Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2005
Malangizo
Dongosolo lotsatirali ndilo lidzagwiritsidwe ntchito pochititsa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu mu 2005.
MABUKU OPHUNZIRA: Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu [bi53-CN], Nsanja ya Olonda [w-CN], Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu [be-CN], Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako [gt-CN], ndi Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN].
Sukulu iyenera kuyamba PANTHAŴI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje, ndiyeno n’kupitiriza motere:
LUSO LA KULANKHULA: Mphindi 5. Woyang’anira sukulu, mlangizi wothandiza, kapena mkulu wina woyenerera adzafotokoza luso la kulankhula kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki. (Mipingo imene ili ndi akulu ochepa ingagwiritse ntchito mtumiki wotumikira woyenerera.) Fotokozaninso zimene zili m’mabokosi amene ali m’nkhani imene yaperekedwayo ngati sitinanene kuti musafotokoze. Musaphatikizepo mbali ya zochita. Mbali imeneyi kwenikweni ndi yoti munthu aziigwiritsa ntchito payekha ndiponso popereka malangizo am’seri.
NKHANI NA. 1: Mphindi 10. Mkulu woyenerera kapena mtumiki wotumikira woyenerera ndi amene ayenera kukamba nkhani imeneyi, ndipo izitengedwa mu Nsanja ya Olonda, m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kapena m’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Imeneyi ndi nkhani yolangiza imene ayenera kuikamba kwa mphindi khumi popanda mafunso obwereza. Cholinga chake chisakhale kufotokoza chisawawa mfundo za m’nkhaniyo koma kusonyeza phindu la mfundozo, ndi kutsindika mfundo zomwe zingathandize kwambiri mpingowo. Agwiritse ntchito mutu wosonyezedwa. Abale amene apatsidwa nkhani imeneyi azionetsetsa kuti akusunga nthaŵi. Malangizo am’seri angaperekedwe ngati pakufunika kutero.
MFUNDO ZAZIKULU ZA KUŴERENGA BAIBULO: Mphindi 10. Kwa mphindi sikisi zoyambirira, mkulu kapena mtumiki wotumikira woyenerera afotokoze mmene machaputala ofunika kuŵerenga mlunguwo angathandizire mpingowo. Angafotokoze mbali ina iliyonse ya chigawo cha kuŵerenga Baibulo cha mlunguwo. Isakhale chidule chabe cha gawo loŵerenga mlunguwo. Cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvera kuzindikira chifukwa chake komanso mmene mfundozo zilili zaphindu. Wokamba nkhaniyo ayenera kuonetsetsa kuti asapitirire mphindi zisanu ndi imodzi zoperekedwa pa mbali yoyambirira imeneyi. Aonetsetse kuti wagwiritsa ntchito mphindi zinayi zomalizira kuti omvera alankhulepo. Apemphe omvera kulankhulapo mwachidule (kwa masekondi 30 kapena kucheperapo) pa mfundo za m’Baibulo zimene zinawasangalatsa poŵerenga ndiponso phindu lake. Ndiyeno woyang’anira sukulu apemphe ophunzira amene ali m’makalasi ena kupita ku makalasi awo.
NKHANI NA. 2: Mphindi 4. Iyi ndi nkhani yoti mbale aŵerenge. Nthaŵi zambiri aziŵerenga m’Baibulo. Koma kamodzi pamwezi, wopatsidwa nkhaniyi adzaŵerenga nkhani ya mu Nsanja ya Olonda. Wophunzira aŵerenge nkhani imene wapatsidwa popanda kukamba mawu oyamba kapena omaliza. Kutalika kwa nkhani yoŵerenga kuzisiyana pang’ono mlungu uliwonse koma ayenera kuŵerenga m’mphindi zinayi kapena kucheperapo. Woyang’anira sukulu aziona nkhaniyo asanagaŵire munthu, kuti pogaŵa aigwirizanitse ndi misinkhu ndiponso luso la ophunzira. Woyang’anira sukulu makamaka adzaonetsetsa kuti akuthandiza wophunzira kuŵerenga mosonyeza kuti akumvetsa zimene akuŵerengazo, kuŵerenga mosadodoma, kutsindika ganizo moyenera, kusinthasintha mawu, kupuma moyenera, ndiponso kuŵerenga mwachibadwa.
NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhani imeneyi azikamba ndi mlongo. Wophunzira amene wapatsidwa nkhani imeneyi angasankhe yekha kapena azipatsidwa mtundu wa makambirano kuchokera pa mndandanda umene uli patsamba 82 m’buku la Sukulu ya Utumiki. Wophunzira agwiritse ntchito mutu wa nkhani umene wapatsidwa ndipo agwirizanitse ndi mbali ya utumiki wakumunda yomwe ndi yotheka ndiponso yothandiza m’gawo la mpingowo. Ngati sitinasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhani imeneyo mwa kufufuza m’zofalitsa za gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Ophunzira atsopano azipatsidwa nkhani zimene tasonyeza buku limene nkhaniyo yachokera. Woyang’anira sukulu adzaonetsetsa makamaka mmene wophunzira akufotokozera nkhaniyo ndiponso mmene akuthandizira mwininyumba kulingalira pa Malemba ndi kumvetsa mfundo zazikulu za nkhaniyo. Ophunzira amene angapatsidwe nkhani imeneyi ayenera kukhala odziŵa kuŵerenga. Woyang’anira sukulu adzasankha wothandiza mmodzi.
