Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu October: Gaŵirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mwezi wonse. Malangizo owonjezereka adzaperekedwabe m’tsogolo muno kuonetsetsa kuti magazini onse amene timalandira akugwiritsidwa ntchito. Kwa amene aonetsa chidwi, asonyezeni bulosha la Mulungu Amafunanji, ndipo mudzabwerereko ndi cholinga chokayambitsa maphunziro a Baibulo. November: Gaŵirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati eninyumba anena kuti alibe ana, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Pogaŵira buloshali khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo. December: Gaŵirani buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati palibe gaŵirani mabuku ena, kuphatikizapo Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. January: Gaŵirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
◼ Mphatika imene ili mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno ndi “Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2005.” Isungeni kuti mudzaigwiritse ntchito chaka chonse cha 2005.
◼ Mipingo iyambe kuitanitsa Lemba la Chaka la 2005 pamodzi ndi oda yawo ya October. (Chonde itanitsani za chinenero cha m’dera lanu). Mipingo iyenera kuitanitsa Lemba la Chaka limodzi lokha m’chinenero chilichonse. N’kofunika kuti mipingo idzaike Lemba la Chaka latsopano limeneli pa January 1, 2005.
◼ Ma DVD Atsopano Amene Alipo:
Transfusion Alternatives—Documentary Series (dvalt). DVD imodzi imeneyi ili ndi mapulogalamu atatu a pavidiyo, Transfusion-Alternative Strategies—Simple, Safe, Effective (vcae), Transfusion-Alternative Health Care-Meeting Patient Needs and Rights (vcnr), ndi No Blood—Medicine Meets the Challenge (vcnb).—Chingelezi
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako (dvgt-ASL) —Chinenero Chamanja cha ku America
◼ Ma CD Atsopano Amene Alipo.
Yandikirani kwa Yehova (cdcl) —Chingelezi