunzitsi” osati “Wochiritsa”? (Luka 3:12; 7:40) [w02-CN 5/1 tsa. 4 ndime 3; tsa. 6 ndime 5]
8. Kodi lemba la Miyambo 11:24, 25 limasonyeza bwanji phindu lochita zonse zomwe tingathe mu utumiki wa kumunda? [w02-CN 7/15 tsa. 30 ndime 3-5]
9. Kodi ndi nkhani yokhudza ulamuliro yotani imene inayamba ndi kupanduka kwa mu Edene, ndipo zotsatirapo za kupanduka kumeneko zakhala zotani? (Gen. 3:1-6) [w02-CN 10/1 tsa. 6 ndime 1, 3-4]
10. Kuti tipeze chimwemwe chenicheni, n’chifukwa chiyani kuchiritsa kwauzimu kuyenera kuchitika kaye kuchiritsa kwenikweni kusanachitike? [w02-CN 5/1 tsa. 6 mpaka 7; w02 8/15 tsa. 29]
KUŴERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Popeza Yehova anauza Balamu kupita ndi amuna a Balaki, n’chifukwa chiyani anakwiya Balamu atapita nawo? (Num. 22:20-22)
12. Kodi mwamuna wa mkazi wachikristu angafafanize zowinda za mkaziyo? (Num. 30:6-8)
13. Kodi ‘midzi yopulumukirako’ imaimira chiyani masiku ano? (Num. 35:6) [w95-CN 11/15 tsa. 17 ndime 8]
14. Kodi lamulo limene lili pa Deuteronomo 6:6-9 loti ‘azimanga lamulo la Mulungu padzanja ndipo likhale ngati chapamphumi pakati pa maso’ tiyenera kulimva kuti limanena za dzanja ndi mphumi yeniyeni?
15. Kodi mawu akuti “zovala zanu sizinatha pathupi panu” akungotanthauza kuti zovala za Aisrayeli zikatha amawapatsa zina? (Deut. 8:4)