NKHANI NA. 4: Mphindi 5. Wophunzira akambe nkhani pa mutu umene wapatsidwa. Ngati sitinasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhaniyo mwa kufufuza m’zofalitsa za gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Akapatsidwa mbale, aziikamba monga nkhani yokambira omvera amene asonkhana m’Nyumba ya Ufumuyo. Mlongo akapatsidwa nkhani imeneyi, nthaŵi zonse aziikamba mofanana ndi Nkhani Na. 3. Woyang’anira sukulu angapereke nkhani Na. 4 kwa mbale nthaŵi ina iliyonse imene akuona kuti m’poyenera kupatsa mbale. Dziŵani kuti nkhani zimene zili ndi nyenyezi ziyenera kuperekedwa kwa abale basi kuti akambe ngati nkhani.
KUSUNGA NTHAŴI: Nkhani iliyonse isadye nthaŵi. Chimodzimodzinso ndi ndemanga za mlangizi. Nkhani Na. 2 mpaka Na. 4 ziziimitsidwa mwaluso nthaŵi yake ikatha. Ngati abale amene akamba nkhani yotsegulira ya luso la kulankhula, Nkhani Na. 1, kapena mfundo zazikulu za kuŵerenga Baibulo adya nthaŵi, azilangizidwa m’seri. Aliyense ayenera kusamala kwambiri nthaŵi. Pulogalamu yonse izitenga mphindi 45, osaphatikizapo nthaŵi ya nyimbo ndi pemphero.
MALANGIZO: Mphindi 1. Wophunzira aliyense akamaliza nkhani yake, woyang’anira sukulu adzanena mfundo zolimbikitsa za mbali ya nkhaniyo zimene wophunzirayo wachita bwino. Asapitirire mphindi imodzi pofotokoza zimenezi. Cholinga chake sindicho kungonena kuti “mwachita bwino” koma kutchula zifukwa zenizeni zimene zachititsa kuti mbali za nkhaniyo zikhale zogwira mtima. Malinga ndi zimene wophunzira aliyense akufunikira, malangizo ena othandiza angaperekedwe m’seri misonkhano itatha kapena panthaŵi ina.
MLANGIZI WOTHANDIZA: Bungwe la akulu lingasankhe mkulu waluso, ngati alipo, kuphatikiza pa woyang’anira sukulu, kuti akhale mlangizi wothandiza. Ngati pali akulu angapo pa mpingo, ndiye kuti chaka chilichonse mkulu wina woyenerera angasamalire udindo umenewu. Ntchito yake idzakhala yopereka malangizo am’seri, ngati angafunike, kwa abale amene akamba Nkhani Na. 1 ndi mfundo zazikulu za Baibulo. N’kosafunika kuti azipereka malangizo kwa mkulu mnzake aliyense kapena mtumiki wotumikira aliyense akakamba nkhani zimenezi. Dongosolo limeneli lipitiriza kugwira ntchito mu 2005 ndipo mwina lingasinthidwe m’tsogolo.
FOMU YOLANGIZIRA: Ili m’buku momwemo.
KUBWEREZA KWA PAKAMWA: Mphindi 30. M’miyezi iŵiri iliyonse, woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza kwa pakamwa. Kudzatsatira pambuyo pa kukambirana luso la kulankhula ndi mfundo zazikulu za kuŵerenga Baibulo monga mmene tafotokozera kale. Kubwereza kwa pakamwaku kudzakhala kwa nkhani zimene zinakambidwa m’sukulu m’miyezi iŵiri yapita, kuphatikizapo mlungu wa kubwerezaku. Ngati mpingo wanu udzakhala ndi msonkhano wadera kapena ngati woyang’anira dera adzachezera mpingo wanu mlungu umene muyenera kukhala ndi kubwereza kwa pakamwa, tsatirani malangizo opezeka patsamba 6 mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa December 2003 osonyeza zimene muyenera kuchita.
NDANDANDA
Jan. 3 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 16-20 Nyimbo 6
Luso la Kulankhula: Lankhulani Zomveka Bwino kwa Ena (be-CN tsa. 226 ndime 1–tsa. 227 ndime 2)
Na. 1: Opani Mulungu Woona (be-CN tsa. 272 ndime 1–tsa. 273 ndime 1)
Na. 2: Yoswa 16:1–17:4
Na. 3: Chifukwa Chake Kungoŵerenga Baibulo Sikokwanira (rs-CN tsa. 89 ndime 1-2)
Na. 4: Kodi Kukhala Wolemera Kapena Kukhala Wosauka Masiku Ano ndi Chizindikiro Chosonyeza Kuti Munthu ndi Woopadi Mulungu?
Jan. 10 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 21-24 Nyimbo 100
Luso la Kulankhula: Kufotokoza Mawu Achilendo (be-CN tsa. 227 ndime 3–tsa. 228 ndime 1)
Na. 1: Kudziŵitsa Dzina la Mulungu (be-CN tsa. 273 ndime 2–tsa. 274 ndime 1)
Na. 2: Yoswa 23:1-13
Na. 3: Chipembedzo Choona Ziphunzitso Zake N’zozikidwa pa Baibulo Ndipo Chimazindikiritsa Dzina la Mulungu (rs-CN tsa. 89 ndime 3-4)
Na. 4: Kodi Kulambira Yesu N’koyenera?
Jan. 17 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 1-4 Nyimbo 97
Luso la Kulankhula: Kupereka Mafotokozedwe Ofunikira (be-CN tsa. 228 ndime 2-3)
Na. 1: Kum’dziŵa Mulungu wa Dzinalo (be-CN tsa. 274 ndime 2-5)
Na. 2: Oweruza 2:1-10
Na. 3: Chipembedzo Choona Chimasonyeza Chikhulupiriro Choona mwa Yesu Kristu (rs-CN tsa. 89 ndime 5)
Na. 4: Kodi Mungadziteteze Bwanji ku Mavidiyo a Nyimbo Zoipa?
Jan. 24 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 5-7 Nyimbo 47
Luso la Kulankhula: Zimadaliranso Mtima wa Munthu (be-CN tsa. 228 ndime 4-6)
Na. 1: Dzina la Mulungu Ndilo “Linga Lolimba” (be-CN tsa. 274 ndime 6–tsa. 275 pakamutu)
Na. 2: Oweruza 6:25-35
Na. 3: Kodi Baibulo Liyenera Kukhudza Bwanji Ufulu Wathu Wosankha?
Na. 4: Chipembedzo Choona Sichili Chamwambo Koma Ndi Njira ya Moyo (rs-CN tsa. 90 ndime 1)
Jan. 31 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 8-10 Nyimbo 174
Luso la Kulankhula: Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvera (be-CN tsa. 230 ndime 1-6)
Na. 1: Kuchitira Umboni za Yesu (be-CN tsa. 275 pakamutu–tsa. 276 ndime 1)
Na. 2: w03-CN 1/15 mas. 19-20 ndime 16-18
Na. 3: Ziŵalo za Chipembedzo Choona Zimakondana Ndipo N’cholekana ndi Dziko (rs-CN tsa. 90 ndime 2-3)
Na. 4: Kukondetsa Chuma Kumatanthauza Zambiri Osati Kungokhala ndi Katundu Wambiri
Feb. 7 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 11-14 Nyimbo 209
Luso la Kulankhula: Kukonza Nkhani Yophunzitsadi mwa Kufufuza (be-CN tsa. 231 ndime 1-3)
Na. 1: Kugogomezera Mbali ya Yesu Monga Momboli (be-CN tsa. 276 ndime 2-3)
Na. 2: Oweruza 12:1-15
Na. 3: Zimene Zimachititsa Kuti Mboni za Yehova Zikhale Zogwirizana
Na. 4: Ziŵalo za Chipembedzo Choona ndi Mboni Zokangalika za Ufumu wa Mulungu (rs-CN tsa. 90 ndime 4)
Feb. 14 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 15-18 Nyimbo 105
Luso la Kulankhula: Kufotokoza Malemba (be-CN tsa. 231 ndime 4-5)
Na. 1: Kugogomezera Mbali ya Yesu Monga Mkulu wa Ansembe ndi Mutu wa Mpingo (be-CN tsa. 277 ndime 1-2)
Na. 2: Oweruza 15:9-20
Na. 3: aNgati Wina Anena Kuti, ‘Malinga Ngati Mukhulupirira Yesu, Zilibe Kanthu Kwenikweni Tchalitchi Chomwe Muli’ (rs-CN tsa. 93 ndime 2)
Na. 4: Chifukwa Chomwe Akristu Sachita Nawo Zogodomalitsa Maganizo (g03-CN 7/8 mas. 14-15)
Feb. 21 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 19-21 Nyimbo 53
Luso la Kulankhula: Kufotokoza Tanthauzo la Mawu (be-CN tsa.232 ndime 1)
Na. 1: Kugogomezera Mbali ya Yesu Monga Mfumu Yolamulira (be-CN tsa. 277 ndime 3-4)
Na. 2: w03-CN 2/1 mas. 17-18 ndime 18-21
Na. 3: bNgati Wina Anena Kuti, ‘Kodi N’chiyani Chomwe Chimakupangitsani Kuganiza Kuti Pali Chipembedzo Chimodzi Chokha Cholungama?’ (rs-CN tsa. 93 ndime 3)
Na. 4: Kodi Zina mwa “Zakuya za Mulungu” N’chiyani? (1 Akor. 2:10)
Feb. 28 Kuŵerenga Baibulo: Rute 1-4 Nyimbo 120
Luso la Kulankhula: Kufotokoza Malemba (be-CN tsa. 232 ndime 2-4)
Kubwereza kwa Pakamwa
Mar. 7 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 1-4 Nyimbo 221
Luso la Kulankhula: Kusankha Mfundo Zimene Zidzapindulitsa Omvera Anu (be-CN tsa. 233 ndime 1-5)
Na. 1: Kumanga Pamaziko a Kristu (be-CN tsa. 278 ndime 1-4)
Na. 2: 1 Samueli 2:1-11
Na. 3: Yesu Sanapite Kumwamba M’thupi Lanyama (rs-CN tsa. 107 ndime 2–tsa. 108 ndime 2)
Na. 4: Chifukwa Chimene Akristu Enieni Satsatira Zonena za Openda Nyenyezi
Mar. 14 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 5-9 Nyimbo 151
Luso la Kulankhula: Kukamba Mfundo za M’nkhani Imene Mwapatsidwa (be-CN tsa. 234 ndime 1–tsa. 235 ndime 3)
Na. 1: Uthenga Uwu Wabwino wa Ufumu (be-CN tsa. 279 ndime 1-4)
Na. 2: 1 Samueli 5:1-12
Na. 3: Chifukwa Chimene Yesu Ankavalira Matupi Anyama (rs-CN tsa. 108 ndime 3–tsa. 109 ndime 2)
Na. 4: Mmene Tingalimbitsire Ubwenzi Wathu ndi Yehova
Mar. 21 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 10-13 Nyimbo 166
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Mafunso Mwaluso (be-CN tsa. 236 ndime 1-5)
Na. 1: Kufotokoza Kuti Ufumu N’chiyani (be-CN tsa. 280 ndime 1-5)
Na. 2: 1 Samueli 10:1-12
Na. 3: Kodi Akristu Ayenera Kuchita Bwanji Zinthu ndi Okondedwa Awo Achipembedzo China?
Na. 4: Anthu Oukitsidwa Kuti Akalamulire ndi Kristu Adzakhala Ngati Iyeyo (rs-CN tsa. 109 ndime 4-8)
Mar. 28 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 14-15 Nyimbo 172
Luso la Kulankhula: Mafunso Oyambira Mfundo Zofunika Kwambiri (be-CN tsa. 237 ndime 1-2)
Na. 1: Kufotokoza Mmene Ufumu Umatikhudzira (be-CN tsa. 281 ndime 1-4)
Na. 2: w03-CN 3/15 mas. 19-20 ndime 17-21
Na. 3: Chifukwa Chimene Akristu Amakhomera Misonkho
Na. 4: Chimene Chiukiriro Chidzatanthauza kwa Anthu Onse (rs-CN tsa. 110 ndime 1–tsa. 111 ndime 2)
Apr. 4 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 16-18 Nyimbo 27
Luso la Kulankhula: Mafunso Othandiza Kuganizapo pa Nkhaniyo (be-CN tsa. 237 ndime 3–tsa. 238 ndime 2)
Na. 1: Chifukwa Chake Maphunziro Ali Ofunika kwa Akristu (w03-CN 3/15 tsa. 10 ndime 1–tsa. 11 ndime 5)
Na. 2: 1 Samueli 17:41-51
Na. 3: Chifukwa Chimene Anthu Oukitsidwa Sadzalangidwira Ntchito Zawo Zakale (rs-CN tsa. 111 ndime 4)
Na. 4: Kusinkhasinkha za Zotsatirapo za Zochita Zathu Kungatithandize Kukonda Chabwino ndi Kudana ndi Choipa
Apr. 11 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 19-22 Nyimbo 73
Luso la Kulankhula: Mafunso Olimbikitsa Munthu Kulankhula za Kukhosi (be-CN tsa. 238 ndime 3-5)
Na. 1: Mmene Achinyamata Angapitire Patsogolo Mwauzimu (w03-CN 4/1 mas. 8-10)
Na. 2: 1 Samueli 20:24-34
Na. 3: Chifukwa Chimene Khalidwe la Kudzichepetsa Kwenikweni Lilili Lokopa
Na. 4: Mmene “Otsala a Akufa” Adzabwererenso Kumoyo Padziko Lapansi (rs-CN tsa. 112 ndime 1-4)
Apr. 18 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 23-25 Nyimbo 61
Luso la Kulankhula: Mafunso Othandiza Kutsindika Mfundo (be-CN tsa. 239 ndime 1-2)
Na. 1: Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wanu Wonse (w03-CN 11/1 mas. 4-7)
Na. 2: w03-CN 5/1 tsa. 17 ndime 11-14
Na. 3: Amene Adzaphatikizidwa M’chiukiriro Chapadziko Lapansi (rs-CN tsa. 113 ndime 1-5)
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Panali Pangano la Abrahamu?
Apr. 25 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 26-31 Nyimbo 217
Luso la Kulankhula: Mafunso Amavumbulanso Malingaliro Olakwika (be-CN tsa. 239 ndime 3-5)
Kubwereza kwa Pakamwa
May 2 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 1-3 Nyimbo 91
Luso la Kulankhula: Mawu Oyerekeza Zinthu ndi Ofananitsa Zinthu Ophunzitsadi (be-CN tsa. 240 ndime 1–tsa. 241 ndime 1)
Na. 1: Cholinga cha Maphunziro Sikungopeza Ntchito Kokha (w03-CN 3/15 tsa. 11 ndime 6–tsa. 14 ndime 6)
Na. 2: 2 Samueli 2:1-11
Na. 3: Zochitika Zogwirizanitsidwa ndi Kukhalapo kwa Kristu Zimachitika M’kati mwa Nyengo ya Zaka Zambiri (rs-CN tsa. 162 ndime 1-2)
Na. 4: Phindu Losiyanasiyana la Kukhala Woona Mtima
May 9 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 4-8 Nyimbo 183
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Zitsanzo (be-CN tsa. 241 ndime 2-4)
Na. 1: Yehova Amaganiziradi Achinyamata (w03-CN 4/15 tsa. 29 ndime 3–tsa. 31 ndime 4)
Na. 2: 2 Samueli 5:1-12
Na. 3: Kodi Pangano la Chilamulo Linagwira Ntchito Yanji?
Na. 4: Kubweranso kwa Kristu Kudzakhala Kosaoneka (rs-CN tsa. 162 ndime 3–tsa. 163 ndime 1)
May 16 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 9-12 Nyimbo 66
Luso la Kulankhula: Zitsanzo za m’Malemba (be-CN tsa. 242 ndime 1-2)
Na. 1: Kodi Yehova Amaona Zimene Inu Mumachita? (w03-CN 5/1 mas. 28-31)
Na. 2: 2 Samueli 9:1-13
Na. 3: Mmene Kubwerera kwa Yesu Kudzakhalire ndi Mmene Diso Lililonse Lidzamuonere (rs-CN tsa. 163 ndime 3–tsa. 164 ndime 4)
Na. 4: Kodi Mawu a Mulungu Ndi Amoyo M’njira Zotani? (Aheb. 4:12)
May 23 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 13-15 Nyimbo 103
Luso la Kulankhula: Kodi Fanizolo Adzalimva? (be-CN tsa. 242 ndime 3–tsa. 243 ndime 1)
Na. 1: Kodi Nkhani ya Nowa Ili ndi Tanthauzo kwa Ife? (w03-CN 5/15 mas. 4-7)
Na. 2: 2 Samueli 13:10-22
Na. 3: Kodi Lemba la Yohane 11:25, 26 Limatanthauza Chiyani?
Na. 4: Zochitika Zimene Zimagwirizanitsidwa ndi Kukhalapo kwa Kristu (rs-CN tsa. 165 ndime 1-5)
May 30 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 16-18 Nyimbo 132
Luso la Kulankhula: Mafanizo a Zinthu Zodziŵika Bwino (be-CN tsa. 244 ndime 1-2)
Na. 1: Ganizani Bwino Kuti Muchite Zinthu Mwanzeru (w03-CN 7/15 mas. 21-23)
Na. 2: w03-CN 5/15 mas. 16-17 ndime 8-11
Na. 3: Akristu Safunika Kusunga Sabata (rs-CN tsa. 346 ndime 2-3)
Na. 4: Chifukwa Chake Kudzichepetsa Sikutanthauza Kufooka
June 6 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 19-21 Nyimbo 224
Luso la Kulankhula: Mafanizo Oyenerera Omvera Anu (be-CN tsa. 244 ndime 3–tsa. 245 ndime 4)
Na. 1: Kumvetsa Cholinga cha Kulanga (w03-CN 10/1 tsa. 20 ndime 1–tsa. 22 ndime 1)
Na. 2: 2 Samueli 19:1-10
Na. 3: Kodi Mkristu Angaloŵe Bwanji mu Mpumulo wa Mulungu?
Na. 4: M’Baibulo Palibe Pamene Panalembedwa Kuti Adamu Ankasunga Sabata (rs-CN tsa. 346 ndime 4–tsa. 347 ndime 2)
June 13 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 22-24 Nyimbo 74
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zooneka Pophunzitsa (be-CN tsa. 247 ndime 1-2)
Na. 1: Khalani Ophunzitsika Ndipo Samalani ndi Lilime Lanu (w03-CN 9/15 tsa. 21 ndime 1–tsa. 22 ndime 3)
Na. 2: 2 Samueli 24:10-17
Na. 3: Yesu Sanagaŵe Chilamulo cha Mose Kukhala ndi Mbali ya “Madzoma” ndi ya “Makhalidwe Abwino” (rs-CN tsa. 347 ndime 3–tsa. 348 ndime 1)
Na. 4: Kodi Mkristu Ayenera Kukhala Wolekana ndi Dziko M’njira Zotani?
June 20 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 1-2 Nyimbo 2
Luso la Kulankhula: Mmene Yesu Anaphunzitsira ndi Zinthu Zooneka (be-CN tsa. 247 ndime 3)
Na. 1: Kuphunzira Chinsinsi Chokwanitsidwa ndi Zimene Tili Nazo (w03-CN 6/1 mas. 8-11)
Na. 2: w03-CN 6/1 mas. 12-13 ndime 1-4
Na. 3: Kodi N’chiyani Chimene Chinali Chapadera ndi Lamulo Lakhumi?
Na. 4: Malamulo Khumi Anathera Limodzi ndi Chilamulo cha Mose (rs-CN tsa. 348 ndime 2-3)
June 27 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 3-6 Nyimbo 167
Luso la Kulankhula: Mmene Tingaphunzitsire ndi Zinthu Zooneka (be-CN tsa. 248 ndime 1-3)
Kubwereza kwa Pakamwa
July 4 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 7-8 Nyimbo 194
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Mapu, Mapulogalamu Osindikizidwa a Misonkhano Yaikulu, ndi Mavidiyo (be-CN tsa. 249 ndime 1-2)
Na. 1: Okhulupirira Achikulire Muziwaona Kuti ndi Ofunika Kwambiri (w03-CN 9/1 mas. 30-31)
Na. 2: 1 Mafumu 8:1-13
Na. 3: Kodi Yesu Analigonjetsa Bwanji Dziko Lapansi?
Na. 4: Chifukwa Chimene Malamulo Onse Amakhalidwe Abwino Sanachotsedwe Pamene Malamulo Khumi Anachotsedwa (rs-CN tsa. 349 ndime 1-2)
July 11 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 9-11 Nyimbo 191
Luso la Kulankhula: Kuphunzitsa Gulu la Anthu ndi Zinthu Zooneka (be-CN tsa. 249 ndime 3–tsa. 250 ndime 1)
Na. 1: Umboni Woti Yesu Kristu Anakhalako Padziko Lapansi (w03-CN 6/15 mas. 4-7)
Na. 2: 1 Mafumu 9:1-9
Na. 3: Zimene Sabata Limatanthauza kwa Akristu (rs-CN tsa. 349 ndime 3–tsa. 351 ndime 1)
Na. 4: Munthu Angasiye Kugwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo mwa Kutsatira Mfundo za M’Baibulo
July 18 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 12-14 Nyimbo 162
Luso la Kulankhula: Chifukwa Chake Kulankhula M’njira Yokambirana Kuli Kofunika (be-CN tsa. 251 ndime 1-3)
Na. 1: Maganizo Amabala Ntchito Ndipo Ntchito Zimakhala ndi Zotsatira Zake (w03-CN 1/15 tsa. 30 ndime 1-3)
Na. 2: 1 Mafumu 12:1-11
Na. 3: Mmene Chikhulupiriro Chingatithandizire Kulimbana ndi Ziyeso
Na. 4: Amene Baibulo Limawatcha Oyera Mtima (rs-CN tsa. 331 ndime 1–tsa. 332 ndime 1)
July 25 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 15-17 Nyimbo 158
Luso la Kulankhula: Poyambira Pake (be-CN tsa. 251 ndime 4–tsa. 252 ndime 3)
Na. 1: M’mene ‘Tingadziŵire Kuti Chifuno cha Yehova N’chiyani’ (w03-CN 12/1 tsa. 21 ndime 3–tsa. 23 ndime 3)
Na. 2: w03-CN 7/15 tsa. 19 ndime 15-17
Na. 3: Chifukwa Chimene Sitipempherera kwa “Oyera Mtima” (rs-CN tsa. 332 ndime 2-4)
Na. 4: Kodi Mzimu Woyera Umatonthoza Bwanji Akristu?
Aug. 1 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 18-20 Nyimbo 207
Luso la Kulankhula: Pamene Muyenera Kulolera (be-CN tsa. 252 ndime 4–tsa. 253 ndime 1)
Na. 1: Achinyamata, Yendani Moyenera Yehova (w03-CN 10/15 tsa. 23 ndime 1–tsa. 24 ndime 1)
Na. 2: 1 Mafumu 18:1-15
Na. 3: Akristu Onse Angabale Zipatso Zochuluka
Na. 4: Zoona Zake za Kulambira Zinthu Zakale ndi Zifanizo za “Oyera Mtima” (rs-CN tsa. 333 ndime 1–tsa. 334 ndime 2)
Aug. 8 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 21-22 Nyimbo 92
Luso la Kulankhula: Kupereka Mafunso ndi Kupereka Zifukwa (be-CN tsa. 253 ndime 2–tsa. 254 ndime 2)
Na. 1: Njira Yothetseratu Umphaŵi (w03-CN 8/1 mas. 4-7)
Na. 2: 1 Mafumu 21:15-26
Na. 3: Akristu Oyera Mtima Enieni Si Opanda Machimo (rs-CN tsa. 334 ndime 3)
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Olimba Mtima, Ndipo Tingakhale Bwanji Otero?
Aug. 15 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 1-4 Nyimbo 16
Luso la Kulankhula: Zifukwa Zomveka Zochokeradi m’Mawu a Mulungu (be-CN tsa. 255 ndime 1–tsa. 256 ndime 2)
Na. 1: Munalandira Kwaulere, Patsani Kwaulere (w03-CN 8/1 mas. 20-22)
Na. 2: 2 Mafumu 3:1-12
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Chigumula Chisanachitike Anthu Ankakhala ndi Moyo Nthaŵi Yaitali Kwambiri?
Na. 4: Zoti Anthu Onse Adzapulumuka Si za M’Malemba (rs-CN tsa. 94 ndime 2)
Aug. 22 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 5-8 Nyimbo 193
Luso la Kulankhula: Kambani Mfundo Zimene Maumboni Enanso Amavomereza (be-CN tsa. 256 ndime 3-5)
Na. 1: Dziŵani Mmene Mungachitire Zinthu Moganizira Ena (w03-CN 8/1 mas. 29-31)
Na. 2: w03-CN 8/1 tsa. 19 ndime 18-22
Na. 3: Kodi Anthu Onse Potsirizira Pake Adzapulumutsidwa? (rs-CN tsa. 95 ndime 1)
Na. 4: Kodi ndi Makhalidwe Abwino Ati a Yona Amene Tiyenera Kutsanzira?
Aug. 29 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 9-11 Nyimbo 129
Luso la Kulankhula: Kupereka Umboni Wokwanira (be-CN tsa. 257 ndime 1-4)
Kubwereza kwa Pakamwa
Sept. 5 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 12-15 Nyimbo 175
Luso la Kulankhula: Yesetsani Kuwafika Pamtima Anthu (be-CN tsa. 258 ndime 1-5)
Na. 1: Kodi Mukufuna Yehova Mwakhama? (w03-CN 8/15 mas. 25-28)
Na. 2: 2 Mafumu 12:1-12
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuyesetsa Kukhala Ofatsa?
Na. 4: ‘Anthu a Mitundu Yonse’ Adzapulumuka (rs-CN tsa. 95 ndime 2)
Sept. 12 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 16-18 Nyimbo 203
Luso la Kulankhula: Kuchititsa Anthu Kulankhula Zakukhosi Kwawo (be-CN tsa. 259 ndime 1-3)
Na. 1: Kodi Anthu Anakumbukira Zotani za Yesu? (w03-CN 8/15 tsa. 6 ndime 6–tsa. 8 ndime 6)
Na. 2: 2 Mafumu 16:10-20
Na. 3: Baibulo Limati Ena Sadzapulumutsidwa Konse (rs-CN tsa. 95 ndime 3–tsa. 96 ndime 2)
Na. 4: Kodi Tingadziŵe Bwanji Kuti Chokondweretsa Ambuye N’chiyani?
Sept. 19 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 19-22 Nyimbo 89
Luso la Kulankhula: Limbikitsani Maganizo Opindulitsa (be-CN tsa. 259 ndime 4–tsa. 260 ndime 1)
Na. 1: “Gwira Chitsanzo cha Mawu a Moyo” (w03-CN 1/1 tsa. 29 ndime 3–tsa. 30 ndime 4)
Na. 2: 2 Mafumu 19:20-28
Na. 3: Munthu Akapulumutsidwa Sizitanthauza Kuti Wapulumutsidwa Nthaŵi Yonse (rs-CN tsa. 96 ndime 3-6)
Na. 4: Kodi Tingaphunzire Chiyani Kuchokera kwa Abale Athu Achikristu a ku Smurna Wakale?
Sept. 26 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 23-25 Nyimbo 84
Luso la Kulankhula: Kulimbikitsa Ena Kuopa Mulungu (be-CN tsa. 260 ndime 2-3)
Na. 1: Kodi Mkate Wakumwamba ndi Mphatso Yochoka kwa Ndani? (gt-CN mutu 54)
Na. 2: w03-CN 8/15 tsa. 20 ndime 6-10
Na. 3: Timakhulupirira Kuti M’tsogolo Muno Zinthu Zidzakhala Bwino
Na. 4: Chifukwa Chake Chikhulupiriro Chiyenera Kukhala ndi Ntchito (rs-CN tsa. 97 ndime 1-4)
Oct. 3 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 1-4 Nyimbo 51
Luso la Kulankhula: Khalidwe Lathu N’lofunika Kwambiri kwa Yehova (be-CN tsa. 260 ndime 4-5)
Na. 1: Chifukwa Chimene Ambiri Akusiyira Kutsatira Yesu (gt-CN mutu 55)
Na. 2: 1 Mbiri 4:24-43
Na. 3: Mmene Timadziŵira Kuti Kulidi Mdyerekezi (rs-CN tsa. 352 ndime 1–tsa. 353 ndime 1)
Na. 4: Yehova Amatikonda Aliyense Payekha
Oct. 10 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 5-7 Nyimbo 195
Luso la Kulankhula: Thandizani Ena Kudzifufuza (be-CN tsa. 261 ndime 1-3)
Na. 1: Kodi Chimaipitsa Munthu N’chiyani? (gt-CN mutu 56)
Na. 2: 1 Mbiri 5:18-26
Na. 3: Zimene Tikudziŵa za “Tsiku la Yehova”
Na. 4: Satana Sali Lingaliro Loipa Chabe Lokhala M’kati mwa Anthu (rs-CN tsa. 353 ndime 2-4)
Oct. 17 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 8-11Nyimbo 201
Luso la Kulankhula: Kulimbikitsa Ena Kumvera ndi Mtima Wonse (be-CN tsa. 261 ndime 4–tsa. 262 ndime 1)
Na. 1: Chifundo Chimene Yesu Anali Nacho kwa Anthu Okanthidwa (gt-CN mutu 57)
Na. 2: 1 Mbiri 10:1-14
Na. 3: Mulungu Sanalenge Mdyerekezi (rs-CN tsa. 354 ndime 1)
Na. 4: Kodi Ndani Amene Tifunika Kuchita Nawo Zinthu Mosamala Kwambiri?
Oct. 24 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 12-15 Nyimbo 80
Luso la Kulankhula: Kuchita Zinthu Mogwirizana ndi Yehova Pofika Anthu Pamtima (be-CN tsa. 262 ndime 2-3)
Na. 1: Yesu Akonza Mfundo Imene Anthu Sanaimve Bwino (gt-CN mutu 58)
Na. 2: w03-CN 11/1 mas. 10-11 ndime 10-13
Na. 3: Zimene Kuyenda M’dzina la Yehova Kumatanthauzadi
Na. 4: Kodi N’chifukwa Ninji Mulungu Sanawononge Satana Mwamsanga Atangopanduka? (rs-CN tsa. 354 ndime 2–tsa. 355 ndime 1)
Oct. 31 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 16-20 Nyimbo 129
Luso la Kulankhula: Kusunga Nthaŵi (be-CN tsa. 263 ndime 1–tsa. 264 ndime 4)
Kubwereza kwa Pakamwa
Nov. 7 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 21-25 Nyimbo 215
Luso la Kulankhula: Kulimbikitsa Ena Mogwira Mtima Kuti Achitepo Kanthu (be-CN tsa. 265 ndime 1–tsa. 266 ndime 1)
Na. 1: Kodi Yesu Kwenikweni Ndani? (gt-CN mutu 59)
Na. 2: 1 Mbiri 22:1-10
Na. 3: Musaderere Mphamvu ya Mdyerekezi (rs-CN tsa. 355 ndime 2–tsa. 356 ndime 1)
Na. 4: cMmene Ukwati Ungalimbitsidwire
Nov. 14 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 26-29 Nyimbo 35
Luso la Kulankhula: Kulimbikitsa Ena Mwachikondi (be-CN tsa. 266 ndime 2-5)
Na. 1: Kuoneratu Ulemerero wa Ufumu wa Kristu (gt-CN mutu 60)
Na. 2: 1 Mbiri 29:1-9
Na. 3: Chifukwa Chimene Atumiki a Yehova Amazunzidwira
Na. 4: Kupeza Mpumulo ku Chisonkhezero Choipa cha Satana Kuli Pafupi (rs-CN tsa. 356 ndime 3–tsa. 357 ndime 2)
Nov. 21 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 1-5 Nyimbo 46
Luso la Kulankhula: Kulimbikitsa Kochokera M’Malemba (be-CN tsa. 267 ndime 1-2)
Na. 1: Mphamvu ya Chikhulupiriro (gt-CN mutu 61)
Na. 2: 2 Mbiri 2:1-10
Na. 3: Zindikirani Cholinga cha Chilango
Na. 4: dKodi Maunansi Onse a Kugonana Ndi Tchimo? (rs-CN tsa. 179 ndime 1–tsa. 180 ndime 3)
Nov. 28 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 6-9 Nyimbo 106
Luso la Kulankhula: Kukhala ndi “Ufulu wa Kulankhula” (be-CN tsa. 267 ndime 3-4)
Na. 1: Phunziro la Kudzichepetsa (gt-CN mutu 62)
Na. 2: w03-CN 12/1 mas. 15-16 ndime 3-6
Na. 3: Mmene Timasonyezera Kuti Timakondwera mwa Yehova
Na. 4: eZimene Baibulo Limanena za Kugonana kwa Aziŵalo Zofanana (rs-CN tsa. 180 ndime 5–tsa. 181 ndime 2)
Dec. 5 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 10-14 Nyimbo 116
Luso la Kulankhula: Chifukwa Chake Ndi Bwino Kukhala Wolimbikitsa (be-CN tsa. 268 ndime 1-3)
Na. 1: Peŵani Kukhumudwitsa Ena (gt-CN mutu 63)
Na. 2: 2 Mbiri 12:1-12
Na. 3: Chifukwa Chake Timafunikira Chisomo cha Mulungu
Na. 4: Zimene Anthu Ayenera Kusintha Kuti Asangalatse Mulungu (rs-CN tsa. 181 ndime 3–tsa. 182 ndime 1)
Dec. 12 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 15-19 Nyimbo 182
Luso la Kulankhula: Kuwakumbutsa Zimene Yehova Wachita (be-CN tsa. 268 ndime 4–tsa. 269 ndime 2)
Na. 1: Phunziro la Kukhululukira (gt-CN mutu 64)
Na. 2: 2 Mbiri 19:1-11
Na. 3: Chifukwa Chimene Zinaliri Zotheka Kuti Munthu Wangwiro Athe Kuchimwa (rs-CN tsa. 358 ndime 1-4)
Na. 4: Zimene Tingaphunzire ku Banja la Yesu
Dec. 19 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 20-24 Nyimbo 186
Luso la Kulankhula: Kusonyeza Mmene Yehova Wathandizira Anthu Ake (be-CN tsa. 269 ndime 3-5)
Na. 1: Ulendo Wakachetechete wa ku Yerusalemu (gt-CN mutu 65)
Na. 2: w03-CN 12/15 mas. 16-17 ndime 13-15
Na. 3: Phindu Lophunzira Chinsinsi Chokhutitsidwa ndi Zimene Tili Nazo
Na. 4: Chifukwa Chimene Tiyenera Kuzindikira Kuti Tchimo N’loopsa (rs-CN tsa. 359 ndime 2–tsa. 360 ndime 2)
Dec. 26 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 25-28 Nyimbo 137
Luso la Kulankhula: Kusonyeza Kuti Mukusangalala ndi Zimene Mulungu Akuchita Tsopano (be-CN tsa. 270 ndime 1–tsa. 271 ndime 1)
Kubwereza kwa Pakamwa
[Mawu a M’munsi]
a Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
b Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
c Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
d Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
e Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.